Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Genesis 42

Abale a Yosefe Apita ku Igupto

42 Yakobo atamva kuti ku Igupto kuli tirigu, anati kwa ana ake, “Nʼchifukwa chiyani mukungoyangʼanana wina ndi mnzake? Ine ndamva kuti ku Igupto kuli tirigu. Pitani kumeneko mukatigulireko kuti tisafe ndi njala.”

Choncho abale ake khumi a Yosefe anapita kukagula tirigu ku Igupto. Koma Yakobo sanamulole Benjamini mngʼono wake wa Yosefe kuti apite nawo chifukwa anaopa kuti choyipa chingamuchitikire. Choncho ana a Israeli aja anapita pamodzi ndi gulu la anzawo kukagula tirigu pakuti ku Kanaani kunalinso njala.

Pakuti Yosefe anali nduna yayikulu yolamulira dziko la Igupto, ndiye kuti analinso amene ankagulitsa tirigu kwa anthu onse. Choncho abale ake a Yosefe nawonso anabwera, ndipo anamugwadira pansi. Yosefe atangowaona abale ake anawazindikira, koma ananamizira kukhala ngati mlendo nawayankhula mwaukali kuwafunsa kuti, “Mwachokera kuti?”

Iwo anayankha, “Ku dziko la Kanaani, tikudzagula chakudya.”

Ngakhale Yosefe anawazindikira abale ake, koma iwo sanamuzindikire. Pamenepo anakumbukira maloto aja amene analota za iwo ndipo anati, “Inu ndinu akazitape! Mwabwera kudzazonda dziko lathu kuti muone pamene palibe chitetezo.”

10 Iwo anayankha, “Ayi mbuye wathu, antchito anufe tabwera kudzagula chakudya. 11 Tonse ndife ana a munthu mmodzi. Ndife antchito anu okhulupirika osati akazitape.”

12 Iye anawawuza kuti, “Ayi! Inu mwabwera kudzaona pamene palibe chitetezo mʼdziko muno.”

13 Koma iwo anayankha, “Tinalipo ana aamuna khumi ndi awiri. Abambo athu ndi mmodzi, ndipo kwathu ndi ku Kanaani. Panopo wotsiriza ali ndi abambo athu ndipo wina anamwalira.”

14 Yosefe anawawuza kuti, “Ndi momwe ndaneneramo: Inu ndinu akazitape. 15 Ndiye ndikuyesani motere: Ine ndikulumbira pali Farao ndithu, inuyo simudzachoka malo ano mpaka wotsirizayo atabwera kuno. 16 Tumizani mmodzi wa inu akamutenge mʼbale wanuyo ndipo ena nonsenu musungidwa mʼndende, kuti titsimikize ngati zimene mukunenazi ndi zoona. Apo ayi, pali Farao ndithu, inu ndinu akazitape!” 17 Ndipo onse anawayika mʼndende kwa masiku atatu.

18 Pa tsiku lachitatu Yosefe anawawuza kuti, “Popeza ine ndimaopa Mulungu, ndipo inuyo ngati mukufuna kukhala ndi moyo muchite izi: 19 Ngati muli anthu achilungamo, mmodzi wa inu atsale mʼndende, pamene ena nonse mupite kwanu kuti muwatengere chakudya anthu akwanu kuli njalako. 20 Mukabwere naye kuno mngʼono wanu wotsirizayo kuti titsimikizire zimene munanena kuti musafe.” Ndipo anachita zomwezo.

21 Iwo anati kwa wina ndi mnzake, “Ndithu ife tinalakwira mʼbale wathu uja popeza kuti ngakhale tinaona kuvutika kwake ndi kumva kulira kwake pamene ankatidandaulira kuti timuchitire chifundo, koma ife sitinamvere. Nʼchifukwa chake masautso awa atigwera.”

22 Rubeni anayankha, “Kodi sindinakuwuzeni kuti musamuchite kanthu mnyamata uja? Koma inu simunamvere! Tsopano tikulandira malipiro a magazi ake.” 23 Koma sanadziwe kuti Yosefe ankawamva popeza kuti ankagwiritsa ntchito wotanthauzira poyankhula naye.

24 Yosefe anapita pambali payekha kukalira. Kenaka anabweranso nadzayankhula nawo. Iye anatenga Simeoni namumanga iwo akuona.

25 Yosefe analamula kuti awadzazire matumba awo ndi tirigu, awayikiremo ndalama zawo momwemo ndiponso awapatse chakudya cha panjira. Izi anawachitiradi. 26 Abale a Yosefe aja anasenzetsa abulu awo tirigu amene anagula uja ndipo ananyamuka ulendo wawo.

27 Atafika pamalo pena poti agone, mmodzi mwa iwo anatsekula thumba lake kuti atapemo chakudya cha bulu wake. Atangomasula anaona kuti ndalama zake zili pakamwa pa thumba. 28 Iye anati kwa abale akewo, “Ndalama zanga andibwezera, izi zili mʼthumba mwangamu.”

Mitima yawo inachita ngati yachokamo ndipo anali ndi mantha ambiri, nati, “Ndi chiyani chimene Mulungu watichitira?”

29 Atafika kwa abambo awo Yakobo mʼdziko la Kanaani anafotokoza zonse zimene zinawachitikira nati, 30 “Nduna yayikulu ya mʼdzikomo inatiyankhula mwa ukali kwambiri ndipo inkatiyesa kuti ndife akazitape. 31 Koma tinamuwuza kuti, ‘Ndife anthu woona mtima osati akazitape. 32 Ife tonse tinalipo ana aamuna khumi ndi awiri, abambo mmodzi. Mmodzi anamwalira, ndipo wamngʼono ali ndi abambo athu ku Kanaani.’ ”

33 Ndipo nduna ija inati kwa ife, “Kuti ndidziwedi kuti ndinu anthu owona mtima muchite izi: Mmodzi mwa inu atsale ndi ine kuno, ndipo enanu mutenge chakudya ndi kubwerera kwanu kumene kuli njalako. 34 Koma mundibweretsere wotsirizayo kuti ndidziwedi kuti sindinu akazitape koma anthu achilungamo. Kenaka ndidzakubwezerani mʼbale wanuyu ndipo mukhoza kuchita malonda mʼdzikoli.”

35 Pamene amakhuthula matumba awo a tirigu aliyense anapeza kuti kathumba kake ka ndalama kali momwemo. Ataona zimenezi, iwo pamodzi ndi abambo awo anachita mantha kwambiri. 36 Abambo awo Yakobo anawawuza kuti, “Mwandilanda ana anga ine. Yosefe anamwalira ndipo Simeoni palibenso, ndiye tsopano mukufuna mutengenso Benjamini. Zonsezi zandigwera ine!”

37 Koma Rubeni anati kwa abambo ake, “Ngati sindidzabwera naye kwa inu, mudzaphe ana anga aamuna awiri. Muperekeni mʼmanja mwangamu ndipo ndidzamusamala ndi kubwera naye kwa inu.”

38 Koma Yakobo anati, “Mwana wanga sapita nanu kumeneko; mkulu wake anamwalira ndipo watsala yekha. Ngati choyipa chitamuchitikira pa ulendo mukupitawu, ndiye kuti ndi mmene ndakalambiramu inu mudzandipha ndi chisoni chotere.”

Marko 12

Fanizo la Alimi

12 Kenaka Iye anayamba kuyankhula nawo mʼmafanizo: “Munthu wina analima munda wamphesa. Anamanga mpanda mozungulira, nakumba dzenje lofinyiramo mphesa ndipo anamanga nsanja. Anawubwereketsa munda wamphesawo kwa alimi ena napita ku dziko lina. Pa nthawi yokolola anatumiza wantchito kwa alimiwo kuti akatenge kuchokera kwa iwo zina mwa zipatso za munda wamphesa. Koma iwo anamugwira, namumenya ndi kumupirikitsa wopanda kanthu. Kenaka anatumizanso wantchito wina kwa iwo. Iwo anamumenya munthuyo pamutu ndipo anamuzunza mochititsa manyazi. Anatumizanso wina, ndipo iwo anamupha. Anatumizanso ena ambiri; ena a iwo anawamenya, ena anawapha.

“Munthu uja anatsala ndi mwana mmodzi, wamwamuna amene amamukonda. Pomaliza anamutumiza mwanayo nati, ‘Adzamuchitira ulemu mwana wanga.’

“Koma alimi aja anati kwa wina ndi mnzake, ‘Uyu ndi mlowamʼmalo. Tiyeni timuphe, ndipo cholowacho chidzakhala chathu.’ Ndipo anamutenga ndi kumupha, ndipo anamuponya kunja kwa munda wamphesa.

“Kodi nanga mwini munda wamphesa adzachita chiyani? Iye adzabwera ndi kupha alimiwo nadzapereka munda wamphesawo kwa ena. 10 Kodi simunawerenge lemba lakuti:

“ ‘Mwala umene amisiri omanga nyumba anawukana
    wakhala mwala wa pa ngodya.
11 Ambuye achita zimenezi,
    ndipo ndi zodabwitsa mʼmaso mwathu?’ ”

12 Ndipo akulu a ansembe, aphunzitsi a malamulo ndi akuluakulu anafunafuna njira yoti amugwirire Iye chifukwa amadziwa kuti anayankhula fanizoli mowatsutsa iwo. Koma amaopa gulu la anthu; ndipo anamusiya napita.

Za Kupereka Msonkho kwa Kaisara

13 Pambuyo pake anatuma ena a Afarisi ndi Aherode kwa Yesu kuti adzamukole mawu ake. 14 Iwo anabwera kwa Iye nati, “Aphunzitsi, ife tikudziwa kuti Inu ndi munthu amene mumanena zoona. Inu simutengeka ndi anthu, chifukwa simusamala kuti ndi ndani; koma mumaphunzitsa njira ya Mulungu molingana ndi choonadi. Kodi ndi koyenera kupereka msonkho kwa Kaisara kapena ayi? 15 Kodi ife tipereke msonkho kapena ayi?”

Koma Yesu anadziwa chinyengo chawo. Iye anafunsa kuti, “Bwanji mukufuna kundipeza chifukwa? Bweretsani ndalama kuti ndiyione.” 16 Iwo anamubweretsera ndalama, ndipo anawafunsa kuti, “Kodi nkhope iyi ndi ya ndani? Nanga malembawa ndi a ndani?”

Iwo anayankha kuti, “Za Kaisara.”

17 Ndipo Yesu anawawuza kuti, “Perekani kwa Kaisara zake za Kaisara ndi kwa Mulungu zake za Mulungu.”

Ndipo anazizwa naye.

Za Ukwati ndi Kuuka kwa Akufa

18 Kenaka Asaduki, amene amati kulibe kuuka kwa akufa, anabwera kwa Iye ndi funso. 19 Iwo anati, “Aphunzitsi, Mose anatilembera kuti munthu akamwalira ndi kusiya mkazi wopanda ana, mʼbale wa munthu womwalirayo akuyenera kukwatira mkaziyo kuti amuberekere ana mʼbale wakeyo. 20 Tsopano panali abale asanu ndi awiri. Woyamba anakwatira namwalira wosabereka ana. 21 Wachiwiri anakwatira mkazi wamasiyeyo, koma iye anamwalira wosabereka mwana. Zinali chimodzimodzi ndi wachitatu. 22 Kunena zoona, palibe ndi mmodzi yemwe wa asanu ndi awiriwo anasiya ana. Pomaliza, mkaziyo anamwaliranso. 23 Pa kuuka kwa akufa, adzakhala mkazi wa yani pakuti anakwatiwa ndi onse asanu ndi awiri?”

24 Yesu anawafunsa kuti, “Kodi si pamenepa nanga pomwe mumalakwira chifukwa simukudziwa malemba kapena mphamvu za Mulungu? 25 Pamene akufa auka, sadzakwatira kapena kukwatiwa; adzakhala ngati angelo kumwamba. 26 Tsopano kunena zakuti akufa amauka, kodi simunawerenge mʼbuku la Mose, pa nkhani yachitsamba choyaka moto, mmene Mulungu anati kwa iye, ‘Ine ndine Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo?’ 27 Iye si Mulungu wa anthu akufa, koma wa amoyo. Inu mwalakwitsa kwambiri!”

Lamulo Lalikulu Koposa

28 Mmodzi wa aphunzitsi amalamulo anabwera namva iwo akukambirana motsutsana. Poona kuti Yesu anawapatsa yankho labwino, anamufunsa Iye kuti, “Mwa malamulo onse, kodi lopambana koposa ndi liti?”

29 Yesu anayankha kuti, “Lamulo loposa onse ndi ili: ‘Tamvani inu Aisraeli! Yehova Mulungu wathu, Yehova ndi mmodzi! 30 Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse ndi mphamvu zako zonse.’ 31 Lachiwiri ndi ili: ‘Konda mnansi wako monga iwe mwini.’ Palibe lamulo lina loposa amenewa.”

32 Munthuyo anayankha kuti, “Mwanena bwino Aphunzitsi. Mwalondola ponena kuti Mulungu ndi mmodzi ndipo palibe wina wofanana naye koma Iye yekha. 33 Kumukonda Iye; ndi mtima wako wonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mphamvu zako zonse, ndi kukonda mnansi wako monga iwe mwini, ndi zopambana kuposa zopereka ndi nsembe zopsereza.”

34 Yesu ataona kuti wayankha mwanzeru, anati kwa iye, “Iwe suli kutali ndi ufumu wa Mulungu.” Ndipo kuyambira pamenepo panalibe ndi mmodzi yemwe anayesa kumufunsanso.

Khristu ndi Mwana wa Yani?

35 Yesu akuphunzitsa mʼmabwalo a Nyumba ya Mulungu, anafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani aphunzitsi amalamulo amanena kuti, ‘Khristu ndi Mwana wa Davide?’ 36 Pajatu Davide mwini wake, poyankhula mwa Mzimu Woyera, ananena kuti,

“Ambuye anati kwa Ambuye anga:
    ‘Khalani pa dzanja langa lamanja
kufikira nditayika adani anu
    pansi pa mapazi anu.’

37 Davide mwini wake amutchula Iye, ‘Ambuye.’ Nanga angakhale bwanji mwana wake?”

Gulu lalikulu la anthu linamvetsera ndi chisangalalo.

Yesu Achenjeza Anthu za Aphunzitsi a Malamulo

38 Pamene ankaphunzitsa, Yesu anati, “Samalani ndi aphunzitsi a malamulo. Amakonda kuyendayenda atavala mikanjo ikuluikulu ndi kumalonjeredwa mʼmisika. 39 Ndipo amakhala pa mipando yofunika kwambiri mʼmasunagoge ndi malo aulemu pa maphwando. 40 Amawononga chuma cha akazi amasiye ndiponso amapemphera mapemphero aatali odzionetsera. Anthu oterewa adzalangidwa kwambiri.”

Chopereka cha Mayi Wamasiye

41 Yesu anakhala pansi moyangʼanana ndi pamene amaperekera zopereka ndipo amaona anthu akupereka ndalama zawo mʼthumba la Nyumba ya Mulungu. Anthu ambiri olemera anaponya ndalama zambiri. 42 Koma mkazi wamasiye, wosauka anabwera ndi kuyikamo tindalama tiwiri ta kopala, tongokwanira theka la ndalama.

43 Yesu anayitana ophunzira ake nati, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti mayi wosauka wamasiyeyu waponya zambiri mʼthumbali kuposa ena onsewa. 44 Iwo apereka molingana ndi chuma chawo; koma iye, mwaumphawi wake, wapereka zonse anali nazo ngakhale zoti akanagulira chakudya.”

Yobu 8

Mawu a Bilidadi

Pamenepo Bilidadi wa ku Suki anayankha kuti,

“Kodi udzakhala ukuyankhula zoterezi mpaka liti?
    Mawu ako ali ngati mphepo yamkuntho.
Kodi Mulungu amapotoza chiweruzo cholungama?
    Kodi Wamphamvuzonse amalephera kuchita zachilungamo?
Pamene ana ako anamuchimwira Mulungu,
    Iye anawapereka kuti alangidwe chifukwa cha tchimo lawo.
Koma utayangʼana kwa Mulungu,
    ndi kudandaulira Wamphamvuzonse,
ngati uli wangwiro ndi wolungama mtima
    ngakhale tsopano Iye adzachitapo kanthu mʼmalo mwako
    ndipo adzakubwezeretsa pa malo ako oyenera.
Chiyambi chako chidzaoneka ngati chochepa
    koma chimaliziro chako chidzakhala chopambana.

“Funsa kwa anthu amvulazakale
    ndipo upeze zimene makolo awo anaziphunzira
pakuti ife ndife ana adzulodzuloli ndipo sitidziwa chilichonse,
    ndipo moyo wathu pa dziko lapansi uli ngati chithunzithunzi.
10 Kodi iwo sadzakulangiza ndi kukufotokozera?
    Kodi sadzakuwuza mawu ochokera pa zimene amazidziwa?
11 Kodi bango nʼkumera pa nthaka yopanda chinyontho?
    Nanga mawango nʼkukula bwino popanda madzi?
12 Popanda madzi, zimenezi zimafota zikanali zaziwisi ndi zosadula;
    zimawuma msangamsanga kuposa bango.
13 Ndimo mmene amachitira anthu onse amene amayiwala Mulungu;
    ndi mmene chiyembekezo cha munthu wosapembedza Mulungu chimathera.
14 Kulimba mtima kwake kumafowoka;
    zimene iye amadalira zili ngati ukonde wa kangawude.
15 Iye amatsamira ukonde wake, koma umaduka;
    amawugwiritsitsa koma sulimba.
16 Munthu woyipayo ali ngati chomera chothiriridwa bwino chimene chili pa dzuwa,
    nthambi zake zimatambalala pa munda wake;
17 mizu yake imayanga pa mulu wa miyala
    ndi kufunafuna malo woti izikike pa miyalapo.
18 Koma pamene yachotsedwa pamalo pakepo,
    pamalopo pamakana chomeracho ndi kuti, ‘Ine sindinakuonepo.’
19 Ndithudi chomeracho chimafota,
    ndipo pa nthakapo pamatuluka zomera zina.

20 “Ndithudi, Mulungu sakana munthu amene alibe cholakwa
    kapena kulimbikitsa anthu ochita zoyipa.
21 Iye adzadzaza mʼkamwa mwako ndi phwete
    ndipo milomo yako idzafuwula ndi chimwemwe.
22 Adani ako adzachita manyazi,
    ndipo malo okhalamo anthu oyipa sadzaonekanso.”

Aroma 12

Nsembe za Moyo

12 Nʼchifukwa chake ine ndikukupemphani abale, mwa chifundo cha Mulungu, kuti mupereke matupi anu monga nsembe yamoyo, yopatulika ndi yokondweretsa Mulungu. Nsembeyi ndiye kupembedza kwanu kwa uzimu. Musafanizidwenso ndi makhalidwe a dziko lino koma musandulike pokonzanso maganizo anu. Ndipo mudzadziwa ndi kuzindikira chifuniro chabwino cha Mulungu chomwe ndi chokondweretsa ndi changwiro.

Chifukwa cha chisomo chopatsidwa kwa ine, ndinena kwa aliyense wa inu kuti musadziyenereze nokha kuposa mmene mulili. Koma mudziganizire nokha modzichepetsa, molingana ndi muyeso wa chikhulupiriro chimene Mulungu wakupatsani. Pakuti monga aliyense wa ife ali ndi thupi limodzi koma ziwalo zambiri, ziwalozi sizili ndi ntchito yofanana. Momwemonso mwa Khristu ife amene tili ambiri tipanga thupi limodzi ndipo chiwalo chilichonse ndi cholumikizika ku chinzake. Ife tili ndi mphatso zosiyana, molingana ndi chisomo chopatsidwa kwa ife. Ngati mphatso ya munthu ndi kunenera, musiyeni ayigwiritse ntchito molingana ndi chikhulupiriro chake. Ngati ndi kutumikira, musiyeni atumikire. Ngati ndi kuphunzitsa, musiyeni aphunzitse. Ngati ndi kulimbikitsa, musiyeni alimbikitse. Ngati ndi kupereka kuthandiza osowa, musiyeni apereke mowolowamanja. Ngati ndi utsogoleri, musiyeni alamulire mosamala. Ngati ndi kuonetsa chifundo, musiyeni achite mosangalala.

Chikondi

Chikondi chikhale chopanda chinyengo. Dana nacho choyipa; gwiritsitsa chabwino. 10 Mukondane kwathunthu monga abale. Lemekezanani wina ndi mnzake kuposa inu eni. 11 Musakhale aulesi mʼmachitidwe anu. Khalani achangu mu mzimu ndipo tumikirani Ambuye. 12 Kondwerani mʼchiyembekezo, pirirani mʼmasautso ndiponso khulupirikani mʼpemphero. 13 Gawanani ndi anthu a Mulungu amene ali ndi chosowa. Cherezani alendo.

14 Adalitseni amene akuzunzani. Adalitseni ndipo musawatemberere. 15 Kondwani pamodzi ndi amene akukondwa ndipo lirani ndi amene akulira. 16 Muyanjane wina ndi mnzake. Musakhale onyada, koma lolani kuyanjana ndi anthu wamba. Musaganize kuti mumadziwa zonse.

17 Musabwezere choyipa ndi choyipa kwa aliyense. Samalitsani kuchita chabwino pamaso pa aliyense. 18 Ngati nʼkotheka, khalani mwamtendere ndi aliyense monga momwe mungathere. 19 Okondedwa anga, musabwezere choyipa, koma lekerani Mulungu. Pakuti kwalembedwa, “Kubwezera chilango nʼkwanga. Ndidzawalanga ndine,” akutero Ambuye. 20 Koma,

“Ngati mdani wako ali ndi njala, mupatse chakudya.
    Ngati ali ndi ludzu, mupatse kanthu kakumwa.
Pochita ichi, udzamuwunjikira makala amoto pamutu pake.”

21 Musagonjetsedwe ndi choyipa, koma gonjetsani choyipa pochita chabwino.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.