Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.
68 Adzuke Mulungu, adani ake amwazikane;
adani ake athawe pamaso pake.
2 Monga momwe mphepo imachotsera utsi; Inu muwawulutsire kutali.
Monga phula limasungunukira pa moto,
oyipa awonongeke pamaso pa Mulungu.
3 Koma olungama asangalale
ndi kukondwera pamaso pa Mulungu;
iwo akondwere ndi kusangalala.
4 Imbirani Mulungu imbirani dzina lake matamando,
mukwezeni Iye amene amakwera pa mitambo;
dzina lake ndi Yehova ndipo sangalalani pamaso pake.
5 Atate wa ana amasiye, mtetezi wa akazi amasiye,
ndiye Mulungu amene amakhala mʼmalo oyera.
6 Mulungu amakhazikitsa mtima pansi osungulumwa mʼmabanja,
amatsogolera amʼndende ndi kuyimba;
koma anthu osamvera amakhala ku malo owuma a dziko lapansi.
7 Pamene munatuluka kutsogolera anthu anu, Inu Mulungu,
pamene munayenda kudutsa chipululu,
8 dziko lapansi linagwedezeka, miyamba inakhuthula pansi mvula,
pamaso pa Mulungu, Mmodzi uja wa ku Sinai.
Pamaso pa Mulungu, Mulungu wa Israeli.
9 Munapereka mivumbi yochuluka, Inu Mulungu;
munatsitsimutsa cholowa chanu cholefuka.
10 Anthu anu anakhala mʼmenemo
ndipo munapatsa anthu osauka zimene zinkawasowa chifukwa cha ubwino wanu Mulungu.
19 Matamando akhale kwa Ambuye, kwa Mulungu Mpulumutsi wathu
amene tsiku ndi tsiku amasenza zolemetsa zathu.
20 Mulungu wathu ndi Mulungu amene amapulumutsa;
Ambuye Wamphamvuzonse ndiye amene amatipulumutsa ku imfa.
Mawu a Elifazi
22 Pamenepo Elifazi wa ku Temani anayankha kuti,
2 “Kodi munthu nʼkukhala waphindu kwa Mulungu?
Kodi munthu wanzeru angamupindulire Iye?
3 Kodi Wamphamvuzonse akanapeza chabwino chotani iweyo ukanakhala wolungama?
Kodi iyeyo akanapeza phindu lanji makhalidwe ako akanakhala angwiro?
4 “Kodi nʼchifukwa choti umamuopa, kuti azikudzudzula,
kuti azifuna kukukokera ku mlandu?
5 Kodi osati nʼchifukwa chakuti kuyipa kwako nʼkwakukulu?
Kodi machimo ako si opanda malire?
6 Iwe unkawumiriza abale ako kuti akupatse chikole popanda chifukwa;
umalanda anthu zovala zawo ndi kuwasiya amaliseche.
7 Sunawapatse madzi anthu otopa,
ndipo unawamana chakudya anthu anjala,
8 ngakhale unali munthu wamphamvu, wokhala ndi malo akeake,
munthu waulemu wake, wokhala mʼdzikomo.
9 Ndipo akazi amasiye unawachotsa wopanda kanthu,
ndipo unapondereza ana amasiye.
10 Nʼchifukwa chake misampha yakuzungulira,
nʼchifukwa chake tsoka ladzidzidzi lakuchititsa mantha,
11 nʼchifukwa chake kuli mdima kuti sungathe kuona kanthu,
nʼchifukwa chakenso madzi achigumula akumiza.
12 “Kodi Mulungu sali kutalitali kumwamba?
Ndipo ona nyenyezi zili mmwamba kwambirizo, ona kutalika kwake pamene zililipo!
13 Komabe iweyo ukunena kuti, ‘Kodi Mulungu amadziwa chiyani?
Kodi Iye amaweruza mu mdima woterewu?
14 Mitambo yakuda yamuphimba, kotero kuti Iye sakutiona
pamene akuyendayenda pamwamba pa thambopo.’
15 Kodi iwe udzayendabe mʼnjira yakale
imene anthu oyipa ankayendamo?
16 Iwo anachotsedwa nthawi yawo isanakwane,
maziko awo anakokoloka ndi madzi achigumula.
17 Anthuwo anati kwa Mulungu, ‘Tichokereni!
Kodi Wamphamvuzonse angatichitire chiyani?’
18 Chonsecho ndi Iye amene anadzaza nyumba zawo ndi zinthu zabwino,
choncho ine sindigwirizana ndi uphungu wa anthu oyipa.
19 “Anthu olungama amaona kuwonongeka kwawo ndipo amakondwera;
anthu osalakwa amangoseka, akamuona woyipa akulangidwa.
20 Amanena kuti, ‘Ndithudi adani athu awonongeka
ndipo moto wawononga chuma chawo!’
Atumwi Alandira Paulo
2 Kenaka, patatha zaka khumi ndi zinayi, ndinapitanso ku Yerusalemu, nthawi iyi ndinapita ndi Barnaba. Ndinatenganso Tito kuti apite nafe. 2 Ine ndinapita chifukwa Mulungu anachita kundionetsera kuti ndipite ndipo ndinakakumana ndi atsogoleri mu msonkhano mwamseri ndi kuwafotokozera Uthenga Wabwino umene ndimalalikira pakati pa anthu a mitundu ina. Ndinachita zimenezi kuti ndikhale ndi chitsimikizo kuopa kuti mwina ndinathamanga kapena ndimathamanga liwiro pachabe. 3 Komatu ngakhale Tito, amene anali nane sanakakamizidwe kuti achite mdulidwe, ngakhale iyeyo anali Mgriki. 4 Nkhani iyi inayambika chifukwa abale ena achinyengo amene analowerera pakati pathu kuti adzaone za ufulu umene tili nawo mwa Khristu Yesu ndikuti atisandutse akapolo. 5 Ife sitinawagonjere ndi pangʼono pomwe, nʼcholinga chakuti choonadi cha Uthenga Wabwino chikhalebe ndi ife.
6 Koma kunena za aja ankaoneka ngati ofunika kwambiri, chimene iwo anali sichisintha kanthu kwa ine; chifukwa Mulungu alibe tsankho, iwowo sanawonjezepo kanthu pa uthenga wanga. 7 Makamaka anaona kuti ine ndinapatsidwa ntchito yolalikira Uthenga Wabwino kwa anthu a mitundu ina monga momwe Petro anapatsidwa ntchito yolalikira Uthenga Wabwino kwa Ayuda. 8 Pakuti Mulungu, amene amagwira ntchito mu utumiki wa Petro monga mtumwi kwa Ayuda, amagwiranso ntchito mu utumiki wanga monga mtumiki kwa anthu a mitundu ina. 9 Yakobo, Petro ndi Yohane, amene ankatengedwa ngati mizati, atazindikira chisomo chimene chinapatsidwa kwa ine, anagwirana chanza ndi ine ndi Barnaba kusonyeza chiyanjano chathu. Iwo anavomereza kuti ife tipite kwa anthu a mitundu ina ndipo iwo apite kwa Ayuda. 10 Chimene iwo anapempha ndi chakuti ife tipitirize kukumbukira osauka, chinthu chimene ine ndinali okonzeka kuchichita.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.