M’Cheyne Bible Reading Plan
Mliri wa Dzombe
10 Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Pita kwa Farao, pakuti Ine ndawumitsa mtima wake ndi mitima ya nduna zake kuti ndichite zizindikiro zozizwitsa pakati pawo 2 kuti inu mudzawuze ana ndi zidzukulu zanu za mmene ndinawakhawulitsira Aigupto ndi zizindikiro zozizwitsa zimene ndinachita pakati pawo ndiponso kuti inu mudziwe kuti ine ndine Yehova.”
3 Ndipo Mose ndi Aaroni anapita kwa Farao ndi kukanena kuti, “Yehova Mulungu wa Ahebri, akuti: ‘Kodi udzakanabe kudzichepetsa pamaso panga mpaka liti? Alole anthu anga apite kuti akandipembedze. 4 Ngati ukana kuwalola, ndigwetsa dzombe mʼdziko lako lino mawa. 5 Dzombeli lidzakuta nthaka yonse moti sidzaoneka konse. Lidzadya kalikonse kakangʼono kamene sikanawonongedwe ndi matalala aja, kuphatikizapo mitengo yonse imene ikumera mʼminda yanu. 6 Dzombeli lidzadzaza nyumba zako ndi za nduna zako ndiponso za Aigupto onse, chinthu chimene ngakhale makolo anu kapena makolo awo sanachionepo kuyambira tsiku limene anakhala mʼdzikoli mpaka lero.’ ” Ndipo Mose ndi Aaroni anatembenuka ndi kumusiya Farao.
7 Nduna za Farao zinamufunsa kuti, “Kodi munthu uyu adzativutitsa mpaka liti? Aloleni anthuwa apite, kuti akapembedze Yehova Mulungu wawo. Kodi simukuona kuti dziko la Igupto lawonongeka?”
8 Choncho Mose ndi Aaroni anayitanidwanso kwa Farao ndipo anati, “Pitani kapembedzeni Yehova Mulungu wanu. Koma ndani amene adzapite?”
9 Mose anayankha kuti, “Ife tidzapita tonse pamodzi; angʼonoangʼono ndi akuluakulu, ana athu aamuna ndi aakazi, ndiponso ziweto zathu ndi ngʼombe chifukwa tikakhala ndi chikondwerero cha kwa Yehova.”
10 Farao anati, “Yehova akhale ndi inu ngati ndingakuloleni kupita pamodzi ndi akazi ndi ana anu! Zikuoneka kuti mwakonzeka kuchita choyipa. 11 Ndakana! Amuna okha ndiwo apite ndi kukapembedza Yehova pakuti izi ndi zimene mwakhala mukupempha.” Kenaka Mose ndi Aaroni anathamangitsidwa pamaso pa Farao.
12 Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Tambalitsa dzanja lako pa dziko la Igupto kuti dzombe lidze pa dziko la Igupto ndi kuwononga chilichonse chimene chikumera mʼminda ndi chilichonse chimene chinatsala pa nthawi ya matalala.”
13 Kotero Mose anakweza ndodo yake pa dziko la Igupto, ndipo Yehova anawutsa mphepo ya kummawa imene inawomba pa dziko usana ndi usiku wonse. Mmene kumacha nʼkuti mphepoyo itabweretsa dzombe. 14 Dzombelo linafika pa dziko lonse la Igupto ndi kukhala dera lililonse la dzikolo. Dzombe lambiri ngati limenelo silinakhaleponso nʼkale lonse ndipo silidzakhalapo ngakhale mʼtsogolo. 15 Dzombelo linaphimba nthaka yonse mpaka kuoneka kuti bii. Linadya zonse zimene zinatsala nthawi ya matalala, zomera za mʼmunda ndi zipatso. Panalibe chobiriwira chilichonse chimene chinatsala pa mtengo kapena pa chomera chilichonse mʼdziko lonse la Igupto.
16 Mwamsangamsanga, Farao anayitanitsa Mose ndi Aaroni ndipo anati, “Ine ndachimwira Yehova Mulungu wanu ndiponso inu. 17 Tsopano ndikhululukirenso tchimo langa kano konkha ndipo pempherani kwa Yehova Mulungu wanu kuti andichotsere mliri wosakazawu.”
18 Mose anachoka kwa Farao nakapemphera kwa Yehova. 19 Ndipo Yehova anasintha mphepo ija kuti ikhale ya mphamvu yochokera ku madzulo, ndipo inanyamula dzombe lija nʼkulikankhira mʼNyanja Yofiira. Panalibe dzombe ndi limodzi lomwe limene linatsala mu Igupto. 20 Koma Yehova anawumitsa mtima wa Farao, ndipo sanalole kuti Aisraeli apite.
Mliri wa Mdima
21 Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Tambasulira dzanja lako kumwamba kuti kukhale mdima umene udzaphimba dziko lonse la Igupto, mdima wandiweyani.” 22 Choncho Mose anakweza dzanja lake kumwamba ndipo mdima wandiweyani unaphimba dziko lonse la Igupto kwa masiku atatu. 23 Palibe amene anatha kuona mnzake kapena kuchoka pa khomo pake kwa masiku atatu. Koma kumalo kumene kumakhala Aisraeli kunali kowala.
24 Kenaka Farao anayitanitsa Mose ndi Aaroni nati, “Pitani kapembedzeni Yehova. Ngakhale akazi ndi ana anu apite pamodzi ndi inu. Koma musatenge ziweto zanu ndi ngʼombe zanu.”
25 Koma Mose anati, “Ndiye inu mutipatse nsembe zopsereza zoti tikapereke kwa Yehova Mulungu wathu. 26 Koma ayi, ife tipita ndi ziweto zathu. Palibe chiweto chilichonse chimene chitatsale kuno, popeza tikasankha komweko ziweto zokapembedzera Yehova. Sitingadziwe zimene tikagwiritse ntchito popembedza Yehova mpaka titakafika kumeneko.”
27 Koma Yehova anawumitsa mtima wa Farao ndipo sanafune kuwalola kuti apite. 28 Farao anati kwa Mose, “Choka pamaso panga! Uwonetsetse kuti usadzaonekerenso pamaso panga! Tsiku limene ndidzakuonenso udzafa.”
29 Mose anayankha kuti, “Monga momwe mwaneneramu, Ine sindidzaonekeranso pamaso panu.”
Za Kutembenuka Mtima
13 Nthawi yomweyo panali ena amene analipo omwe amamuwuza Yesu za Agalileya amene magazi awo Pilato anawasakaniza ndi nsembe zawo. 2 Yesu anayankha kuti, “Kodi mukuganiza kuti Agalileya amenewa anali ochimwa kwambiri kuposa Agalileya ena onse chifukwa anavutika mʼnjira iyi? 3 Ine ndikuti, ayi! Koma ngati inu simutembenuka mtima, inunso mudzawonongeka nonse. 4 Kapena anthu 18 aja amene anafa nsanja ya Siloamu itawagwera, kodi mukuganiza kuti iwo aja anali ochimwa kwambiri kuposa onse amene amakhala mu Yerusalemu? 5 Ine ndikuti, ayi! Koma ngati inu simutembenuka mtima, inunso mudzawonongeka nonse.”
6 Kenaka Iye anawawuza fanizo kuti, “Munthu wina anali ndi mtengo wamkuyu, umene anadzala mʼmunda wamphesa, ndipo Iye anapita kukayangʼana zipatso, koma sanazipeze. 7 Tsono kwa munthu amene amasamalira munda wamphesawo anati, ‘Kwa zaka zitatu tsopano ndakhala ndikubwera kudzafuna chipatso pa mtengo uwu ndipo sindinachipeze. Udule! Nʼchifukwa chiyani ukuwononga nthaka?’
8 “Munthuyo anayankha kuti, ‘Bwana, tawusiyani kwa chaka chimodzi chokha ndipo ine ndikumba ngalande mozungulira ndi kuthira manyowa. 9 Ngati udzabale zipatso chaka chamawa, zili bwino! Koma ngati sudzabala, pamenepo mudzawudule.’ ”
Mayi Wokhota Msana Achiritsidwa pa Sabata
10 Pa Sabata Yesu ankaphunzitsa mʼsunagoge ina, 11 ndipo momwemo munali mayi amene anali ndi mzimu woyipa umene unamudwalitsa zaka 18. Iye anali wokhota msana ndipo samatha kuweramuka ndi pangʼono pomwe. 12 Yesu atamuona anamuyitana kutsogolo ndipo anati kwa iye, “Amayi, mwamasulidwa ku mavuto.” 13 Kenaka anasanjika manja ake pa iye, ndipo nthawi yomweyo anawongoka nayamika Mulungu.
14 Chifukwa cha kuyipidwa kuti Yesu anachiritsa pa Sabata, wolamulira sunagoge anati kwa anthu, “Pali masiku asanu ndi limodzi ogwira ntchito. Choncho bwerani kuti mudzachiritsidwe masiku amenewo osati pa Sabata.”
15 Ambuye anamuyankha kuti, “Iwe wachiphamaso! Kodi nonsenu simumasula pa Sabata ngʼombe zanu kapena bulu kumuchotsa mʼkhola ndi kupita naye kukamupatsa madzi? 16 Nanga mayiyu, amene ndi mwana wa Abrahamu, ndipo anamangidwa ndi Satana zaka 18, kodi siwoyenera kuti amasulidwe msinga imeneyi pa tsiku la Sabata?”
17 Atanena izi, onse omutsutsa anachititsidwa manyazi, koma anthu anakondwera ndi zodabwitsa zonse zimene Iye anazichita.
Fanizo la Mbewu ya Mpiru ndi la Yisiti
18 Kenaka Yesu anafunsa kuti, “Kodi ufumu wa Mulungu uli ngati chiyani? Kodi Ine ndingawufanizire ndi chiyani? 19 Uli ngati mbewu ya mpiru, imene munthu anatenga ndi kudzala mʼmunda mwake. Inakula, nʼkukhala mtengo, ndipo mbalame zamlengalenga zinakhala mʼnthambi zake.”
20 Iye anafunsanso kuti, “Kodi ufumu wa Mulungu ndingawufanizire ndi chiyani? 21 Uli ngati yisiti amene mayi anatenga ndi kusakaniza ndi ufa wambiri mpaka anafufumitsa ufawo.”
Khomo Lopapatiza
22 Ndipo Yesu anayendayenda mʼmizinda ndi mʼmidzi, kumaphunzitsa pamene Iye ankapita ku Yerusalemu. 23 Wina anamufunsa Iye kuti, “Ambuye, kodi ndi anthu ochepa okha amene adzapulumutsidwe?”
Iye anawawuza kuti, 24 “Yesetsani kulowa pa khomo lopapatiza, chifukwa ndikukuwuzani kuti ambiri adzafuna kulowa koma sadzatha kutero. 25 Nthawi yomwe mwini nyumba adzayimirira ndi kutseka chitseko, inu mudzayima kunja kugogoda ndi kudandaula kuti, ‘Bwana, tatitsekulirani khomo.’
“Koma Iye adzayankha kuti, ‘Ine sindikukudziwani ndipo sindikudziwanso kumene mwachokera.’
26 “Ndipo inu mudzati, tinkadya ndi kumwa ndi inu ndipo munkaphunzitsa mʼmisewu yathu.
27 “Koma Iye adzayankha kuti, ‘Ine sindikukudziwani ndipo sindikudziwanso kumene mwachokera. Chokereni inu nonse ochita zoyipa!’
28 “Mudzalira ndi kukuta mano mukadzaona Abrahamu, Isake ndi Yakobo ndi aneneri onse ali mu ufumu wa Mulungu koma inuyo mutaponyedwa kunja. 29 Anthu adzachokera kummawa ndi kumadzulo, kumpoto ndi kummwera, kudzakhala pa phwando mu ufumu wa Mulungu. 30 Ndithudi otsirizira ndiye adzakhale oyambirira, ndipo oyambirira ndiye adzakhale otsirizira.”
Yesu Amvera Chisoni Yerusalemu
31 Pa nthawi imeneyo Afarisi anabwera kwa Yesu ndipo anati kwa Iye, “Chokani malo ano ndipo pitani kumalo ena aliwonse. Herode akufuna kukuphani.”
32 Iye anayankha kuti, “Pitani kawuzeni nkhandweyo, Ine ndikutulutsa ziwanda ndi kuchiritsa anthu lero ndi mawa ndipo tsiku lachitatu ndidzakwaniritsa cholinga changa.” 33 Mʼnjira ina iliyonse, Ine ndiyenera kupitirira ulendo wanga lero, mawa ndi mkuja. Zoona nʼzakuti mneneri sangafere kunja kwa Yerusalemu.
34 Iwe Yerusalemu, Yerusalemu! Umapha aneneri ndi kuwagenda miyala anthu amene atumizidwa kwa iwe. Nthawi zambiri ndakhala ndikufuna kusonkhanitsa ana ako pamodzi, monga nkhuku imasonkhanitsira anapiye pansi pa mapiko ake, koma iwe sunafune! 35 Taona, nyumba yako yasanduka bwinja. Ine ndikukuwuza kuti, sudzandionanso mpaka pamene udzati, “Wodala amene akubwera mʼdzina la Ambuye!”
28 Pali mgodi wa siliva
ndiponso malo oyengerapo golide.
2 Chitsulo amachikumba pansi,
ndipo mkuwa amawusungunula ku miyala yamkuwa.
3 Munthu amalowa mu mdima atatenga nyale,
amafunafuna miyala mpaka ku malire a mgodiwo,
kufuna mkuwa mu mdima wandiweyani.
4 Amakumba njira zapansi mu mgodimo, kutali ndi kumene kumakhala anthu,
kumalo kumene phazi la munthu silinapondeko;
iye amakhala ali lende pansipo namazungulira uku ndi uku.
5 Nthaka, imene imatulutsa zakudya,
kunsi kwake kumachita ngati kwasandulizika ndi moto;
6 miyala ya safiro imachokera mʼmatanthwe ake,
ndipo mʼfumbi lake mumakhala miyala yagolide.
7 Palibe mbalame yodya zinzake imene imadziwa njira yobisikayi,
palibe kamtema amene anayiona.
8 Zirombo zolusa sizipondamo mʼnjiramo,
ndipo mkango sudzeranso mʼmenemo.
9 Munthu amaphwanya matanthwe olimba,
ndipo amagubuduza mapiri kuyambira mʼtsinde.
10 Amabowola njira mʼmatanthwewo;
ndipo amaona chuma chonse cha mʼphirimo.
11 Amaletsa mitsinje ya pansipo kuti isayendenso,
motero amatulutsira poyera zinthu zobisika.
12 “Koma nzeru zingapezeke kuti?
Kodi kumvetsa zinthu kumakhala kuti?
13 Munthu sadziwa kufunika kwake kwa nzeruzo;
nzeruyo sipezeka pa dziko lino la anthu amoyo.
14 Phompho likuti, ‘Sizipezeka mwa ine muno.’
Nyanja ikuti, ‘Mwa ine munonso ayi.’
15 Nzeru sungazigule ndi golide wabwino kwambiri,
mtengo wake sungawuyerekeze ndi siliva wambiri.
16 Nzeru singagulidwe ndi golide wa ku Ofiri,
kapena ndi miyala ya onikisi kapena ya safiro.
17 Nzeru sungayiyerekeze ndi golide kapena mwala wa galasi,
sungayigule ndi zokometsera zagolide.
18 Miyala ya korali ndi krisitali siyoyeneranso ndi kuyitchula nʼkomwe;
mtengo wa nzeru ndi woposa miyala ya rubi.
19 Nzeru sungayiyerekeze ndi miyala ya topazi ya ku Kusi;
nzeru singagulidwe ndi golide wabwino kwambiri.
20 “Kodi tsono nzeru zimachokera kuti?
Kodi kumvetsa zinthu kumakhala kuti?
21 Malo ake ndi obisika kwa zamoyo zonse,
ndi obisika ngakhale kwa mbalame zamlengalenga.
22 Chiwonongeko ndi imfa zikuti,
‘Tangomva mphekesera chabe ya zimenezo!’
23 Mulungu yekha ndiye amadziwa njira yake yopita kumeneko,
ndipo Iye yekha amadziwa kumene nzeru imakhala,
24 pakuti Iye amayangʼana mpaka ku malekezero a dziko lapansi
ndipo amaona zonse za kunsi kwa thambo.
25 Iye atapatsa mphepo mphamvu zake,
nayeza kuzama kwa nyanja,
26 atakhazikitsa lamulo loti mvula izigwa
ndi kukonza njira ya chingʼaningʼani cha bingu,
27 pamenepo ndi pamene anayangʼana nzeruzo naziyeza mtengo wake;
nazikhazikitsa ndi kuzisanthula bwino lomwe.
28 Ndipo Iye anati kwa munthu,
‘Taonani, kuopa Ambuye, ndiye nzeru zimenezo
ndipo kuthawa zoyipa ndiye kumvetsa zinthu kumeneko.’ ”
Mphatso ya Uneneri ndi ya Malilime
14 Funafunani chikondi, ndikufunitsitsa mphatso zauzimu, makamaka mphatso ya uneneri. 2 Pakuti aliyense amene amayankhula malilime sayankhula kwa anthu, koma kwa Mulungu. Zoonadi, palibe amene amamva zimene akunena chifukwa Mzimu ndiye amamuyankhulitsa zachinsinsi. 3 Koma amene amanenera amayankhula kwa anthu kuti awapatse mphamvu, awalimbikitse ndi kuwakhazikitsa mtima pansi. 4 Iye amene amayankhula malilime amadzilimbikitsa yekha, koma amene amanenera amalimbikitsa mpingo. 5 Nʼkanakonda kuti aliyense mwa inu atamayankhula malilime, koma ndi bwino kuti muzinenera. Amene amanenera amaposa amene amayankhula malilime, pokhapokha atatanthauzira kuti mpingo upindule.
6 Tsono, abale, mudzapindula chiyani nditabwera kwa inu ndi kukuyankhulani mʼmalilime? Koma mudzapindula ngati nditakubweretserani vumbulutso lina lake, kapena chidziwitso, kapena chiphunzitso. 7 Ngakhale mu zinthu zopanda moyo monga chitoliro kapena gitala, zimene zimatulutsa liwu; kodi munthu akhoza kudziwa bwanji nyimbo imene ikuyimbidwa ngati mawu sakumveka mogwirizana bwino? 8 Komanso ngati lipenga silimveka bwino, ndani angakonzekere nkhondo? 9 Chimodzimodzinso inu. Ngati simungayankhule mawu omveka bwino mʼchiyankhulo chanu, wina angadziwe bwanji chimene mukunena? Muzingodziyankhulira nokha. 10 Mosakayika, pali ziyankhulo zosiyanasiyana pa dziko lapansi, koma palibe nʼchimodzi chomwe chimene chilibe tanthauzo. 11 Tsono ngati sindingatolepo tanthauzo la zimene wina akuyankhula, ndiye kuti ndine mlendo kwa oyankhulayo ndipo iyeyo ndi mlendo kwa ine. 12 Chimodzimodzinso inu. Popeza mumafunitsitsa mphatso za Mzimu, yesetseni kuchita bwino pa mphatso zimene zimamanga mpingo.
13 Pa chifukwa ichi munthu amene amayankhula malilime apemphere kuti azitha kutanthauzira zimene akunena. 14 Popeza ngati ndipemphera mʼmalilime, ndi mzimu wanga umene ukupemphera, koma nzeru zanga sizikupindula kanthu. 15 Tsono pamenepa nʼkutani? Ndidzapemphera ndi mzimu wanga, komanso ndidzapemphera ndi nzeru zanga. Ndidzayimba ndi mzimu wanga, komanso ndidzayimba ndi nzeru zanga. 16 Ngati mutamanda Mulungu mu mzimu, kodi munthu amene wapezeka pakati pa amene akuyankhula zomwe sakumva, adzavomereza bwanji kuti “Ameni” pa pemphero lanu loyamikalo popeza sakumva chimene mukunena? 17 Mukhoza kumathokoza mokwanira, koma munthu winayo sanathandizikepo.
18 Ndikuyamika Mulungu chifukwa ndimayankhula malilime kuposa nonsenu. 19 Koma mu mpingo ndi kwabwino kuti ndiyankhule mawu asanu okha omveka bwino kuti ndilangize bwino ena kusiyana ndikuyankhula mawu ambirimbiri mʼmalilime.
20 Abale, lekani kuganiza ngati ana. Mukhale ana pa nkhani ya zoyipa koma mʼmaganizo anu mukhale okhwima. 21 Zinalembedwa mʼMalamulo kuti,
“Ndidzayankhula kwa anthu awa,
kudzera mwa anthu aziyankhulo zachilendo
ndiponso ndi milomo yachilendo.
Koma ngakhale nthawi imeneyo sadzandimvera Ine,
akutero Ambuye.”
22 Kotero, malilime ndi chizindikiro, osati cha kwa okhulupirira koma kwa osakhulupirira. Koma kunenera ndi chizindikiro kwa okhulupirira osati kwa osakhulupirira. 23 Kotero kuti ngati mpingo wonse utasonkhana pamodzi ndipo aliyense namayankhula malilime, ndipo wina amene sangazindikire kapena ena osakhulupirira nabwerapo, kodi sadzanena kuti mwachita misala? 24 Koma ngati wosakhulupirira kapena wina amene sakuzindikira abwera pamene aliyense akunenera, adzatsutsika mu mtima ndi zonse zimene akumva ndipo adzaweruzidwa ndi onse 25 ndipo zinsinsi za mu mtima mwake zidzawululika. Kotero kuti adzadzigwetsa pansi ndi kupembedza Mulungu akufuwula kuti, “Mulungu ali pakati panudi!”
Kupembedza Mwadongosolo
26 Kodi tsono abale, tinene chiyani? Pamene musonkhana pamodzi, aliyense amakhala ali ndi nyimbo yoti ayimbe, kapena mawu oti alangize, vumbulutso, malilime, kapena kumasulira kwake. Zonsezi cholinga chake chikhale kulimbikitsa mpingo. 27 Ngati wina ayankhula malilime, awiri kapena akachulukapo atatu ndiye ayankhule mmodzimmodzi, ndipo wina ayenera kutanthauzira zimene ayankhulazo. 28 Ngati palibe wotanthauzira, woyankhulayo akhale chete mu mpingo ndipo adziyankhulire iye mwini ndi Mulungu.
29 Aneneri awiri kapena atatu anenere, ndipo enawo asanthule mosamalitsa zimene anenerazo. 30 Ndipo ngati vumbulutso labwera kwa munthu amene wakhala pansi, amene akuyankhulayo akhale chete. 31 Pakuti nonse mukhoza kunenera mmodzimmodzi motsatana kuti aliyense alangizidwe ndi kulimbikitsidwa. 32 Mizimu ya aneneri imamvera ulamuliro wa aneneri. 33 Pakuti Mulungu si Mulungu wachisokonezo koma wamtendere. Monga mwa mipingo yonse ya oyera mtima.
Amayi Akhale Chete mu Mpingo
34 Amayi akhale chete mʼmisonkhano ya mpingo. Iwo asaloledwe kuyankhula, koma azikhala omvera monga mmene lamulo linenera. 35 Ngati ali ndi mafunso, akafunse amuna awo ku nyumba. Nʼchochititsa manyazi kuti mkazi ayankhule mu msonkhano wa mpingo.
36 Kodi kapena mawu a Mulungu anachokera kwa inu? Kapena anafika kwa inu nokha? 37 Ngati wina aliyense akuganiza kuti ndi mneneri kapena kuti ali ndi mphatso za Mzimu, ayenera kudziwa kuti zimene ndikukulemberanizi ndi lamulo la Ambuye. 38 Ngati munthu savomereza zimenezi, iyeyonso sadzavomerezedwa.
39 Nʼchifukwa chake, abale anga, funitsitsani kunenera, ndipo musaletse anthu kuyankhula malilime. 40 Koma chilichonse chichitike moyenera ndi mwadongosolo.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.