Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Genesis 35-36

Yakobo Abwerera ku Beteli

35 Tsono Mulungu anati kwa Yakobo, “Nyamuka uchoke kuno kupita ku Beteli. Kumeneko ukamange guwa lansembe la Mulungu amene anadza kwa iwe pamene umathawa Esau, mʼbale wako.”

Choncho Yakobo anawuza a pa banja pake ndi onse amene anali naye kuti, “Chotsani milungu yachilendo imene muli nayo, ndipo mudziyeretse nokha ndi kusintha zovala zanu. Tiyeni tinyamuke kuchoka kuno kupita ku Beteli. Kumeneko ndikamumangira guwa lansembe Mulungu amene anandithandiza pa nthawi za masautso anga, komanso amene wakhala nane mʼmayendedwe anga onse.” Choncho anamupatsa Yakobo milungu yachilendo yonse imene anali nayo pamodzi ndi ndolo. Iye anazikwirira pansi pa mtengo wa thundu ku Sekemu. Pamenepo ananyamuka, ndipo mtima woopa Mulungu unagwera anthu onse a mʼmizinda yozungulira, kotero kuti palibe aliyense amene anatsatira banja la Yakobo.

Yakobo ndi anthu onse anali naye aja anafika ku Luzi (ku Beteli) mu dziko la Kanaani. Kumeneko anamanga guwa lansembe nalitcha Eli Beteli, chifukwa kunali kumeneko kumene Mulungu anadziwulula yekha kwa Yakobo pamene ankathawa mʼbale wake.

Debora mlezi wa Rakele anamwalira komweko nayikidwa mʼmanda pansi pa mtengo wa thundu cha kumunsi kwa Beteli. Choncho panatchedwa Aloni-Bakuti (mtengo wamaliro).

Yakobo atabwera kuchokera ku Padanaramu, Mulungu anabweranso kwa iye namudalitsa. 10 Mulungu anati kwa iye, “Dzina lako ndiwe Yakobo, koma sudzatchedwanso Yakobo; koma udzatchedwa Israeli.” Choncho anamutcha iye Israeli.

11 Ndipo Mulungu anati kwa iye, “Ine ndine Mulungu Wamphamvuzonse; berekanani ndi kuchulukana. Mtundu wa anthu, inde, mitundu yambiri ya anthu idzatuluka mwa iwe, ndipo ena mwa zidzukulu zako adzakhala mafumu. 12 Dziko limene ndinapereka kwa Abrahamu ndi Isake ndiliperekanso kwa iwe. Lidzakhala lako ndi la zidzukulu zako.” 13 Kenaka Mulungu anamusiya Yakobo.

14 Yakobo anayika mwala wachikumbutso pa malo pamene Mulungu anayankhula naye paja. Iye anathirapo nsembe yachakumwa ndi yamafuta. 15 Yakobo anawatcha malo amene Mulungu anayankhula naye aja kuti Beteli.

Imfa ya Isake ndi Rakele

16 Kenaka anachoka ku Beteli. Koma ali pafupi kufika ku Efurata nthawi yakuti Rakele aone mwana inakwana. Iye anavutika pobereka. 17 Akanali chivutikire choncho, mzamba anamulimbikitsa nati, “Usaope pakuti ubala mwana wina wamwamuna.” 18 Tsono pamene Rakele ankapuma wefuwefu (popeza ankamwalira) iye anatcha mwana uja kuti Beni-Oni. Koma abambo ake anamutcha kuti Benjamini.

19 Choncho Rakele anamwalira ndipo anayikidwa pa njira yopita ku Efurata (Kumeneko ndiye ku Betelehemu). 20 Pa manda ake, Yakobo anayimika mwala wachikumbutso wa pa manda ndipo ulipobe mpaka lero.

21 Israeli (Yakobo) anasunthanso nakamanga tenti yake kupitirira nsanja ya Ederi. 22 Israeli akanali mʼderali, Rubeni anapita nakagonana ndi Biliha, mdzakazi wa abambo ake. Yakobo uja anazimva zimenezi.

Yakobo anali ndi ana aamuna khumi ndi awiri:

23 Ana a Leya ndi awa:

Rubeni anali mwana woyamba wa Yakobo,

Simeoni, Levi, Yuda, Isakara, ndi Zebuloni.

24 Ana a Rakele ndi awa:

Yosefe ndi Benjamini.

25 Ana a Biliha, wantchito wa Rakele ndi awa:

Dani ndi Nafutali.

26 Ana a Zilipa wantchito wa Leya ndi awa:

Gadi ndi Aseri.

Awa ndiwo ana a Yakobo amene anabadwira ku Padanaramu.

27 Yakobo anafika ku mudzi kwa abambo ake Isake ku Mamre, (kumene kunkatchedwa ku Kiriyati-Ariba kapenanso Hebroni) kumene Abrahamu ndi Isake anakhalako kale. 28 Isake anakhala ndi moyo zaka 180. 29 Anamwalira ali wokalamba kwambiri ndipo anakakhala ndi anthu a mtundu wake. Ndipo ana ake Esau ndi Yakobo anamuyika mʼmanda.

Zidzukulu za Esau

36 Nazi zidzukulu za Esau amene ankatchedwanso Edomu:

Esau anakwatira akazi atatu a ku Kanaani. Iwowa ndiwo Ada mwana wa Eloni Mhiti; Oholibama mwana wa Ana amene anali mwana wa Zibeoni Mhivi ndi Basemati mwana wa Ismaeli, amenenso anali mlongo wa Nabayoti.

Ada anaberekera Esau, Elifazi; Basemati anabereka Reueli; ndipo Oholibama anabereka Yeusi, Yolamu ndi Kora. Amenewa anali ana a Esau amene anabadwira ku Kanaani.

Esau anatenga akazi ake, ana ake aamuna ndi aakazi ndi ena onse a pa banja pake. Anatenganso ziweto zake ndi ziweto zake zonse pamodzi ndi katundu wake yense amene anamupata ku Kanaani, ndipo anachoka ku dziko la Kanaani kupatukana ndi mʼbale wake Yakobo. Iwo anatero chifukwa dziko limene ankakhalamo silikanakwanira awiriwo. Iwowa anali ndi ziweto zochuluka motero kuti sakanatha kukhala pamodzi. Choncho Esau (amene ndi Edomu) anakakhazikika ku dziko la mapiri ku Seiri.

Nazi zidzukulu za Esau, kholo la Aedomu amene ankakhala ku Seiri.

10 Awa ndi mayina a ana aamuna a Esau:

Elifazi, mwana wa Ada, mkazi wa Esau, ndi Reueli, mwana wamwamuna wa Basemati, mkazi wa Esau.

11 Awa ndi mayina a ana a Elifazi:

Temani, Omari, Zefo, Gatamu ndi Kenazi.

12 Timna anali mzikazi wa Elifazi, mwana wa Esau. Iyeyo anaberekera Elifazi mwana dzina lake Amaleki. Amenewa ndiwo zidzukulu za Ada, mkazi wa Esau.

13 Awa ndi ana a Reueli:

Nahati, Zera, Sama ndi Miza. Amenewa ndi ana a Basemati, mkazi wa Esau.

14 Ana aamuna a Oholibama, mkazi wa Esau, mwana wa Ana ndi mdzukulu wa Zebeoni ndi awa:

Yeusi, Yolamu ndi Kora.

15 Nawa mafumu a zidzukulu za Esau:

Mwa ana a Elifazi, mwana woyamba wa Esau panali mafumu awa:

Temani, Omari, Zefo, ndi Kenazi, 16 Kora, Gatamu, ndi Amaleki. Awa anali mafumu mwa ana a Elifazi ku Edomu ndipo onsewa anali zidzukulu za Ada.

17 Mwa ana a Reueli, mwana wa Esau munali mafumu awa:

Nahati, Zera, Sama ndi Miza. Awa anali mafumu mwa ana a Reueli ku Edomu. Iwowa anali zidzukulu za Basemati mkazi wa Esau.

18 Mwa ana a Oholibama, mkazi wa Esau munali mafumu awa:

Yeusi, Yolamu, ndi Kora. Amenewa anali mafumu mwa ana a mkazi wa Esau, Oholibama, mwana wa Ana.

19 Amenewa ndiwo zidzukulu za Esau (amene ndi Edomu) ndiponso mafumu awo.

20 Awa ndi ana a Seiri Mhori, amene ankakhala mʼdzikomo:

Lotani, Sobala, Zibeoni, Ana, 21 Disoni, Ezeri ndi Disani. Amenewa ndiwo ana a Seiri a ku Edomu ndipo analinso mafumu a Ahori.

22 Ana aamuna a Lotani anali awa:

Hori ndi Homamu. Timna anali mlongo wake wa Lotani.

23 Ana aamuna a Sobala anali awa:

Alivani, Manahati, Ebala, Sefo ndi Onamu.

24 Ana aamuna a Zibeoni anali awa:

Ayiwa ndi Ana. Uyu ndi Ana amene anapeza akasupe a madzi amoto mʼchipululu pamene ankadyetsa abulu abambo wake Zibeoni.

25 Ana a Ana anali:

Disoni ndi Oholibama mwana wake wamkazi.

26 Ana aamuna a Disoni anali awa:

Hemudani, Esibani, Itirani ndi Kerani.

27 Ana aamuna a Ezeri anali awa:

Bilihani, Zaavani ndi Akani.

28 Ana aamuna a Disani anali awa:

Uzi ndi Arani.

29 Mafumu a Ahori anali awa:

Lotani, Sobala, Zibeoni, Ana, 30 Disoni, Ezeri ndi Disani. Amenewa ndiwo mafumu a Ahori, monga mwa mafuko awo, mʼdziko la Seiri.

Mafumu a ku Edomu

31 Awa ndi mafumu amene ankalamulira dziko la Edomu, mfumu iliyonse ya Israeli isanayambe kulamulira kumeneko:

32 Bela mwana wa Beori anakhala mfumu ya ku Edomu. Mzinda wake ankawutcha Dinihaba.

33 Bela atamwalira, Yobabu mwana wa Zera wochokera ku Bozira analowa ufumu mʼmalo mwake.

34 Atafa Yobabu, Husamu wochokera ku dziko la Atemani, analowa mʼmalo mwake ngati mfumu.

35 Husamu atamwalira, Hadadi mwana wa Bedadi, amene anagonjetsa Amidiyani mʼdziko la Mowabu, analowa ufumu mʼmalo mwake. Mzinda wake unkatchedwa Aviti.

36 Hadadi atamwalira, Samila wochokera ku Masireka, analowa ufumu mʼmalo mwake.

37 Samila atamwalira, Sauli wochokera ku Rehoboti wa ku Mtsinje, analowa ufumu mʼmalo mwake.

38 Sauli atamwalira, Baala-Hanani, mwana wa Akibori analowa ufumu mʼmalo mwake.

39 Pamene Baala-Hanani mwana wa Akibori anamwalira, Hadari analowa ufumu mʼmalo mwake. Mzinda wake unkatchedwa Pau, ndipo dzina la mkazi wake linali Mehatabeli, mwana wamkazi wa Matiredi, mwana wamkazi wa Me-Zahabu.

40 Mayina a mafumu ochokera mwa zidzukulu za Esau malingana ndi mafuko awo ndi malo a fuko lililonse anali awa:

Timna, Aliva, Yeteti, 41 Oholibama, Ela, Pinoni, 42 Kenazi, Temani, Mibezari, 43 Magidieli ndi Iramu. Awa anali mafumu a ku Edomu molingana ndi malo awo okhala mʼdzikomo.

Umenewu ndi mndandanda wa mʼbado wa Esau, kholo la Aedomu.

Marko 6

Amupeputsa Yesu ku Nazareti

Yesu anachoka kumeneko napita ku mudzi kwawo, pamodzi ndi ophunzira ake. Tsiku la Sabata litafika, anayamba kuphunzitsa mʼsunagoge, ndipo ambiri amene anamumva anadabwa.

Iwo anafunsa kuti, “Kodi munthu uyu anazitenga kuti zimenezi? Kodi ndi nzeru yotani imene munthu ameneyu wapatsidwa, kuti Iye akuchitanso zodabwitsa! Kodi uyu si mpalamatabwa uja? Kodi uyu si mwana wa Mariya ndi mʼbale wa Yakobo, Yose, Yudasi ndi Simoni? Kodi alongo ake si ali ndi ife?” Ndipo anakhumudwa naye.

Yesu anawawuza kuti, “Mneneri amalemekezedwa kulikonse kupatula kwawo, ndi pakati pa abale ake ndi a mʼbanja mwake.” Sanachite zodabwitsa kumeneko, koma anangosanjika manja pa odwala ochepa ndi kuwachiritsa. Ndipo Iye anadabwa chifukwa chakusowa chikhulupiriro kwawo.

Yesu Atuma Ophunzira Khumi ndi Awiri

Pamenepo Yesu anayenda mudzi ndi mudzi kuphunzitsa. Atayitana khumi ndi awiriwo, Iye anawatuma awiriawiri ndipo anawapatsa ulamuliro pa mizimu yoyipa.

Zomwe anawalangiza ndi izi: “Musatenge kanthu ka paulendo koma ndodo yokha; osatenga buledi, thumba, kapena ndalama. Muvale nsapato koma osatenga malaya apadera. 10 Pamene mulowa mʼnyumba mukakhale momwemo kufikira mutachoka mʼmudzimo. 11 Ndipo ngati pa malo ena sakakulandirani kapena kukumverani, sasani fumbi la kumapazi anu pamene mukuchoka, kuti ukhale umboni wowatsutsa.”

12 Anatuluka kupita kukalalikira kuti anthu atembenuke mtima. 13 Anatulutsa ziwanda zambiri ndi kudzoza mafuta odwala ambiri ndi kuwachiritsa.

Yohane Mʼbatizi Adulidwa Mutu

14 Mfumu Herode anamva zimenezi, pakuti dzina la Yesu linali litadziwika kwambiri. Ena amati, “Yohane Mʼbatizi waukitsidwa kwa akufa, ndipo nʼchifukwa chake mphamvu zochita zodabwitsa zinkagwira ntchito mwa Iye.”

15 Ena anati, “Iye ndi Eliya.”

Enanso anati, “Ndi mneneri, ofanana ndi mmodzi wa aneneri akale.”

16 Koma Herode atamva zimenezi anati, “Yohane, munthu amene ndinamudula mutu, waukitsidwa kuchokera kwa akufa.”

17 Pakuti Herode iye mwini analamula kuti amumange Yohane ndi kumuyika mʼndende. Anachita izi chifukwa cha Herodia, mkazi wa mʼbale wake Filipo, amene iye anamukwatira. 18 Pakuti Yohane ankanena kwa Herode kuti, “Sikololedwa kwa inu kuti mukwatire mkazi wa mʼbale wanu.” 19 Ndipo Herodia anamusungira Yohane chidani ndipo anafuna kumupha, koma sanathe kutero, 20 chifukwa Herode anaopa Yohane ndipo anamuteteza, podziwa kuti iye anali munthu wolungama ndi woyera mtima. Herode akamamva Yohane, ankathedwa nzeru; komabe amakonda kumumvetsera.

21 Pomaliza mpata unapezeka. Pa tsiku lokumbukira kubadwa kwake, Herode anakonzera phwando akuluakulu ake, akulu a ankhondo ndi anthu odziwika a mu Galileya. 22 Mwana wamkazi wa Herodia atabwera ndi kudzavina, anakondweretsa Herode ndi alendo ake a pa mphwandopo.

Mfumu inati kwa mtsikanayo, “Undipemphe chilichonse chimene ukuchifuna, ndipo ndidzakupatsa.” 23 Ndipo analonjeza ndi lumbiriro kuti, “Chilichonse chimene upempha ndidzakupatsa, ngakhale theka la ufumu wanga.”

24 Iye anatuluka nati kwa amayi ake, “Kodi ndikapemphe chiyani?”

Iye anamuyankha kuti, “Mutu wa Yohane Mʼbatizi.”

25 Nthawi yomweyo mtsikana uja anafulumira kupita komwe kunali mfumu ndi pempho lake: “Ndikufuna kuti mundipatse pomwe pano mutu wa Yohane Mʼbatizi mʼmbale.”

26 Mfumu inamva chisoni chachikulu, koma chifukwa cha lumbiro lake ndi alendo ake a pa mphwandolo, sanafune kumukaniza. 27 Nthawi yomweyo iye anatumiza yemwe anali ndi ulamuliro wonyonga anthu kuti abweretse mutu wa Yohane. Munthuyo anapita, nakadula mutu wa Yohane mʼndende, 28 nabweretsa mutuwo mʼmbale. Anawupereka kwa mtsikanayo, ndipo iye anakapereka kwa amayi ake. 29 Atamva izi, ophunzira a Yohane anabwera nadzatenga mtembo ndi kukawuyika mʼmanda.

Yesu Adyetsa Anthu 5,000

30 Atumwi anasonkhana mozungulira Yesu namufotokozera zonse zomwe anachita ndi kuphunzitsa. 31 Popeza kuti panali anthu ambiri amene amabwera ndi kumapita, analibe mpata wakuti adye, ndipo Iye anawawuza kuti, “Tiyeni kuno kumalo achete kuti tikapume.”

32 Ndipo anachoka okha pa bwato napita kumalo a okhaokha. 33 Koma ambiri amene anawaona akuchoka anawazindikira ndipo anathamanga wapansi kuchokera mʼmidzi yonse nakayambirira kufika. 34 Yesu atafika ku mtunda ndi kuona gulu lalikulu la anthu, anamva nawo chisoni chifukwa anali ngati nkhosa zopanda mʼbusa. Ndipo anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.

35 Pa nthawi iyi nʼkuti dzuwa litapendeka, ndipo ophunzira ake anabwera kwa Iye nati, “Kuno ndi kuthengo, ndipo ano ndi madzulo. 36 Awuzeni anthuwa azipita ku midzi ndi madera ozungulira, kuti akadzigulire kanthu kakuti adye.”

37 Koma Iye anayankha kuti, “Apatseni kanthu koti adye.”

Iwo anati kwa Iye, “Apa pafunika ndalama za miyezi isanu ndi itatu zomwe munthu amalandira! Kodi tipite kukagwiritsa ntchito ndalama zotere kugulira buledi kuti tiwapatse adye?”

38 Iye anawafunsa kuti, “Muli ndi malofu a buledi angati? Pitani mukaone.”

Ataona anati kwa Iye, “Asanu ndi nsomba ziwiri.”

39 Pamenepo Yesu anawalamulira kuti awakhazike anthu pansi mʼmagulu pa msipu obiriwira. 40 Ndipo anakhala pansi mʼmagulu a anthu 100 ndi gulu la anthu makumi asanu. 41 Atatenga malofu a buledi asanu ndi nsomba ziwiri, nayangʼana kumwamba, Iye anayamika nagawa malofu a bulediwo. Kenaka anawapatsa ophunzira ake kuti awapatse anthu. Ndipo anagawanso nsomba ziwirizo kwa onse. 42 Onse anadya ndipo anakhuta, 43 ndipo ophunzira ake anatola buledi ndi nsomba zotsalira zokwanira madengu khumi ndi awiri. 44 Chiwerengero cha amuna amene anadya chinali 5,000.

Yesu Ayenda pa Nyanja

45 Nthawi yomweyo Yesu anawuza ophunzira ake kuti alowe mʼbwato ndi kuti atsogole kupita ku Betisaida, pamene Iye ankawuza anthu kuti azipita. 46 Atawasiya, Iye anakwera ku phiri kukapemphera.

47 Pofika madzulo, bwato linali pakati pa nyanja, ndipo Iye anali yekha pa mtunda. 48 Iye anaona ophunzira ake akuvutika popalasa bwato, chifukwa mphepo imawomba mokumana nawo. Pa nthawi ya mʼbandakucha Iye anafika kwa iwo akuyenda pa nyanja. Anali pafupi kuwapitirira, 49 koma atamuona Iye akuyenda pa nyanja, anaganiza kuti anali mzukwa. Iwo anafuwula, 50 pakuti onse anamuona ndipo anachita mantha.

Nthawi yomweyo Iye anawayankhula nati, “Limbani mtima! Ndine. Musachite mantha.” 51 Ndipo Iye anakwera mʼbwato pamodzi nawo, ndipo mphepo inaleka. Iwo anadabwa kwambiri, 52 popeza sanazindikire zimene zinachitika pa malofu a buledi; pakuti mitima yawo inali yowuma.

53 Atawoloka, anafika ku Genesareti nayima pa dooko. 54 Atangotuluka mʼbwato, anthu anamuzindikira Yesu. 55 Anathamanga uku ndi uko mʼdera lonse nakanyamula odwala pa machira kupita nawo kulikonse kumene anamva kuti kuli Iye. 56 Ndipo kulikonse kumene anapita, ku midzi, mʼmizinda ndi madera a ku midzi, iwo anayika odwala mʼmalo a mʼmisika. Iwo anamupempha kuti awalole kuti akhudze ngakhale mphonje za mkanjo wake, ndipo onse amene anamukhudza anachira.

Yobu 2

Yobu Ayesedwa Kachiwiri

Tsiku linanso pamene ana a Mulungu anabwera kudzadzionetsa pamaso pa Yehova, nayenso Satana anabwera nawo limodzi kudzadzionetsa pamaso pa Yehova. Ndipo Yehova anati kwa Satana, “Kodi iwe ukuchokera kuti?”

Satana anayankha Yehova kuti, “Ndakhala ndikungoyendayenda ndi kumangozungulira mʼdzikoli.”

Pamenepo Yehova anati kwa Satana, “Kodi unalingalirapo za mtumiki wanga Yobu? Palibe wina pa dziko lapansi wofanana naye; ndi munthu wosalakwa ndi wolungama mtima, munthu amene amaopa Mulungu ndi kupewa zoyipa. Ndipo iye akanalibe wangwiro, ngakhale iwe unandiwumiriza kuti ndikulole kuti umuvutitse popanda chifukwa.”

Satana anayankha kuti, “Iye ayesedwe mʼthupi mwake. Munthu angathe kupereka zonse ali nazo malingana iyeyo ali ndi moyo. Koma tatambasulani dzanja lanu ndi kuwononga thupi lake, ndipo iyeyo adzakutukwanani ndithu pamaso panu.”

Yehova anati kwa Satana, “Chabwino, iye ali mʼmanja mwako; koma moyo wake usawuchotse.”

Choncho Satana anachoka pamaso pa Yehova napita kukazunza Yobu ndi zilonda zaululu pa thupi lake lonse. Pamenepo Yobu anatenga phale ndi kumadzikanda nalo atakhala pa dzala la phulusa.

Mkazi wake anati kwa iye, “Kodi ukuwumirirabe kukhala wangwiro? Tukwana Mulungu kuti ufe!”

10 Yobu anayankha kuti, “Ukuyankhula ngati mkazi wopusa. Kodi tidzalandira zokoma zokhazokha kwa Mulungu, osalandiranso zowawa?”

Mu zonsezi, Yobu sanachimwe pa zimene anayankhula.

Abwenzi Atatu a Yobu

11 Abwenzi atatu a Yobu, Elifazi wa ku Temani, Bilidadi wa ku Suki ndi Zofari wa ku Naama, atamva za tsoka lonse limene linamugwera iye, ananyamuka ku nyumba zawo nakumana malo amodzi mopangana kuti apite ndi kukamupepesa Yobu ndi kumutonthoza. 12 Atamuona Yobuyo, iwo ali chapatalipo, sanathe kumuzindikira. Choncho anayamba kulira mokweza mawu ndipo anangʼamba mikanjo yawo ndi kuwaza fumbi pa mitu yawo. 13 Tsono anakhala naye pamodzi pansi kwa masiku asanu ndi awiri, usana ndi usiku omwe. Palibe ndi mmodzi yemwe anayankhula naye, chifukwa anazindikira kuti Yobu amavutika kwambiri.

Aroma 6

Kufa ku Tchimo, Kukhala ndi Moyo mwa Khristu

Nanga tinene chiyani? Kodi tipitirire kuchimwa kuti chisomo chichulukebe? Ayi. Mʼnjira iliyonse! Popeza tinafa ku tchimo, nanga tidzapitirira bwanji kukhalabe mʼmenemo? Kodi simukudziwa kuti tonse amene tinabatizidwa mwa Khristu Yesu tinabatizidwa mu imfa yake? Chifukwa chake ife tinayikidwa mʼmanda pamodzi ndi Iye mwa ubatizo. Tinalowa mu imfa ndi cholinga choti monga momwe Khristu anaukitsidwa kwa akufa ndi ulemerero wa Atate, ifenso tikakhale mʼmoyo watsopano.

Pakuti ngati ife tinakhala amodzi ndi Iye mu imfa yake, tidzakhalanso ndithu amodzi ndi Iye mu kuuka kwake. Ife tikudziwa kuti umunthu wathu wakale unapachikidwa pamodzi ndi Iye kuti thupi la uchimo likhale lopanda mphamvu ndi kuti tisakakhalenso akapolo a tchimo chifukwa aliyense amene anafa anamasuka ku tchimo.

Koma ngati tinafa pamodzi ndi Khristu, tikhulupirira kuti tidzakhalanso ndi moyo pamodzi ndi Iye. Pakuti tikudziwa kuti popeza Khristu anaukitsidwa kwa akufa, Iye sangafenso. Imfa ilibenso mphamvu pa Iye. 10 Imfa imene Iye anafa, anafa ku tchimo kamodzi kokha, koma moyo umene akhala ndi wa kwa Mulungu.

11 Kotero inunso, mudzione nokha ngati akufa ku tchimo koma a moyo kwa Mulungu mwa Khristu Yesu. 12 Nʼchifukwa chake, musalole tchimo lilamulire matupi anu amene anafa kuti mumvere zilakolako zonyansa. 13 Musapereke ziwalo zathupi lanu ku tchimo, ngati zipangizo zamakhalidwe oyipa. Mʼmalo mwake, mudzipereke kwa Mulungu, ngati amene achoka ku imfa kupita ku moyo. Ndipo mupereke ziwalo zathupi lanu ngati zipangizo zachilungamo. 14 Tchimo silidzakhalanso ndi mphamvu pa inu, chifukwa Malamulo sakulamulira moyo wanu koma chisomo.

Ife Ndife Akapolo a Mulungu

15 Nʼchiyani tsono? Kodi tidzichimwa chifukwa sitikulamulidwa ndi Malamulo koma chisomo? Ayi. Mʼnjira iliyonse ayi! 16 Kodi inu simudziwa kuti pamene mudzipereka kwa wina wake, kumumvera ngati akapolo, ndinu akapolo a amene mumumvera? Ngati ndinu akapolo a tchimo mudzafa. Koma ngati ndinu akapolo akumvera, mudzakhala olungama pamaso pake. 17 Koma ayamikidwe Mulungu pakuti ngakhale munali akapolo a tchimo, munamvera ndi mtima wonse chiphunzitso chimene munalandira. 18 Inu munamasulidwa ku tchimo ndipo tsopano mwasanduka akapolo achilungamo.

19 Ine ndikufanizira zinthu za tsiku ndi tsiku chifukwa chikhalidwe chanu nʼchofowoka. Monga momwe munkapereka ziwalo za matupi kukhala akapolo a zonyansa ndi makhalidwe oyipa, zimene zimanka zichulukirabe, choncho tsopano dziperekeni ziwalozo kuti zikhale akapolo achilungamo ndi a kuyera mtima. 20 Pomwe munali akapolo atchimo, simunkalabadira za chilungamo. 21 Kodi munapeza phindu lanji pochita zinthu zimenezi, zomwe tsopano mukuchita nazo manyazi? Zinthu zimenezo zotsatira zake ndi imfa! 22 Koma tsopano pakuti inu mwamasulidwa ku tchimo ndipo mwasanduka akapolo a Mulungu, phindu lomwe mulipeza ndi kuyera mtima ndipo chotsatira chake ndi moyo wosatha. 23 Pakuti malipiro a tchimo ndi imfa, koma mphatso yaulere imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha mwa Khristu Yesu Ambuye athu.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.