Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 17

Pemphero la Davide.

17 Imvani Inu Yehova pempho langa lachilungamo;
    mverani kulira kwanga.
Tcherani khutu kuti mumve pemphero langa
    popeza silikuchokera pakamwa pachinyengo.
Kusalakwa kwanga kuchokera kwa inu;
    maso anu aone chimene ndi cholungama.

Ngakhale Inu mutafufuza mtima wanga ndi kundisanthula usiku,
    ngakhale mutandiyesa, simudzapeza kanthu;
    Ine ndatsimikiza kuti pakamwa panga sipadzachimwa.
Kunena za ntchito za anthu,
    monga mwa mawu a pakamwa panu,
Ine ndadzisunga ndekha
    posatsata njira zachiwawa.
Mayendedwe anga akhazikika pa njira zanu;
    mapazi anga sanaterereke.

Ine ndikuyitana Inu, Mulungu wanga, pakuti mudzandiyankha;
    tcherani khutu lanu kwa ine ndipo mumve pemphero langa.
Onetsani kudabwitsa kwa chikondi chanu chachikulu,
    Inu amene mumapulumutsa ndi dzanja lanu lamanja
    iwo amene amathawira kwa inu kuchoka kwa adani awo.
Mundisunge ine ngati mwanadiso;
    mundibise mu mthunzi wa mapiko anu,
kuchoka kwa oyipa amene amandizinga ine,
    kuchoka kwa anthu amene ndi adani anga, amene andizungulira ine.

10 Iwo amatseka mitima yawo yopanda chifundo,
    ndi pakamwa pawo amayankhula modzitamandira.
11 Andisaka, tsopano andizungulira
    ndi maso awo atcheru, kuti andigwetse pansi.
12 Iwo ali ngati mkango wofuna nyama;
    ngati mkango waukulu wokhala mobisala.

13 Dzukani Yehova, mulimbane nawo ndipo muwagwetse pansi;
    landitseni kuchoka kwa oyipa ndi lupanga lanu.
14 Inu Yehova, pulumutseni ndi dzanja lanu kwa anthu otere,
    kwa anthu a dziko lino amene mphotho yawo ili mʼmoyo uno.

Inu mumaletsa njala kwa amene asangalatsidwa nanu;
    ana awo aamuna ali ndi zinthu zambiri,
    ndipo iwo amasunga chuma cha ana awo.
15 Ndipo ine mʼchilungamo ndidzaona nkhope yanu;
    pamene ndidzadzuka, ndidzakondwera kwambiri poonana nanu.

1 Mbiri 21:1-17

Davide Awerenga Ankhondo Ake

21 Satana anafuna kuvutitsa Aisraeli choncho anawutsa mtima wa Davide kuti awerenge Aisraeli. Choncho Davide anati kwa Yowabu pamodzi ndi atsogoleri a ankhondo, “Pitani mukawerenge Aisraeli kuyambira ku Beeriseba mpaka ku Dani. Ndipo mudzandiwuze kuti ndidziwe chiwerengero chawo.”

Yowabu anayankha kuti, “Yehova achulukitse ankhondo ake kukhala miyandamiyanda. Mbuye wanga mfumu, kodi anthu onsewa sali pansi panu? Nʼchifukwa chiyani mbuye wanga mukufuna kuchita zimenezi? Nʼchifukwa chiyani mukufuna kuchimwitsa Israeli?”

Komabe mawu a mfumu anapambana mawu a Yowabu, kotero Yowabu anapita mu Israeli monse ndipo kenaka anabwera ku Yerusalemu. Yowabu anapereka chiwerengero cha anthu ankhondo kwa Davide: Mu Israeli monse munali anthu ankhondo 1,100,000 amene amadziwa kugwiritsa ntchito lupanga, kuphatikizapo anthu 470,000 a fuko la Yuda.

Koma Yowabu sanaphatikizepo fuko la Levi ndi fuko la Benjamini pa chiwerengerochi, pakuti lamulo la mfumu linamuyipira. Lamulo limeneli silinakomerenso Mulungu. Kotero Iye analanga Israeli.

Choncho Davide anati kwa Mulungu, “Ine ndachimwa kwambiri pa zimene ndachita. Tsono ndikupempha kuti mukhululuke kulakwa kwa mtumiki wanu. Ine ndachita zopusa kwambiri.”

Yehova anati kwa Gadi, mlosi wa Davide, 10 “Pita ukamuwuze Davide kuti, ‘Yehova akuti, Ine ndikukupatsa zinthu zitatu izi. Usankhepo chimodzi pa zimenezi choti ndikuchitire.’ ”

11 Choncho Gadi anapita kwa Davide ndipo anati kwa Iye, “Yehova akuti, ‘Musankhepo chimene mungakonde kuti chichitike: 12 mʼdziko mukhale njala zaka zitatu, mukhale mukuthawa adani anu kwa miyezi itatu, akukukanthani ndi lupanga la Yehova, kapena mʼdziko mukhale mliri kwa masiku atatu, mngelo wa Yehova akuwononga Israeli yense.’ Ndipo tsono ganizirani bwino chomwe ndikamuyankhe amene wandituma.”

13 Davide anati kwa Gadi, “Ine ndavutika kwambiri mu mtima mwanga. Ine andilange ndi Yehova, pakuti chifundo chake ndi chachikulu kwambiri; koma ndisalangidwe ndi anthu.”

14 Choncho Yehova anabweretsa mliri pa Aisraeli, ndipo unapha Aisraeli 70,000. 15 Ndipo Mulungu anatumiza mngelo kuti awononge Yerusalemu. Koma pamene mngeloyo amachita zimenezi, Yehova anaona ndipo anavutika mu mtima chifukwa cha zowawazo ndipo anati kwa mngelo amene ankawononga anthu uja, “Basi kwakwanira! Leka kuwononga.” Nthawi imeneyo mngelo wa Yehova anali atayima pamalo opunthira tirigu a Arauna Myebusi.

16 Davide anakweza maso ake ndipo anaona mngelo wa Yehova atayima pakati pa dziko lapansi ndi kumwamba, mʼdzanja lake muli lupanga lotambalitsa kuloza ku Yerusalemu. Ndipo Davide ndi akuluakulu, atavala ziguduli, anadzigwetsa pansi chafufumimba.

17 Davide anati kwa Mulungu, “Kodi si ine amene ndinalamula kuti ankhondo awerengedwe? Ine mʼbusa ndi amene ndachimwa, ndiye ndachita zoyipa. Anthuwa ali ngati nkhosa zosalakwa. Kodi iwowa achita chiyani? Inu Yehova Mulungu wanga, langani ineyo pamodzi ndi banja langa, koma musalole kuti mliriwu ukhale pa anthu anuwa.”

1 Yohane 2:1-6

Inu Ana anga okondedwa, ndikukulemberani zimenezi kuti musachimwe. Koma wina akachimwa, tili nayo Nkhoswe yotinenera kwa Atate, Yesu Khristu, Wolungamayo. Iyeyo ndiye nsembe yopepesera machimo athu, ndipo osati athu okha, komanso machimo onse a dziko lapansi.

Chikondi ndi Chidani

Ife timatsimikiza kuti tikumudziwa ngati tikusunga malamulo ake. Munthu akamanena kuti, “Ine ndimadziwa Mulungu,” koma samvera malamulo a Mulunguyo, ndi wabodza ameneyo ndipo mwa iye mulibe choonadi. Koma munthu aliyense akamvera mawu ake, ndiye kuti chikondi cha Mulungu chafikadi penipeni mwa iyeyo. Pamenepo timatsimikizadi kuti tili mwa Iye. Aliyense amene amati amakhala mwa Mulungu, ayenera kukhala moyo umene Yesu ankakhala.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.