Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 118:1-2

118 Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino;
    pakuti chikondi chake chosasinthika ndi chosatha.

Israeli anene kuti:
    “Chikondi chake ndi chosatha.”

Masalimo 118:14-24

14 Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga;
    Iye wakhala chipulumutso changa.

15 Mfuwu wachimwemwe ndi chipambano
    ukumveka mʼmatenti a anthu olungama mtima kuti:
“Dzanja lamanja la Yehova lachita zamphamvu!
16     Dzanja lamanja la Yehova latukulidwa mmwamba
    Dzanja lamanja la Yehova lachita zamphamvu!”

17 Sindidzafa koma ndidzakhala ndi moyo
    ndipo ndidzalalika za ntchito ya Yehova.
18 Yehova wandilanga koopsa,
    koma sanandipereke ku imfa.

19 Tsekulireni zipata zachilungamo,
    kuti ndifike kudzayamika Yehova.
20 Ichi ndicho chipata cha Yehova
    chimene olungama mtima okha adzalowerapo.
21 Ndidzakuyamikani chifukwa Inu munandiyankha;
    mwakhala chipulumutso changa.

22 Mwala umene amisiri omanga nyumba anawukana
    wasanduka wapangodya;
23 Yehova ndiye wachita zimenezi
    ndipo nʼzodabwitsa pamaso pathu.
24 Lero ndiye tsiku limene Yehova walipanga;
    tiyeni tikondwere ndi kusangalala nalo.

Eksodo 15:1-18

Nyimbo ya Mose ndi Miriamu

15 Ndipo Mose ndi Aisraeli anayimbira Yehova nyimbo iyi:

“Ine ndidzayimbira Yehova
    pakuti wakwezeka mʼchigonjetso.
Kavalo ndi wokwera wake,
    Iye wawaponya mʼnyanja.
Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga;
    ndiye chipulumutso changa.
Iye ndiye Mulungu wanga, ndipo ndidzamutamanda,
    Mulungu wa makolo anga, ine ndidzamukweza.
Yehova ndi wankhondo;
    Yehova ndilo dzina lake.
Magaleta a Farao ndi asilikali ake ankhondo
    Iye wawaponya mʼnyanja.
Akatswiri ankhondo amphamvu a Farao
    amizidwa mʼNyanja Yofiira.
Nyanja yakuya inawaphimba;
    Iwo anamira pansi ngati mwala.”

Yehova, dzanja lanu lamanja
    ndi laulemerero chifukwa cha mphamvu zake.
Ndithu Yehova, dzanja lanu lamanja
    linaphwanya mdani.
Ndi ulemerero wanu waukulu,
    munagonjetsa okutsutsani.
Inu munatumiza mkwiyo wanu waukulu;
    ndipo unawapsereza ngati udzu.
Ndi mpweya wotuluka mʼmphuno mwanu
    madzi anawunjikana pamodzi.
Nyanja yakuya ija inasanduka
    madzi owuma gwaa kufika pansi.

Mdaniyo anati,
    “Ine ndidzawalondola, ndipo ndidzawagwira.
Ndidzagawa chuma chawo;
    ndiye chokhumba changa chidzakwaniritsidwa.
Ine ndidzasolola lupanga langa,
    ndi mkono wanga ndidzawawononga.”
10 Koma Inu munawuzira mphepo yanu,
    ndipo nyanja inawaphimba.
Iwo anamira ngati chitsulo
    mʼmadzi amphamvu.

11 Ndithu Yehova, pakati pa milungu,
    ndani afanana nanu? Inu amene muli woyera,
        ndiponso wotamandika wolemekezeka,
        chifukwa cha ntchito zanu,
        zazikulu ndi zodabwitsa?
12 Munatambasula dzanja lanu lamanja
    ndipo dziko linawameza.

13 Ndi chikondi chanu chosasinthika mudzatsogolera
    anthu amene munawawombola.
Ndi mphamvu zanu munawatsogolera
    ku malo anu woyera.
14 Anthu amitundu ina anamva za mbiriyi ndipo ananjenjemera ndi mantha,
    mantha woopsa agwira anthu a dziko la Filisiti.
15 Tsopano mafumu a ku Edomu agwidwa ndi mantha aakulu,
    otsogolera a dziko la Mowabu akunjenjemera ndi mantha,
ndipo anthu a ku Kanaani asungunuka ndi mantha.
16     Onse agwidwa ndi mantha woopsa.
Popeza anaona mphamvu zanu zazikulu,
    iwo ayima chilili ngati mwala mpaka anthu anu,
Inu Yehova atadutsa;
    inde mpaka atadutsa anthu amene munawagula.
17 Inu mudzawalowetsa ndi kuwakhazikitsa
    pa phiri lanu.
Pa malo pamene Inu Yehova munawapanga kuti muzikhalapo;
    malo wopatulika amene Inu Ambuye munawakonza ndi manja anu.
18 “Yehova adzalamula
    mpaka muyaya.”

Akolose 3:12-17

12 Choncho, ngati anthu osankhidwa ndi Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa kwambiri, muvale chifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, kufatsa ndi kupirira. 13 Mulezerane mtima ndipo muzikhululukirana ngati wina ali ndi chifukwa ndi mnzake. Muzikhululukirana monga Ambuye anakhululukira inu. 14 Ndipo kuwonjezera pa zonsezi valani chikondi, chimene chimangirira zonsezi pamodzi mu mgwirizano wangwiro.

15 Mtendere wa Khristu ulamulire mʼmitima mwanu, popeza monga ziwalo za thupi limodzi, munayitanidwa kuti mukhale ndi mtendere. Ndipo muziyamika. 16 Mawu a Khristu akhazikike kwathunthu mʼmitima mwanu. Muziphunzitsana ndi kulangizana wina ndi mnzake ndi nzeru zonse pamene mukuyimba Masalimo, nyimbo zotamanda ndi nyimbo zauzimu, kuyimbira Mulungu ndi mitima yoyamika. 17 Ndipo chilichonse chimene mungachite, kaya nʼkuyankhula, kaya nʼkugwira ntchito, muchite zonse mʼdzina la Ambuye Yesu, kuyamika kwa Mulungu Atate kudzera mwa Iye.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.