Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
9 Kenaka Yehova anati kwa Yoswa, “Kuyambira tsopano anthu a ku Igupto sadzakunyozaninso.” Nʼchifukwa chake malowa anatchedwa Giligala mpaka lero.
10 Akupumulabe ku Giligala kuja mʼchigwa cha Yeriko, Aisraeli anachita chikondwerero cha Paska madzulo pa tsiku la 14 la mwezi woyamba womwewo. 11 Mmawa mwake ndi pamene anayamba kudya zakudya za mʼdziko la Kanaani. Anaphika buledi wopanda yisiti ndi kukazinga tirigu tsiku lomwelo. 12 Atangodya chakudya cha mʼdzikomo, mana anasiya kugwa, ndipo sanapezekenso. Kuyambira nthawi imeneyo Aisraeli anayamba kudya chakudya cha mʼdziko la Kanaani.
Salimo la Davide. Malangizo.
32 Ngodala munthu
amene zolakwa zake zakhululukidwa;
amene machimo ake aphimbidwa.
2 Ngodala munthu
amene machimo ake Yehova sawawerengeranso pa iye
ndipo mu mzimu mwake mulibe chinyengo.
3 Pamene ndinali chete,
mafupa anga anakalamba
chifukwa cha kubuwula kwanga tsiku lonse.
4 Pakuti usana ndi usiku
dzanja lanu linandipsinja;
mphamvu zanga zinatha
monga nthawi yotentha yachilimwe.
Sela
5 Kotero ine ndinavomereza tchimo langa kwa Inu,
sindinabise mphulupulu zanga.
Ndinati, “Ine ndidzawulula
zolakwa zanga kwa Yehova,
ndipo Inu munandikhululukira
mlandu wa machimo anga.”
Sela
6 Choncho aliyense okhulupirika apemphere kwa Inuyo
pomwe mukupezeka;
ndithu pamene madzi amphamvu auka,
sadzamupeza.
7 Inu ndi malo anga obisala;
muzinditeteza ku mavuto ndipo muzindizinga
ndi nyimbo zachipulumutso.
Sela
8 Ndidzakulangiza ndi kukuphunzitsa njira imene udzayendamo;
ndidzakupatsa uphungu ndi kukuyangʼanira.
9 Usakhale ngati kavalo kapena bulu,
zimene zilibe nzeru,
koma ziyenera kuwongoleredwa ndi zitsulo za mʼkamwa ndi pamutu,
ukapanda kutero sizibwera kwa iwe.
10 Zowawa ndi zambiri za anthu oyipa
koma chikondi chosatha cha Yehova
chimamuzinga munthu amene amadalira Iye.
11 Kondwerani mwa Yehova inu olungama;
imbani, inu nonse amene muli owongoka mtima!
16 Choncho, kuyambira tsopano mpaka mʼtsogolo ife sitiganizirapo za munthu aliyense monga mwanzeru za umunthu, ngakhale kuti poyamba tinkaganiza za Khristu mʼnjira imeneyi, koma tsopano sititeronso. 17 Nʼchifukwa chake, ngati munthu aliyense ali mwa Khristu, ndi wolengedwa kwatsopano; zinthu zakale zapita taonani, zakhala zatsopano. 18 Zonsezi zichokera kwa Mulungu amene anatiyanjanitsa ndi Iye mwini kudzera mwa Khristu ndipo anatipatsa ife utumiki wa chiyanjanitso. 19 Mulungu ankayanjanitsa dziko lapansi kwa Iye mwini kudzera mwa Khristu, osawerengera anthu monga mwa zochimwa zawo. Ndipo watisungitsa ife uthenga uwu wa chiyanjanitso. 20 Choncho ife ndi akazembe a Khristu, monga ngati Mulungu akudandaulira anthu kudzera mwa ife. Ife tikukupemphani inu mʼmalo mwa Khristu kuti, yanjanitsidwani ndi Mulungu. 21 Chifukwa cha ife, Mulungu anasandutsa wopanda tchimoyo kukhala tchimo, kuti mwa Iye ife tikakhale chilungamo cha Mulungu.
Fanizo la Nkhosa Yotayika
15 Tsopano amisonkho ndi “ochimwa” ankasonkhana kudzamvera mawu ake. 2 Koma Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo amangʼungʼudza nati, “Munthu uyu amalandira ochimwa ndi kudya nawo.”
3 Ndipo Yesu anawawuza fanizo ili:
Fanizo la Mwana Wolowerera
11 Yesu anapitiriza kunena kuti, “Panali munthu amene anali ndi ana aamuna awiri. 12 Wamngʼonoyo anati kwa abambo ake, ‘Abambo, patseni gawo langa la chuma chanu.’ Ndipo iye anawagawira awiriwo chuma chawo.
13 “Pasanapite nthawi, wamngʼonoyo anasonkhanitsa chuma chake chonse, napita ku dziko lakutali ndipo kumeneko anayamba kumwaza chuma chake mʼnjira zachitayiko. 14 Iye atawononga zonse, kunagwa njala yoopsa mʼdziko lonselo ndipo anayamba kusauka. 15 Iye anapita kwa nzika ina ya dzikolo nakakhala naye ndi kumagwira ntchito, amene anamutumiza ku munda kukadyetsa nkhumba. 16 Iye analakalaka atakhutitsa mimba yake ndi makoko amene nkhumbazo zinkadya, koma panalibe wina amene anamupatsa kanthu.
17 “Maganizo ake atabweramo, iye anati, ‘Ndi antchito angati a abambo anga amene ali ndi chakudya chimene amadya nʼkutsalako ndipo ine ndili pano kufa ndi njala! 18 Ine ndinyamuka ndi kubwerera kwa abambo anga ndipo ndikati kwa iwo: abambo, ine ndachimwira kumwamba ndi kwa inu. 19 Ndine wosayeneranso kutchedwa mwana wanu; munditenge ngati mmodzi wa antchito anu.’ 20 Ndipo iye ananyamuka ndi kupita kwa abambo ake.
“Koma iye akanali patali, abambo ake anamuona ndipo anamvera chisoni; anathamangira mwanayo, namukumbatira ndi kupsompsona.
21 “Mwanayo anati, ‘Abambo, ine ndachimwira kumwamba ndi inunso. Ine sindiyenera konse kutchedwa mwana wanu.’
22 “Koma abambowo anati kwa antchito ake, ‘Fulumirani! Bweretsani mkanjo wabwino kwambiri ndipo mumuveke. Muvekeni mphete ndi nsapato. 23 Bweretsani mwana wangʼombe wonenepa ndipo iphani. Tiyeni tikhale ndi phwando ndi kukondwerera. 24 Pakuti mwana wangayu anali wakufa, ndipo ali ndi moyonso; iye anatayika ndipo wapezeka.’ Chomwecho anayamba kukondwerera.
25 “Nthawi imeneyi, mwana wake wamkulu uja anali ku munda. Iye atafika pafupi ndi nyumba, anamva anthu akuyimba ndi kuvina. 26 Ndipo iye anayitana mmodzi wa antchito, namufunsa chimene chimachitika. 27 Iye anayankha kuti, ‘Mʼbale wako wabwera ndipo abambo ako apha mwana wangʼombe wonenepa chifukwa wabwera wamoyo ndipo ali bwino.’
28 “Mwana wamkulu anakwiya ndipo anakana kulowa. Chomwecho abambo ake anatuluka ndi kumudandaulira. 29 Koma iye anayankha abambo ake kuti, ‘Taonani! Zaka zonsezi ndakhala ndikukutumikirani kugwira ntchito yowawa ndipo palibe pamene sindinamvere malamulo anu. Koma inu simunandipatse ngakhale mwana wambuzi kuti ine ndichite phwando ndi anzanga. 30 Koma pamene mwana wanu uyu amene wawononga chuma chanu ndi achiwerewere wabwera ku nyumba, inu mwamuphera mwana wangʼombe wonenepa.’ ”
31 Abambowo anati, “Mwana wanga, iwe umakhala ndi ine nthawi zonse ndipo zonse ndili nazo ndi zako. 32 Koma tinayenera kukondwera ndi kusangalala, chifukwa mʼbale wako uyu anali wakufa ndipo ali ndi moyonso; iye anali wotayika ndipo wapezeka.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.