Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 5:1-8

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe zoyimbira za zitoliro. Salimo la Davide.

Tcherani khutu ku mawu anga, Inu Yehova,
    ganizirani za kusisima kwanga
Mverani kulira kwanga kofuna thandizo,
    Mfumu yanga ndi Mulungu wanga,
    pakuti kwa Inu, ine ndikupemphera.
Mmawa, Yehova mumamva mawu anga;
    Mmawa ndimayala zopempha zanga pamaso panu
    ndi kudikira mwachiyembekezo.

Inu si Mulungu amene mumasangalala ndi zoyipa;
    choyipa sichikhala pamaso panu.
Onyada sangathe kuyima pamaso panu;
    Inu mumadana ndi onse ochita zoyipa.
Mumawononga iwo amene amanena mabodza;
    anthu akupha ndi achinyengo,
    Yehova amanyansidwa nawo.

Koma Ine, mwa chifundo chanu chachikulu,
    ndidzalowa mʼNyumba yanu;
mwa ulemu ndidzaweramira pansi
    kuyangʼana ku Nyumba yanu yoyera.
Tsogolereni Inu Yehova, mwa chilungamo chanu
    chifukwa cha adani anga ndipo
    wongolani njira yanu pamaso panga.

1 Mafumu 20:1-22

Beni-Hadadi Athira Nkhondo Samariya

20 Tsono Beni-Hadadi mfumu ya ku Aramu inasonkhanitsa magulu ake onse a ankhondo. Iye pamodzi ndi mafumu 32, akavalo awo ndi magaleta awo, anapita kukawuzungulira mzinda wa Samariya ndi kuwuthira nkhondo. Iye anatuma amithenga ake mu mzindamo kwa Ahabu mfumu ya Israeli, kukanena kuti, “Beni-Hadadi akuti, ‘Siliva wako ndi golide wako ndi wanga, ndipo akazi ako okongola ndi ana ako ndi anganso.’ ”

Mfumu ya Israeli inayankha kuti, “Monga mmene mwanenera, mbuye wanga mfumu, ine pamodzi ndi zonse zomwe ndili nazo ndi zanu.”

Amithenga aja anabwereranso kwa Ahabu ndipo anamuwuza kuti, “Beni-Hadadi akuti, ‘Ine ndinakulamula kuti undipatse siliva wako ndi golide wako, akazi ako ndi ana ako. Koma mawa nthawi ngati yomwe ino ndidzatuma atumiki anga kudzafufuza mʼnyumba yako yaufumu ndi nyumba za akuluakulu ako. Iwo adzatenga chilichonse chimene umachidalira ndi kupita nacho.’ ”

Pamenepo mfumu ya Israeli inayitanitsa akuluakulu a mʼdzikomo niwawuza kuti, “Taonani momwe munthuyu akufunira kutibweretsera mavuto! Atatumiza mawu oti ndimupatse akazi anga ndi ana anga, siliva wanga ndi golide wanga, ine sindinamukanize.”

Akuluakulu onse ndi anthu onse anayankha kuti, “Musamumvere kapena kuvomereza zofuna zake.”

Tsono Ahabu anayankha amithenga a Beni-Hadadi kuti, “Kamuwuzeni mbuye wanga mfumu kuti, ‘Mtumiki wanu adzachita zonse zimene munazifuna nthawi yoyamba ija, koma izi mwazifunazi sindingazikwanitse.’ ” Iwo anachoka nakapereka yankho kwa Beni-Hadadi.

10 Pamenepo Beni-Hadadi anatumizanso uthenga wina kwa Ahabu kuti, “Milungu indilange koopsa, ngati mu Samariya mudzakhale fumbi loti nʼkudzaza dzanja la aliyense wa anthu anga.”

11 Mfumu ya Israeli inayankha kuti, “Kamuwuzeni kuti, ‘Mwamuna mnzako nʼpachulu, nʼkulinga utakwerapo.’ ”

12 Beni-Hadadi anamva uthenga umenewu pamene iye ankamwa ndi mafumu anzake mʼmatenti awo, ndipo analamula anthu ake kuti, “Konzekerani kukathira nkhondo.” Choncho anakonzekera kukathira nkhondo mzindawo.

Ahabu Agonjetsa Beni-Hadadi

13 Ndipo taonani, mneneri wina anabwera kwa Ahabu mfumu ya Israeli nadzalengeza kuti, “Yehova akuti, ‘Kodi ukuchiona chigulu chachikulu cha ankhondochi? Taona, ndikuchipereka chimenechi lero mʼdzanja lako, ndipo pamenepo udzadziwa kuti Ine ndine Yehova.’ ”

14 Ahabu anafunsa kuti, “Koma ndani adzachita zimenezi?”

Mneneri anayankha kuti, “Yehova akuti, ‘Adzachita zimenezi ndi asilikali a nduna za mʼzigawo.’ ”

Ndipo iye anafunsa kuti, “Kodi ndani adzayambe nkhondoyi?”

Mneneriyo anayankha kuti, “Ndinu.”

15 Choncho Ahabu anawerenga asilikali achinyamata a nduna za mʼzigawo ndipo onse analipo 232. Ndipo anawerenganso ankhondo a ku Israeli ndipo onse analipo 7,000. 16 Iwo ananyamuka nthawi yamasana pamene Beni-Hadadi ndi mafumu 32 othandizana naye ankamwa mpaka kuledzera mʼmatenti awo. 17 Asilikali achinyamata a nduna za mʼzigawo ndiwo amene anayamba kupita ku nkhondo.

Nthawi imeneyi Beni-Hadadi nʼkuti atatumiza anthu oti akazonde, amene anadzafotokoza kuti, “Anthu ankhondo akubwera kuchokera ku Samariya.”

18 Iye anati, “Kaya akubwera mwamtendere kapena mwankhondo, muwagwire amoyo.”

19 Choncho asilikali achinyamata a nduna za mʼzigawo anatuluka mu mzinda, gulu lankhondo lili pambuyo pawo. 20 Ndipo aliyense wa iwo anapha munthu wake. Ataona izi, Aaramu anathawa Aisraeli ali pambuyo pawo kuwapirikitsa. Koma Beni-Hadadi mfumu ya ku Aaramu anathawa atakwera pa kavalo pamodzi ndi ankhondo ena okweranso pa akavalo. 21 Mfumu ya Israeli inapita chitsogolo ndi kugwira akavalo ndi magaleta ndipo Aaramu ambiri anaphedwa.

22 Zitachitika izi, mneneri wina anabwera kwa mfumu ya Israeli ndipo anati, “Mulimbike ndipo muganize bwino zoti mudzachite, chifukwa chaka chikudzachi mfumu ya Aramu idzakuthiraninso nkhondo.”

Yakobo 4:1-7

Kugonjera Mulungu

Nʼchiyani chimene chimayambitsa ndewu ndi mapokoso pakati panu? Kodi sizichokera ku zilakolako zimene zimalimbana mʼkati mwanu? Mumalakalaka zinthu koma simuzipeza, choncho mumapha. Mumasirira zinthu koma simutha kuzipeza zimene mukufuna, choncho mumakangana ndi kumenyana. Mulibe zinthuzo chifukwa simupempha kwa Mulungu. Koma ngakhale mumapempha simulandira, chifukwa mumapempha ndi zolinga zoyipa. Mumapempha kuti muzigwiritse ntchito pa zokusangalatsani nokha.

Inu anthu achigololo, kodi simukudziwa kuti kuchita ubwenzi ndi dziko lapansi ndi kudana ndi Mulungu? Choncho, aliyense wosankha kukhala bwenzi la dziko lapansi amasanduka mdani wa Mulungu. Kapena mukuganiza kuti Malemba amanena popanda chifukwa kuti Mulungu amafunitsitsa mwansanje mzimu umene Iye anayika kuti uzikhala mwa ife? Koma amatipatsa chisomo chochuluka. Nʼchifukwa chake Malemba amati,

“Mulungu amatsutsa odzikuza,
    koma apereka chisomo kwa odzichepetsa.”

Dziperekeni nokha kwa Mulungu. Mukaneni Mdierekezi ndipo adzakuthawani.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.