Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 62:5-12

Peza mpumulo mwa Mulungu yekhayo iwe moyo wanga;
    chiyembekezo changa chichokera mwa Iye.
Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa;
    Iyeyo ndi linga langa; sindidzagwedezeka.
Chipulumutso changa ndi ulemu wanga zimachokera kwa Mulungu:
    Iye ndiye thanthwe langa lamphamvu; Mulungu ndiye pothawira panga.
Dalirani Iye nthawi zonse, inu anthu;
    khuthulani mitima yanu kwa Iye,
    pakuti Mulungu ndiye pothawirapo pathu.
            Sela

Anthu wamba ndi mpweya chabe;
    anthu apamwamba ndi bodza chabe;
ngati atayezedwa pa sikelo iwo ndi chabe;
    iwowo pamodzi ndi mpweya ndi chabe
10 Musadalire kulanda mwachinyengo
    kapena katundu wobedwa;
ngakhale chuma chanu chichuluke,
    musayike mtima wanu pa icho.

11 Mulungu wayankhula kamodzi,
    ine ndamvapo zinthu ziwiri;
choyamba nʼchakuti Inu Mulungu ndinu wamphamvu,
12     komanso Inu Ambuye, chikondi chanu nʼchosasinthika.
Chachiwiri nʼchakuti mumamuchitira munthu
    molingana ndi ntchito zake.

Yeremiya 20:14-18

14 Litembereredwe tsiku limene ndinabadwa!
    Tsiku limene amayi anga anandibereka lisatamandidwe!
15 Wotembereredwa munthu amene anapita kukasangalatsa abambo anga
    ndi uthenga woti:
    “Kwabadwa mwana wamwamuna!”
16 Munthu ameneyo akhale ngati mizinda imene
    Yehova anayiwononga mopanda chisoni.
Amve mfuwu mmawa,
    phokoso la nkhondo masana.
17 Chifukwa sanandiphere mʼmimba,
    kuti amayi anga asanduke manda anga,
    mimba yawo ikhale yayikulu mpaka kalekale.
18 Kodi ndinabadwira mavuto ndi chisoni
    kuti moyo wanga
    ukhale wamanyazi wokhawokha?

Luka 10:13-16

13 “Ndiwe watsoka, iwe Korazini! Ndiwe watsoka, iwe Betisaida! Kukanakhala kuti zodabwitsa zimene zinachitika mwa inu zinachitika ku Turo ndi Sidoni, iwo akanatembenuka mtima kale lomwe, atavala ziguduli ndi kudzola phulusa. 14 Koma adzachita chifundo polanga Turo ndi Sidoni kusiyana ndi inu. 15 Kodi iwe Kaperenawo, adzakukweza mpaka kumwamba? Ayi, adzakutsitsa mpaka ku Malo a anthu akufa.

16 “Womvera inu, akumvera Ine; wokana inu, akukana Ine. Ndipo wokana Ine; akukana Iye amene anandituma Ine.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.