Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

New Testament in a Year

Read the New Testament from start to finish, from Matthew to Revelation.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
1 Akorinto 10:19-33

19 Kodi ndikutanthauza kuti nsembe zoperekedwa kwa mafano ndi kanthu konse, kapena kuti mafano ndi kanthu konse? 20 Ayi. Nsembe za osakhulupirira zimaperekedwa kwa ziwanda, osati kwa Mulungu, ndipo sindikufuna kuti muziyanjana ndi ziwandazo. 21 Simungamwe chikho cha Ambuye, ndi kukamweranso chikho cha ziwanda. Simungadyere pa tebulo la Ambuye ndiponso la ziwanda. 22 Kodi tikufuna kuwutsa mkwiyo wa Ambuye? Kodi ndife amphamvu kuposa Iye?

Ufulu wa Munthu Wokhulupirira

23 Mutha kunena kuti, “Zinthu zonse nʼzololedwa,” komatu si zonse zili za phindu. “Zinthu zonse nʼzololedwa,” komatu si zonse zimathandiza. 24 Munthu aliyense asafunefune zokomera iye yekha, koma zokomeranso ena.

25 Idyani nyama iliyonse imene amagulitsa pa msika, osafunsa mafunso okhudzana ndi chikumbumtima chanu. 26 Popeza kuti, “Dziko lapansi ndi la Ambuye ndi zonse za mʼmenemo ndi zake.”

27 Ngati wosakhulupirira akuyitanani kuti mukadye naye, inuyo ndi kuvomera kupitako, mukadye chilichonse chimene akakupatseni ndipo musakafunse mafunso okhudzana ndi chikumbumtima chanu. 28 Koma ngati wina akuwuzani kuti, “Izi zaperekedwa nsembe,” musadye zimenezo, pofuna kuthandiza amene wakuwuzaniyo komanso chifukwa cha chikumbumtima. 29 Ndikunena za chikumbumtima cha winayo osati chanu. Tsono mungafunse kuti, nʼchifukwa chiyani ufulu wanga ukuphwanyidwa chifukwa cha chikumbumtima cha munthu wina? 30 Ngati ndikuyamika Mulungu chifukwa cha chakudya, nanga munthu angandinyoze bwanji pa zinthu zomwe ndayamikira nazo Mulungu?

31 Nʼchifukwa chake chilichonse mungadye kapena kumwa, kapena chimene mungachite, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu. 32 Musakhumudwitse aliyense, kaya ndi Myuda, Mgriki, kapena mpingo wa Mulungu. 33 Mu zonse ndikuyesetsa kukondweretsa aliyense mʼnjira iliyonse. Popeza sindikufunafuna zokondweretsa ine ndekha koma zokomera ambiri kuti apulumutsidwe.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.