Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 83

Nyimbo. Salimo la Asafu.

83 Inu Mulungu musakhale chete;
    musangoti phee, Mulungu musangoti duu.
Onani adani anu akuchita chiwawa,
    amene amadana nanu autsa mitu yawo.
Mochenjera iwo akukambirana za chiwembu kutsutsana ndi anthu anu;
    Iwo akukonzekera kutsutsana ndi omwe mumawakonda.
Iwo akunena kuti, “Bwerani” akutero, “Tiyeni tiwononge mtundu wonsewu
    kuti dzina la Israeli lisakumbukikenso.”

Ndi mtima umodzi akukonzekera chiwembu;
    Iwo achita mgwirizano kutsutsana nanu:
Matenti a Edomu ndi Aismaeli,
    Mowabu ndi Ahagiri,
Agebala, Aamoni ndi Aamaleki,
    Afilisti, pamodzi ndi anthu a ku Turo.
Ngakhalenso Aasiriya aphatikizana nawo
    kupereka mphamvu kwa ana a Loti.
            Sela

Muwachitire zomwe munachitira Amidiyani,
    monga munachitira Sisera ndi Yabini ku mtsinje wa Kisoni.
10 Amene anawonongedwa ku Endori
    ndi kukhala ngati zinyalala.
11 Anthu awo otchuka muwachite zomwe munachita Orebu ndi Zeebu
    ana a mafumu muwachite zomwe munachita Zeba ndi Zalimuna,
12 amene anati, “Tiyeni tilande dziko
    la msipu la Mulungu.”

13 Muwasandutse fumbi lowuluka, Inu Mulungu wanga,
    ngati mankhusu owuluka ndi mphepo.
14 Monga moto umatentha nkhalango,
    kapena malawi a moto kuyatsa phiri,
15 kotero muwathamangitse ndi mphepo yamkuntho,
    ndi kuwachititsa mantha ndi namondwe.
16 Muphimbe nkhope zawo ndi manyazi
    kuti adzafunefune dzina lanu Yehova.

17 Achite manyazi ndi mantha nthawi zonse;
    awonongeke mwa manyazi.
18 Adziwe kuti Inu amene dzina lanu ndi Yehova,
    ndinu nokha Wammwambamwamba pa dziko lonse lapansi.

Malaki 3:5-12

Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Tsono ndidzakuyandikirani kuti ndikuweruzeni. Mosataya nthawi ndidzanena mawu otsutsa mfiti, achigololo, a umboni wonama, amene salipira bwino antchito awo, amene amazunza akazi ndi ana amasiye, amene saweruza alendo mwachilungamo, komanso amene sandiopa Ine.”

Kuba za Mulungu

“Ine ndine Yehova, ndipo sindisintha. Choncho inu zidzukulu za Yakobo, simunawonongedwe. Kuyambira nthawi ya makolo anu mwakhala mukuphwanya malamulo anga ndipo simunawatsatire. Bwererani kwa Ine, ndipo Ine ndidzabwerera kwa inu,” akutero Yehova Wamphamvuzonse.

“Koma inu mukufunsa kuti, ‘Tibwerere motani kwa Yehova?’

“Kodi munthu angathe kuba za Mulungu? Komatu inu mumandibera.

“Koma inu mukufunsa kuti, ‘Kodi timakuberani motani?’

“Pa zakhumi ndi pa zopereka. Mtundu wanu wonse ndinu otembereredwa, chifukwa mukundibera. 10 Bweretsani chakhumi chathunthu ku nyumba yosungira, kuti mukhale chakudya mʼnyumba mwanga.” Akutero Yehova Wamphamvuzonse, “Tandiyesani, ndipo muone ngati sindidzatsekula zipata zakumwamba, ndi kukugwetserani madalitso ochuluka amene mudzasowe malo owayikamo. 11 Ndidzaletsa tizirombo kuti tisawononge mbewu zanu, ndipo mpesa wa mʼminda mwanu zipatso zake sizidzayoyoka,” akutero Yehova Wamphamvuzonse. 12 “Motero anthu amitundu yonse adzakutchulani odala, pakuti dziko lanu lidzakhala lokondweretsa,” akutero Yehova Wamphamvuzonse.

Marko 2:1-12

Yesu Achiritsa Munthu Wofa Ziwalo

Patapita masiku pangʼono, Yesu atalowanso mu Kaperenawo, zinamveka kuti wabwera ali mʼnyumba. Choncho anthu ambiri anasonkhana kotero kuti panalibenso malo, ngakhale ndi pa khomo pomwe, ndipo Iye anawalalikira mawu. Amuna anayi anabwera, atanyamula munthu wofa ziwalo. Popeza sakanatha kufika naye kwa Yesu chifukwa cha gulu la anthu, anasasula denga chapamwamba pamene panali Yesu, ndipo atabowoleza, anatsitsa mphasa yomwe munthu wofa ziwaloyo anagonapo. Yesu ataona chikhulupiriro chawo, anati kwa wofa ziwaloyo, “Mwana, machimo ako akhululukidwa.”

Ndipo ena mwa aphunzitsi amalamulo anakhala pansi pomwepo, namaganiza mʼmitima mwawo kuti, “Nʼchifukwa chiyani munthuyu ayankhula chotere? Iye akuchitira mwano Mulungu! Ndani angakhululukire munthu machimo kupatula Mulungu yekha?”

Nthawi yomweyo Yesu anadziwa mu mzimu wake kuti izi ndi zimene ankaganiza mʼmitima yawo, ndipo anawawuza kuti, “Chifukwa chiyani mukuganiza zinthu izi? Chapafupi nʼchiyani; kunena kwa wofa ziwaloyu kuti, ‘Machimo ako akhululukidwa,’ kapena kuti, ‘Imirira, tenga mphasa yako ndipo yenda?’ 10 Koma kuti mudziwe kuti Mwana wa Munthu ali ndi ulamuliro pa dziko lapansi wokhululukira machimo.” Anati kwa wofa ziwaloyo, 11 “Ndikuwuza iwe, imirira, tenga mphasa yako ndipo pita kwanu.” 12 Anayimirira, nanyamula mphasa yake natuluka onse akumuona. Izi zinadabwitsa aliyense ndipo anayamika Mulungu nati, “Sitinaonepo zinthu ngati izi!”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.