Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
34 Ndipo Samueli anapita ku Rama, koma Sauli anapita ku mudzi kwawo ku Gibeya wa Sauli. 35 Samueli sanamuonenso Sauli mpaka imfa yake ngakhale kuti ankamulira Sauliyo. Yehova anamva chisoni kuti anasankha Sauli kuti akhale mfumu ya Israeli.
Samueli Adzoza Davide Kukhala Mfumu
16 Yehova anati kwa Samueli, “Kodi udzamulira Sauli mpaka liti, popeza Ine ndamukana kuti akhale mfumu ya Israeli? Dzaza mafuta mʼbotolo lako ndipo unyamuke kupita kwa Yese wa ku Betelehemu popeza ndadzisankhira mmodzi mwa ana ake kukhala mfumu.”
2 Koma Samueli anati, “Kodi ndingapite bwanji? Sauli akamva zimenezi adzandipha.”
Yehova anayankha, “Tenga ngʼombe yayikazi ndipo ukanene kuti, ‘Ndabwera kudzapereka nsembe kwa Yehova. 3 Ukamuyitane Yese ku mwambo wa nsembe, ndipo ine ndidzakuwuza choti ukachite. Ukandidzozere amene ndikakulozere.’ ”
4 Samueli anachita zimene Yehova ananena, ndipo anabweradi ku Betelehemu kuja. Akuluakulu a mu mzindawo anamuchingamira ali njenjenje ndi mantha ndipo anamufunsa kuti, “Kodi mwabwera mwa mtendere?”
5 Samueli anayankha kuti, “Inde, kwabwino. Ndabwera kudzapereka nsembe kwa Yehova. Mudzipatule ndipo mubwere kudzapereka nsembe pamodzi nane.” Kenaka iye anamupatula Yese ndi ana ake aamuna ndipo anawayitana kudzapereka nsembe.
6 Pamene anafika, Samueli anaona Eliabu ndipo anaganiza “Ndithu wodzozedwa wa Yehova uja ndi uyu wayima pamaso pakeyu.”
7 Koma Yehova anati kwa Samueli, “Usaone maonekedwe ake kapena msinkhu wake, pakuti ndamukana iyeyu. Yehova sapenya zimene munthu amapenya. Anthu amapenya zakunja, koma Mulungu amapenya za mu mtima.”
8 Kenaka Yese anayitana Abinadabu namubweretsa pamaso pa Samueli. Koma Samueli anati, “Yehova sanamusankhenso ameneyu.” 9 Ndipo Yese anayitana Sama, koma Samueli anati, “Ngakhale uyu Yehova sanamusankhe.” 10 Pambuyo pake, Yese anayitana ana ake amuna asanu ndi awiri kuti apite kwa Samueli. Koma Samueli anati, “Yehova sanasankhe amenewa.” 11 Tsono Samueli anafunsa Yese kuti, “Kodi awa ndi ana ako onse aamuna?”
Yese anayankha kuti, “Ayi, alipo wina wamngʼono amene watsala, koma akuweta nkhosa.”
Samueli anati, “Apite munthu akamutenge popeza sitipereka nsembe mpaka iye atabwera.”
12 Choncho anatuma munthu kukamutenga ndipo anabwera naye. Iye anali wofiirira, wa maonekedwe abwino ochititsa kaso.
Ndipo Yehova anati, “Mudzoze popeza ndi ameneyu.”
13 Samueli anatenga botolo la mafuta ndi kumudzoza pamaso pa abale ake, ndipo Mzimu wa Yehova unabwera mwamphamvu pa Davide kuyambira tsiku limenelo mpaka mʼtsogolo. Pambuyo pake Samueli anabwerera ku Rama.
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.
20 Yehova akuyankhe pamene uli pa msautso;
dzina la Mulungu wa Yakobo likuteteze.
2 Iye atumize thandizo kuchokera ku malo ake opatulika;
akugwirizize kuchokera ku Ziyoni.
3 Iye akumbukire nsembe zako zonse
ndipo alandire nsembe zako zopsereza.
Sela
4 Akupatse chokhumba cha mtima wako
ndipo akuthandize kuti zonse wakonza zichitike.
5 Ife tidzafuwula ndi chimwemwe pamene iwe wapambana
ndipo tidzanyamula mbendera zathu mʼdzina la Mulungu wathu,
Yehova ayankhe zopempha zako zonse.
6 Tsopano ndadziwa kuti Yehova amapulumutsa wodzozedwa wake;
Iye amamuyankha kuchokera kumwamba ku malo ake opatulika
ndi mphamvu yopulumutsa ya dzanja lake lamanja.
7 Ena amadalira magaleta ndipo ena akavalo
koma ife tidzadalira dzina la Yehova Mulungu wathu.
8 Iwo amagonjetsedwa ndi kugwa,
koma ife timadzuka ndi kuyima chilili.
9 Inu Yehova, pulumutsani mfumu!
Tiyankheni pamene tikuyitanani!
6 Nʼchifukwa chake nthawi zonse timalimba mtima, ndipo timadziwa kuti pamene tikukhala mʼthupi, ndiye kuti tili kutali ndi Ambuye. 7 Ife timakhala mwachikhulupiriro, osati mwa zooneka ndi maso. 8 Inde, ife tikulimba mtima, ndipo tikanakonda kulekana nalo thupi lathu ndi kukhala ndi Ambuye. 9 Choncho timayesetsa kukondweretsa Ambuye, ngakhale tikhale mʼthupi, kapena tichokemo. 10 Pakuti tonsefe tiyenera kukaonekera pa mpando woweruza wa Khristu, kuti aliyense wa ife akalandire zomuyenera molingana ndi zimene anachita ali mʼthupi; zabwino kapena zoyipa.
Ntchito Yoyanjanitsa
11 Tsono popeza tikudziwa tanthauzo la kuopa Ambuye, ife timayesetsa kukopa anthu. Mulungu amatidziwa bwino lomwe, ndipo tikukhulupirira kuti inunso mumatidziwa bwino mʼmitima mwanu. 12 Sitikudzichitiranso tokha umboni kwa inu, koma tikukupatsani mwayi oti muzitinyadira. Tikufuna kuti muwayankhe amene amanyadira zinthu zooneka ndi maso osati zimene zili mu mtima. 13 Ngati ndife amisala, monga amanenera ena, nʼchifukwa chofuna kuti Mulungu alemekezedwe. Ngati si ife amisala, nʼkuti inu muthandizike.
14 Pakuti chikondi cha Khristu ndicho chimatikakamiza, chifukwa tikutsimikiza kuti mmodzi anafera anthu onse, kotero kuti anthu onse anafanso. 15 Ndipo Iye anafera anthu onse kuti amene ali ndi moyo, asakhale ndi moyo wofuna kudzikondweretsa okha, koma azikondweretsa amene anawafera naukitsidwa chifukwa cha iwowo.
16 Choncho, kuyambira tsopano mpaka mʼtsogolo ife sitiganizirapo za munthu aliyense monga mwanzeru za umunthu, ngakhale kuti poyamba tinkaganiza za Khristu mʼnjira imeneyi, koma tsopano sititeronso. 17 Nʼchifukwa chake, ngati munthu aliyense ali mwa Khristu, ndi wolengedwa kwatsopano; zinthu zakale zapita taonani, zakhala zatsopano.
Fanizo la Mbewu Imene Ikukula
26 Iye anatinso, “Umu ndi mmene ulili ufumu wa Mulungu. Munthu amafesa mbewu mʼnthaka. 27 Usiku ndi usana, kaya agona kapena adzuka, mbewu imamera ndi kukula, ngakhale sadziwa mmene zimachitikira. 28 Nthaka pa yokha imatulutsa mbewu, umayamba mʼmera, kenaka ngala, kenaka mbewu yokhwima mʼngalayo. 29 Mbewuyo ikangokhwima, amayimweta chifukwa nthawi yokolola yakwana.”
Fanizo la Mbewu ya Mpiru
30 Ndipo anatinso, “Kodi tinene kuti ufumu wa Mulungu ufanana ndi chiyani, kapena ndi fanizo lotani limene tidzagwiritsa ntchito pakuwufotokozera? 31 Uli ngati mbewu ya mpiru imene ndi mbewu yayingʼono kwambiri yomwe mumadzala mʼnthaka. 32 Koma ikadzalidwa, imakula ndi kukhala yayikulu koposa mbewu zina zonse za mʼmunda ndipo mʼnthambi zake zazikulu mbalame zamlengalenga zimadzapuma pa mthunzi wake.”
33 Ndi mafanizo ambiri onga awa Yesu anayankhula mawu kwa iwo, monga mmene akanatha kumvetsa. 34 Iye sananene kanthu kwa iwo osagwiritsa ntchito fanizo. Koma ali yekha ndi ophunzira ake, ankawatanthauzira zonse.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.