Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Genesis 39

Yosefe ndi Mkazi wa Potifara

39 Tsopano Yosefe anatengedwa kupita ku Igupto. Potifara Mwigupto amene anali mmodzi wa akuluakulu a Farao ndiponso mkulu wa asilikali olonda ku nyumba kwa Farao, anagula Yosefe kwa Aismaeli amene anapita naye kumeneko.

Koma Yehova anali ndi Yosefe ndipo zake zonse zimayenda bwino. Iye ankakhala mʼnyumba ya mbuye wake wa ku Igupto. Mbuye wake anaona kuti Yehova anali naye Yosefe ndi kuti pa chilichonse chimene anachita Yehova ankaonetsetsa kuti achite bwino. Potifara anakondwera ndi Yosefe chifukwa cha matumikiridwe ake. Choncho anamusandutsa woyangʼanira nyumba yake ndi zonse za mʼnyumba yake. Kuchokera pa nthawi imene anamuyika kukhala woyangʼanira wa nyumbayo ndi zonse za mʼnyumbamo, Yehova anadalitsa nyumba ya Mwiguptoyo chifukwa cha Yosefe. Madalitso a Yehova anali pa chilichonse chimene Potifara anali nacho, za mʼnyumba komanso za ku munda. Choncho anasiyira mʼmanja mwa Yosefe chilichonse chomwe anali nacho, kotero kuti samadandaula ndi chilichonse kupatula chakudya chimene ankadya.

Tsopano Yosefe anali wa thupi labwino ndi wokongola. Patapita kanthawi, mkazi wa mbuye wake anayamba kusirira Yosefe nati, “Bwanji ugone nane!”

Koma iye anakana namuwuza kuti, “Inu mukuona kuti mbuye wanga sadandaula ndi kena kalikonse mʼnyumba muno, ndipo chawo chilichonse anachiyika mʼmanja mwanga. Motero kuti palibe wina wamkulu kuposa ine mʼnyumba muno. Ndipo palibe chilichonse chimene mbuye wanga sanachipereke kwa ine kupatula inuyo, chifukwa ndinu mkazi wake. Tsono ndingachite bwanji choyipa choterechi ndi kuchimwira Mulungu?” 10 Ndipo ngakhale kuti iye anayankhula mawu omwewa ndi Yosefe tsiku ndi tsiku, Yosefe sanalole kugona naye ngakhale kukhala naye pafupi.

11 Tsiku lina Yosefe analowa mʼnyumbamo kukagwira ntchito zake, ndipo munalibe wina aliyense wantchito mʼnyumbamo. 12 Mkazi uja anamugwira mkanjo Yosefe nati, “Tiye ugone nane!” Koma Yosefe anasiya mkanjo wake mʼmanja mwa mkaziyo nathawira kunja kwa nyumba.

13 Pamene mkazi uja anaona kuti Yosefe wamusiyira mkanjo wake mʼmanja mwake nathawira kunja kwa nyumba, 14 iye anayitana antchito ake a mʼnyumba nati, “Taonani mwamuna wanga anabwera ndi Mhebri uyu mʼnyumba muno kuti adzagone nane. Iyeyu analowa ku chipinda kwanga kuti adzagone nane ndipo ine ndinakuwa kwambiri. 15 Atandimva ndikukuwa, anandisiyira mkanjo wakewu nʼkuthawira kunja.”

16 Tsono mkazi wa Potifara uja anasunga mkanjowo mpaka mbuye wake wa Yosefe atabwera ku nyumba. 17 Tsono anamuwuza nkhaniyi nati: “Wantchito Wachihebri amene munatibweretsera uja anabwera kuti adzagone nane. 18 Koma pamene ndinakuwa, iye anandisiyira mkanjo wake nathawira kunja.”

19 Mbuye wake wa Yosefe atamva nkhani imene mkazi wake anamuwuza kuti, “Ndi zimene anandichitira wantchito wanu,” anapsa mtima kwambiri. 20 Tsono iye anatenga Yosefe namuyika mʼndende mmene ankasungiramo amʼndende a mfumu.

Ndipo Yosefe anakhala mʼndendemo 21 koma Yehova anali naye, ndipo anamuonetsa kukoma mtima kwake, kotero kuti woyangʼanira ndende anakondwera ndi Yosefe. 22 Choncho woyangʼanira ndende uja anamuyika Yosefe kukhala woyangʼanira onse amene anayikidwa mʼndende. Ndiponso anamupatsa udindo woyangʼanira zonse zochitika mʼndendemo. 23 Woyangʼanira ndende uja sankayangʼaniranso china chilichonse chimene chinali mu ulamuliro wa Yosefe, chifukwa Yehova anali ndi Yosefe. Ndipo Yehova anaonetsetsa kuti chilichonse chimene Yosefe ankachita chimuyendere bwino.

Marko 9

Ndipo anawawuza kuti, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti ena amene ayimirira pano sadzafa asanaone ufumu wa Mulungu ukubwera mwa mphamvu.”

Maonekedwe a Ulemerero wa Yesu pa Phiri

Patatha masiku asanu ndi limodzi Yesu anatenga Petro, Yakobo ndi Yohane nawatsogolera kupita ku phiri lalitali, kumene anali okhaokha. Kumeneko maonekedwe ake anasinthika pamaso pawo. Zovala zake zinawala monyezimira kwambiri, kotero kuti palibe sopo wina aliyense amene angaziyeretse monyezimira chotere pa dziko la pansi. Ndipo anaonekera Eliya ndi Mose pamaso pawo, amene ankayankhulana ndi Yesu.

Petro anati kwa Yesu, “Aphunzitsi, ndi kwabwino kuti ife tili pano. Tiyeni timange misasa itatu; umodzi wanu, wina wa Mose ndi wina wa Eliya.” (Iye sanadziwe choti anene, anali ndi mantha akulu).

Pamenepo mtambo unaoneka ndi kuwaphimba, ndipo mawu anamveka kuchokera mu mtambo kuti, “Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa. Mvereni Iye!”

Mwadzidzidzi, atayangʼanayangʼana, sanaonenso wina aliyense ali ndi iwo kupatula Yesu.

Pamene ankatsika kuchokera ku phiri, Yesu anawalamulira kuti asawuze aliyense zimene anaona mpaka Mwana wa Munthu atauka kwa akufa. 10 Iwo anayisunga nkhaniyo nakambirana za tanthauzo lake la “Kuuka kwa akufa.”

11 Ndipo anamufunsa Iye kuti, “Nʼchifukwa chiyani aphunzitsi amalamulo amati Eliya ayenera kuyamba wabwera?”

12 Yesu anayankha kuti, “Kunena motsimikiza, Eliya ayeneradi kuyamba kubwera kudzakonzanso zinthu zonse. Nʼchifukwa chiyani tsono zinalembedwa, kuti Mwana wa Munthu ayenera kuvutika kwambiri ndi kukanidwa? 13 Koma ndikuwuzani, kuti Eliya wabweradi, ndipo amuchitira iye zonse zimene iwo anafuna, monga momwe zalembedwera za iye.”

Kuchiritsidwa kwa Mnyamata Wogwidwa ndi Mzimu Woyipa

14 Atafika kwa ophunzira ena aja, anaona gulu lalikulu la anthu litawazungulira ndi aphunzitsi amalamulo akutsutsana nawo. 15 Nthawi yomweyo anthu onse atamuona, anadabwa kwambiri ndipo anathamanga kukamulonjera.

16 Iye anafunsa kuti, “Mukukangana nawo chiyani iwowa?”

17 Munthu wina mʼgululo anayankha kuti, “Aphunzitsi, ndinakubweretserani mwana wanga wamwamuna, amene ndi ogwidwa ndi mzimu umene umamulepheretsa kuyankhula. 18 Nthawi iliyonse ukamugwira umamugwetsa pansi. Amatuluka thovu kukamwa, amakukuta mano ake ndipo amawuma. Ndinapempha ophunzira anu kuti awutulutse mzimuwo, koma sanathe.”

19 Yesu anayankha kuti, “Haa! Mʼbado osakhulupirira, kodi ndidzakhala nanu mpaka liti? Mubweretseni kwa Ine mnyamatayo.”

20 Ndipo anamubweretsa kwa Iye. Mzimu woyipawo utaona Yesu, nthawi yomweyo unamukomola mnyamatayo. Anagwa pansi ndi kumagubuduka, ndi kuchita thovu kukamwa.

21 Yesu anafunsa abambo a mnyamatayo kuti, “Kodi wakhala chotere nthawi yayitali bwanji?”

Iye anayankha kuti, “Kuyambira ali wamngʼono, 22 wakhala ukumuponya pa moto kapena mʼmadzi kuti umuphe. Koma ngati mungathe kuchita kanthu, tichitireni chifundo ndipo mutithandize.”

23 Yesu anati, “ ‘Ngati mungathe!’ Zinthu zonse ndi zotheka kwa iye amene akhulupirira.”

24 Nthawi yomweyo abambo a mwanayo anafuwula kuti, “Ndikhulupirira; thandizani kusakhulupirira kwanga!”

25 Yesu ataona kuti gulu la anthu likuthamangira kumalowo, anadzudzula mzimu woyipawo kuti, “Iwe mzimu wolepheretsa kuyankhula ndi kumva, ndikulamulira tuluka mwa iye ndipo usadzalowenso.”

26 Mzimuwo unafuwula ndi kumugubuduza kwambiri ndipo unatuluka. Mnyamatayo anaoneka ngati mtembo ndipo ambiri anati, “Wafa.” 27 Koma Yesu anamugwira dzanja ndipo anamuyimiritsa, ndipo anayimirira.

28 Yesu atalowa mʼnyumba, ophunzira ake anamufunsa ali pa okha kuti, “Kodi ndi chifukwa chiyani ife sitinathe kutulutsa chiwandacho?”

29 Iye anayankha kuti, “Mtundu uwu umatuluka pokhapokha mwapemphera ndi kusala kudya.”

Yesu aneneratu za Imfa yake Kachiwiri

30 Anachoka malo amenewo nadutsa ku Galileya. Yesu sanafune kuti wina aliyense adziwe kumene anali, 31 chifukwa amaphunzitsa ophunzira ake. Anati kwa iwo, “Mwana wa Munthu adzaperekedwa mʼmanja mwa anthu. Adzamupha, ndipo patatha masiku atatu adzauka.” 32 Koma sanazindikire chimene amatanthauza, ndipo anachita mantha kuti amufunse.

Wamkulu Ndani mu Ufumu wa Mulungu?

33 Anafika ku Kaperenawo. Pamene anali mʼnyumba, anawafunsa kuti, “Kodi mumatsutsana chiyani mʼnjira muja?” 34 Koma anakhala chete chifukwa ali mʼnjira amatsutsana za kuti wamkulu kuposa onse ndani.

35 Atakhala pansi, Yesu anayitana khumi ndi awiriwo nati, “Ngati wina aliyense afuna kukhala woyamba, ayenera kukhala wotsiriza ndi wotumikira onse.”

36 Anatenga kamwana nakayimiritsa pakati pawo ndipo anawawuza kuti, 37 “Aliyense wolandira mmodzi wa ana angʼono awa mʼdzina langa alandira Ine; ndipo aliyense wolandira Ine salandira Ine koma amene anandituma.”

Wosatsutsana Nafe Athandizana Nafe

38 Yohane anati, “Aphunzitsi, tinaona munthu akutulutsa ziwanda mʼdzina lanu ndipo ife tinamuwuza kuti aleke, chifukwa sanali mmodzi wa ife.”

39 Yesu anati, “Musamuletse, palibe amene amachita chodabwitsa mʼdzina langa ndipo kenaka nanena zoyipa za Ine, 40 pakuti aliyense amene satsutsana nafe ali mbali yathu. 41 Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti aliyense amene akupatsani chikho cha madzi mʼdzina langa chifukwa ndinu ake a Khristu, sadzataya konse mphotho yake.”

Zochimwitsa Ena

42 “Ndipo ngati wina aliyense achimwitsa mmodzi wa ana angʼono awa amene akhulupirira Ine, kukanakhala bwino kwa iye kuti aponyedwe mʼnyanja atamangiriridwa mwala waukulu mʼkhosi mwake. 43 Ngati dzanja lako likuchimwitsa, lidule. Ndi kwabwino kwa iwe kulowa mʼmoyo ndi dzanja limodzi kusiyana ndi kukhala ndi manja awiri ndi kupita ku gehena, kumene moto wake suzima. 44 (Kumene mphutsi zake sizifa ndipo moto wake suzima). 45 Ndipo ngati phazi lako likuchimwitsa, lidule. Ndi kwabwino kwa iwe kulowa mʼmoyo olumala kusiyana ndi kukhala ndi mapazi awiri ndi kuponyedwa mu gehena. 46 (Kumene mphutsi zake sizifa ndipo moto wake suzima). 47 Ndipo ngati diso lako likuchimwitsa, likolowole. Ndi kwabwino kwa iwe kulowa ufumu wa Mulungu ndi diso limodzi, kusiyana ndi kukhala ndi maso awiri ndi kuponyedwa mu gehena, 48 kumene

“ ‘mphutsi zake sizifa
    ndipo moto wake suzima.’

49 Aliyense adzayesedwa ndi moto.

50 “Mchere ndi wabwino, koma ngati utasukuluka, mungawukoleretsenso bwanji? Mukhale nawo mchere mwa inu nokha, ndipo mukhale pa mtendere wina ndi mnzake.”

Yobu 5

“Itana ngati ungathe, koma ndani adzakuyankhe?
    Kodi ndi kwa mngelo uti ungapezeko thandizo?
Mkwiyo umapha chitsiru,
    ndipo njiru imawononga wopusa.
Ine ndinaona chitsiru chitamera mizu,
    koma mwadzidzidzi nyumba yake inatembereredwa.
Ana ake alibe ndi chitetezo chomwe;
    amaponderezedwa mʼbwalo la milandu popanda owateteza.
Anthu anjala amamudyera zokolola zake,
    amamutengera ndi za pa minga pomwe,
    ndipo anthu akhwinthi amafunkha chuma chake.
Pakuti masautso satuluka mʼfumbi,
    ndipo kuwukira sikuchokera mʼdothi.
Komatu munthu amabadwira kuti azunzike
    monga momwe mbaliwali zimathethekera mlengalenga.

“Koma ndikanakhala ine, ndikanamudandawulira Mulungu;
    ndikanapereka mlandu wanga kwa Iye.
Iye amachita zozizwitsa zimene sizimvetsetseka,
    zodabwitsa zimene sizingatheke kuwerengedwa.
10 Iye amagwetsa mvula pa dziko lapansi,
    ndipo amathirira minda ya anthu.
11 Iye amakweza anthu wamba,
    ndipo iwo amene akulira amawayika pa malo otetezedwa.
12 Iyeyo amalepheretsa chiwembu cha anthu ochenjera,
    kotero kuti cholinga chawo sichipindula kanthu.
13 Iye amakola anthu ochenjera mu msampha wa kuchenjera kwawo,
    ndipo zolinga za atambwali amazithetsa msangamsanga.
14 Mdima umawagwera nthawi yamasana;
    nthawi yamasana amayenda moyambasayambasa monga nthawi ya usiku.
15 Mulungu amapulumutsa amphawi ku lupanga la mʼkamwa mwawo;
    amawapulumutsa mʼmanja mwa anthu amphamvu.
16 Choncho osauka ali ndi chiyembekezo,
    ndipo anthu opanda chilungamo amawatseka pakamwa.

17 “Wodala munthu amene Mulungu amamudzudzula;
    nʼchifukwa chake usanyoze chilango cha Wamphamvuzonse.
18 Pakuti Iye amavulaza koma amamanganso mabalawo;
    Iye amakantha munthu, komanso manja ake amachiritsa.
19 Pakuti adzakupulumutsa ku masautso nthawi ndi nthawi,
    mavuto angachuluke bwanji, sadzakukhudza ndi pangʼono pomwe.
20 Pa nthawi ya njala adzakulanditsa ku imfa,
    ndipo nthawi ya nkhondo adzakupulumutsa ku lupanga.
21 Adzakuteteza kwa anthu osinjirira,
    ndipo palibe chifukwa chochitira mantha pamene chiwonongeko chafika.
22 Uzidzaseka pa nthawi ya chiwonongeko ndi ya njala,
    ndipo palibe chifukwa chochitira mantha ndi zirombo za mʼdziko lapansi.
23 Pakuti udzachita pangano ndi miyala ya mʼmunda mwako,
    ndipo nyama zakuthengo zidzakhala nawe mwamtendere.
24 Udzadziwa kuti nyumba yako ndi malo otetezedwa;
    udzawerengera katundu wako ndipo sudzapeza kanthu kamene kasowapo.
25 Udzadziwa kuti ana ako adzakhala ambiri,
    ndipo zidzukulu zako zidzakhala ngati udzu wa mʼdziko lapansi.
26 Udzafika ku manda utakalamba,
    monga mitolo ya zokolola pa nyengo yake.

27 “Ife tafufuza zimenezi ndipo ndi zoona,
    choncho uzimvere ndi kuzitsata.”

Aroma 9

Chisankho Chopambana cha Mulungu

Ine ndikunena zoona mwa Khristu. Sindikunama ndipo chikumbumtima changa kudzera mwa Mzimu Woyera chikundichitira umboni. Ndili ndi chisoni chachikulu ndipo ndikumva kupwetekeka kosalekeza mu mtima mwanga. Pakuti ndikanafuna ine mwini nditatembereredwa ndi kuchotsedwa mwa Khristu chifukwa cha abale anga, amene ndi a mtundu wanga, anthu Aisraeli. Iwo anasankhidwa kukhala ana. Mulungu anawapatsa ulemerero, anachita nawo mapangano, kuwapatsa Malamulo, Nyumba yopembedzeramo ndi malonjezano ake. Awo ndi makolo athu. Kuchokera kwa iwo mʼthupi ndi kumene kunachokera makolo a Khristu Yesu amene ndi Mulungu wolamulira zinthu zonse, alemekezeke mpaka muyaya! Ameni.

Sikuti mawu a Mulungu analephera. Pakuti si onse obadwa mwa Israeli amene ndi Israeli. Kapena kuti ana ake chifukwa anachokera mwa Abrahamu. Koma zidzukulu zako zidzachokera mwa Isake. Kutanthauza kuti, si ana obadwa mʼthupi amene ndi ana a Mulungu koma ndi ana a lonjezano amene amatengedwa kukhala zidzukulu za Abrahamu. Pakuti Mulungu analonjeza ponena kuti, “Pa nthawi yake ngati yomwe ino chaka chamawa ndidzabweranso, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna.”

10 Ndipo si pokhapo ayi. Ana awiri a Rebeka aja abambo awo anali mmodzi, kholo lathu Isake. 11 Komabe, ana amapasawa asanabadwe kapena asanachite chilichonse chabwino kapena choyipa, nʼcholinga choti chifuniro cha Mulungu chosankhiratu munthu aliyense chipitirire, 12 osati chifukwa cha ntchito za munthu koma chifuniro cha Iye mwini, anawuza Rebeka kuti, “Wamkulu adzatumikira wamʼngʼono.” 13 Monga momwe kwalembedwa kuti, “Ine ndinakonda Yakobo, koma ndinamuda Esau.”

14 Nanga tsono tidzanena chiyani? Kodi Mulungu ndi osalungama? Ayi, ndi pangʼono pomwe! 15 Pakuti Mulungu anawuza Mose kuti,

“Ine ndidzachitira chifundo amene ndikufuna kumuchitira chifundo,
    ndipo ndidzakomera mtima amene ndikufuna kumukomera mtima.”

16 Nʼchifukwa chake, izi sizitengera zokhumba za munthu kapena kuyesetsa koma chifundo cha Mulungu. 17 Malemba akuti Mulungu anamuwuza Farao kuti, “Ine ndakuyika kukhala mfumu ndi cholinga choti ndionetse mphamvu zanga, kuti mwa iwe dzina langa litchuke pa dziko lonse lapansi.” 18 Choncho Mulungu amachitira chifundo munthu amene akufuna kumuchitira chifundo ndipo amawumitsa mtima munthu amene Iye akufuna kumuwumitsa mtima.

19 Tsono mmodzi wa inu nʼkundifunsa kuti, “Nanga nʼchifukwa chiyani Mulungu amatipeza olakwa? Nanga ndani amene amakana chifuniro chake?” 20 Koma ndiwe yani, munthu wamba, woti nʼkutsutsana ndi Mulungu? “Kodi chimene chinawumbidwa nʼkufunsa amene anachiwumba kuti, ‘Kodi unandiwumbiranji motere?’ ” 21 Kodi wowumba alibe ufulu wowumba kuchokera ku dothi lomwelo mbiya yamtengowapatali ndi ina yamtengo wotsika?

22 Koma Mulungu, anafuna kuonetsa mkwiyo wake ndi kuti mphamvu yake idziwike. Iye anapirira modekha mtima kwambiri zochita za anthu omwe anawakwiyirawo amene anayeneradi chiwonongeko. 23 Iye anachita izi kufuna kuonetsa kulemera kwa ulemerero wake ndi kuti udziwike kwa amene analandira chifundo chake. Iye anawakonzeratu kuti alandire ulemerero wake 24 ngakhale ifenso amene anatiyitana osati kuchokera kwa Ayuda okha komanso kwa a mitundu ina. 25 Monga momwe Mulungu akunenera mʼbuku la Hoseya kuti,

“Amene sanali anthu anga ndidzawatcha ‘anthu anga;’
    ndipo Ine ndidzatcha ‘wokondedwa wanga’ amene sali wokondedwa wanga,”

26 ndipo,

“Pamalo omwewo pamene ananena kuti,
    ‘Sindinu anthu anga,’
pomweponso adzawatchula kuti, ‘Ana a Mulungu wamoyo.’ ”

27 Yesaya anafuwula za Aisraeli kuti,

“Ngakhale chiwerengero cha Aisraeli chingakhale ngati mchenga wa ku nyanja,
    otsala okha ndiye adzapulumuke.
28 Pakuti Ambuye adzagamula milandu
    ya anthu pa dziko lapansi mofulumira ndi kumaliziratu.”

29 Monga momwe Yesaya ananena malo ena kuti,

“Ngati Yehova Wamphamvuzonse
    akanapanda kutisiyira zidzukulu,
ife tikanawonongeka
    ngati anthu a ku Sodomu, tikanakhala ngati anthu a ku Gomora.”

Kusakhulupirira kwa Aisraeli

30 Kodi nanga tidzati chiyani? Tidzati a mitundu ina amene sanafune chilungamo analandira chilungamo chachikhulupiriro 31 koma Aisraeli, amene anafuna chilungamo cha lamulo sanachilandire. 32 Chifukwa chiyani? Chifukwa iwo sanachifune ndi chikhulupiriro koma ngati mwa ntchito. Iwo anapunthwa pa “Mwala wopunthwitsa.” 33 Monga momwe kwalembedwa kuti,

“Taonani, Ine ndikuyika mwala mu Ziyoni wopunthwitsa anthu,
    thanthwe limene limagwetsa anthu.
Koma amene akhulupirira Iye sadzachititsidwa manyazi.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.