Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 23

Salimo la Davide.

23 Yehova ndiye mʼbusa wanga, sindidzasowa kanthu.
    Amandigoneka pa msipu wobiriwira,
amanditsogolera ku madzi akumwa abwino,
    amatsitsimutsa moyo wanga.
Amanditsogolera mʼnjira zachilungamo
    chifukwa cha dzina lake.
Ngakhale ndiyende
    mʼchigwa cha mdima wakuda bii,
sindidzaopa choyipa,
    pakuti Inu muli ndi ine;
chibonga chanu ndi ndodo yanu
    zimanditonthoza.

Mumandikonzera chakudya
    adani anga akuona.
Mumadzoza mutu wanga ndi mafuta;
    chikho changa chimasefukira.
Zoonadi, zokoma ndi chikondi chosasinthika zidzanditsata
    masiku onse a moyo wanga,
ndipo ndidzakhala mʼNyumba ya Yehova
    kwamuyaya.

Eksodo 3:16-22

16 “Pita, ukawasonkhanitse akuluakulu a Israeli ndipo ukati kwa iwo, ‘Yehova, Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abrahamu, Isake ndi Yakobo, anandionekera ndipo akuti Iye wadzakuyenderani ndipo waona mmene Aigupto akukuzunzirani. 17 Choncho wanenetsa kuti adzakutulutsani mʼdziko la Igupto, dziko la masautsoli kupita ku dziko la Akanaani, Ahiti, Aamori Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi, dziko loyenda mkaka ndi uchi.’

18 “Akuluakulu a Israeli akakumvera. Kenaka iwe ndi akuluakuluwo mukapite kwa mfumu ya Igupto ndipo mukanene kuti, ‘Yehova, Mulungu wa Ahebri, wakumana nafe. Tsono tikukupemphani kuti mutilole tipite pa ulendo wa masiku atatu mʼchipululu kuti tikapereke nsembe kwa Yehova Mulungu wathu.’ 19 Koma Ine ndikudziwa kuti mfumu ya Igupto sikakulolani kuti mupite pokhapokha Ine nditayikakamiza. 20 Tsono Ine ndidzatambasula dzanja langa ndi kukantha Aigupto ndi zodabwitsa zanga zimene ndidzazichita pakati pawo. Zikadzatha izi, Iye adzakulolani kuti mupite.

21 “Ndipo ine ndidzafewetsa mtima wa Aigupto pa anthu anga, kotero kuti mukadzatuluka simudzapita wopanda kanthu. 22 Mkazi aliyense adzapemphe Mwigupto woyandikana naye ndiponso mkazi amene akukhala mʼnyumba yake, kuti amupatse ziwiya za siliva ndi golide ndiponso zovala zimene mudzaveka ana anu aamuna ndi aakazi. Ndipo potero mudzawalanda zonse Aiguptowo.”

Eksodo 4:18-20

Mose Abwerera ku Igupto

18 Tsono Mose anabwerera kwa Yetero, mpongozi wake ndipo anati kwa Iye, “Chonde ndiloleni kuti ndibwerere ku Igupto kwa anthu anga kuti ndikaone ngati ali moyo.”

Yeteri anati, “Pitani mu mtendere.”

19 Nthawiyi Yehova anali atamuwuza kale Mose ku Midiyani kuti, “Bwerera ku Igupto, pakuti anthu onse amene amafuna kukupha aja anamwalira.” 20 Kotero Mose anatenga mkazi wake ndi ana ake aamuna, ndipo anawakweza pa bulu nayamba ulendo wobwerera ku Igupto. Ndipo anatenga ndodo ya Mulungu ija mʼdzanja lake.

1 Petro 2:13-17

Kugonjera Olamulira

13 Gonjerani maulamuliro onse chifukwa cha Ambuye. Kaya ndi mfumu, imvereni chifukwa ili ndi ulamuliro waukulu, 14 kaya ndi mabwanamkubwa, pakuti watumidwa ndi mfumu kuti alange onse amene amachita zoyipa ndi kuyamikira onse amene amachita zabwino. 15 Pakuti Mulungu akufuna kuti pochita ntchito zabwino muthetse kuyankhula mosazindikira ndi mopusa. 16 Mukhale monga mfulu, koma musagwiritse ntchito ufulu wanuwo ngati chophimbira zoyipa; mukhale monga atumiki a Mulungu. 17 Chitirani ulemu aliyense, kondani abale okhulupirira, wopani Mulungu, ndipo chitirani mfumu ulemu.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.