Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 9:9-20

Yehova ndiye kothawirako kwa opsinjika mtima,
    linga pa nthawi ya mavuto.
10 Iwo amene amadziwa dzina lanu adzadalira Inu,
    pakuti Inu Yehova, simunawatayepo amene amafunafuna inu.

11 Imbani nyimbo zamatamando kwa Yehova, ali pa mpando waufumu mu Ziyoni;
    lengezani pakati pa mitundu ya anthu zimene wachita.
12 Pakuti Iye amene amabwezera chilango akupha anzawo wakumbukira;
    Iye salekerera kulira kwa ozunzika.

13 Inu Yehova, onani momwe adani anga akundizunzira!
    Chitireni chifundo ndipo ndichotseni pa zipata za imfa,
14 kuti ndilengeze za matamando anu
    pa zipata za ana aakazi a Ziyoni,
    kuti pamenepo ndikondwere ndi chipulumutso chanu.
15 Mitundu ya anthu yagwa mʼdzenje limene yakumba;
    mapazi awo akodwa mu ukonde umene anawubisa.
16 Yehova amadziwika ndi chilungamo chake;
    oyipa akodwa ndi ntchito za manja awo.
            Higayoni. Sela
17 Oyipa amabwerera ku manda,
    mitundu yonse imene imayiwala Mulungu.
18 Koma osowa sadzayiwalika nthawi zonse,
    kapena chiyembekezo cha ozunzika kutayika nthawi zonse.

19 Dzukani Inu Yehova, musalole munthu kuti apambane;
    mitundu yonse iweruzidwe pamaso panu.
20 Akantheni ndi mantha aakulu, Inu Yehova;
    mitundu idziwe kuti iwo ndi anthu wamba.
            Sela

1 Samueli 16:14-23

Davide Atumikira Sauli

14 Nthawi imeneyo Mzimu wa Yehova unamuchokera Sauli, ndipo mzimu woyipa wochokera kwa Yehova unayamba kumuzunza.

15 Atumiki a Sauli anati, “Taonani mzimu woyipa wochokera kwa Mulungu ukukuzunzani. 16 Ndiyetu, inu mbuye wathu titumeni ife antchito anu kuti tikafune munthu wodziwa bwino kuyimba zeze. Tsono pamene mzimu woyipa wochokera kwa Mulungu wakufikirani, iye azidzayimba ndipo mudzakhala bwino.”

17 Choncho Sauli anati kwa atumiki ake, “Chabwino, kandipezereni munthu wodziwa bwino kuyimba ndipo mubwere naye kuno.”

18 Mmodzi mwa antchito ake anati, “Ine ndinaona mwana wa Yese wa ku Betelehemu. Ndiye munthu wodziwa bwino kuyimba, wolimba mtima, ngwazi pa nkhondo, wodziwa kuyankhula ndi wokongola. Ndipotu Yehova ali ndi iye.”

19 Ndipo Sauli anatumiza amithenga kwa Yese kukanena kuti, “Nditumizireni mwana wanu Davide, amene amaweta nkhosa.” 20 Choncho Yese anatenga bulu namunyamulitsa buledi, thumba la vinyo ndi mwana wambuzi mmodzi. Zonsezi anamupatsa mwana wake Davide kuti akapereke kwa Sauli.

21 Davide anafika kwa Sauli ndipo anayamba ntchito. Sauli anamukonda kwambiri Davide ndipo anamusandutsa wonyamula zida zake za nkhondo. 22 Kenaka Sauli anatumiza mawu kwa Yese ndi kuti, “Mulole kuti Davide azinditumikira, pakuti ndamukonda kwambiri.”

23 Nthawi zonse mzimu woyipa wochokera kwa Mulungu umati ukamufikira Sauli, Davide ankatenga zeze wake nʼkumamuyimbira. Choncho Sauli ankapeza bwino, ndipo mzimu woyipa uja unkamusiya.

Machitidwe a Atumwi 20:1-16

Paulo Apita ku Makedoniya ndi ku Grisi

20 Litatha phokoso, Paulo anayitanitsa ophunzira ndipo atawalimbikitsa anawatsanzika ndipo ananyamuka kupita ku Makedoniya. Iye anayendera madera a kumeneko, nalimbitsa mtima anthu, ndipo pomaliza pake anapita ku Grisi. Kumeneko anakhala miyezi itatu. Popeza kuti Ayuda anakonza zomuchita chiwembu pamene amati azinyamuka kupita ku Siriya pa sitima ya pamadzi, iye anaganiza zobwereranso kudzera ku Makedoniya. Iye anapita pamodzi ndi Sopatro mwana wa Puro wa ku Bereya, Aristariko ndi Sekundo a ku Tesalonika, Gayo wa ku Derbe ndi Timoteyo, ndipo a ku Asiya anali Tukiko ndi Trofimo. Anthu amenewa anatsogola ndipo anakatidikira ku Trowa. Koma ife tinayenda pa sitima ya pamadzi kuchokera ku Filipi chitatha Chikondwerero cha Buledi wopanda Yisiti. Patapita masiku asanu tinakumana nawo enawo ku Trowa, ndipo tinakhala kumeneko masiku asanu ndi awiri.

Paulo Aukitsa Utiko ku Trowa

Pa tsiku loyamba la Sabata, tinasonkhana kuti tidye mgonero. Paulo analalikira kwa anthu chifukwa anaganiza zoti achoke tsiku linalo, ndipo analalika mpaka pakati pa usiku. Munali nyale zambiri mʼchipinda chammwamba mʼmene tinasonkhanamo. Pa chipinda chachitatu chammwamba cha nyumbayo, pa zenera, panakhala mnyamata wina dzina lake Utiko, amene ankasinza pomwe Paulo amayankhulabe. Atagona tulo, iye anagwa pansi kuchokera pa chipinda chammwamba ndipo anamutola atafa. 10 Paulo anatsika, nadziponya pa mnyamatayo, namukumbatira. Paulo anati, “Musadandaule, ali moyo!” 11 Kenaka Paulo anakweranso, mʼchipinda muja nanyema buledi nadya. Atayankhula mpaka kucha, anachoka. 12 Anthu anatenga mnyamatayo kupita kwawo ali moyo ndipo anatonthozedwa mtima kwambiri.

Paulo Alawirana ndi Akulu Ampingo a ku Efeso

13 Ife tinatsogola kukakwera sitima ya pa madzi kupita ku Aso, kumene tinayembekeza kukatenga Paulo. Iye anakonza motero chifukwa amayenda wapansi. 14 Pamene anakumana nafe ku Aso tinamutenga ndipo tinapita ku Mitilene. 15 Mmawa mwake tinachoka kumeneko pa sitima ya pamadzi ndipo tinafika pafupi ndi Kiyo. Tsiku linalo tinawolokera ku Samo, ndipo tsiku linanso tinafika ku Mileto. 16 Paulo anali atatsimikiza kuti alambalale Efeso kuopa kutaya nthawi ku Asiya, pakuti ankafulumira kuti akafike ku Yerusalemu kuti ngati nʼkotheka kuti tsiku la Pentekosite akakhale ali ku Yerusalemu.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.