Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

New Testament in a Year

Read the New Testament from start to finish, from Matthew to Revelation.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Aroma 11:19-36

19 Tsono mudzati, “Nthambizo zinakhadzulidwa kuti ine ndilumikizidwepo.” 20 Nʼzoona. Koma iwo anakhadzulidwa chifukwa chosakhulupirira ndipo inu mukuyima mwachikhulupiriro. Musadzitukumule, koma muchite mantha. 21 Pakuti ngati Mulungu sanalekerere nthambi zachibadwidwe, Iye sadzakulekererani inunso.

22 Nʼchifukwa chake ganizirani za kukoma mtima ndi za ukali wa Mulungu. Ukali uli kwa iwo amene anagwa koma kukoma mtima kwa inu, malinga ngati musamala kukoma mtima kwakeko kupanda kutero inunso mudzakhadzulidwanso. 23 Ngati iwo asiya kukhala osakhulupirira, adzalumikizidwanso pakuti Mulungu akhoza kuwalumikizanso. 24 Pakuti ngati inu, mwa chilengedwe munali mtengo wa olivi wa kuthengo, Mulungu anakukhadzulani nakulumikizani ku mtengo wa olivi wodzalidwa, zomwe ndi zotsutsana ndi chilengedwe, kodi sikudzakhala kwapafupi kwa Iye kuwalumikizanso mu mtengo wawowawo wa olivi?

Aisraeli Onse Adzapulumuka

25 Abale, ine sindifuna kuti mukhale osadziwa za chinsinsi ichi, kuti mungadziyese nokha anzeru. Kuwuma mtima kumene Aisraeli akuchita ndi kwa kanthawi kufikira chiwerengero cha a mitundu chitalowa. 26 Kotero tsono Aisraeli onse adzapulumuka, monga kwalembedwa kuti,

“Mpulumutsi adzachokera ku Ziyoni;
    Iye adzachotsa zoyipa zonse za Yakobo.
27 Ndipo ili lidzakhala pangano langa ndi iwo
    pamene Ine ndidzachotsa machimo awo.”

28 Chifukwa cha Uthenga Wabwino, Aisraeli asanduka adani a Mulungu kuti inu mupindule. Koma kunena za kusankhidwa, iwo ndi okondedwa ndi Mulungu chifukwa cha makolo awo aja. 29 Pakuti Mulungu akayitana munthu ndi kumupatsa mphatso sangasinthenso. 30 Monga mmene inu munalili, osamvera Mulungu pa nthawi ina, tsopano mwalandira chifundo chifukwa cha kusamvera kwawo. 31 Chonchonso iwo akhala osamvera tsopano kuti iwonso alandire chifundo chifukwa cha chifundo cha Mulungu kwa inu. 32 Pakuti Mulungu anasandutsa anthu onse a mʼndende ya kusamvera kuti Iye akaonetse chifundo kwa onse.

Kulemekeza Mulungu

33 Aa! Nzeru za Mulungu ndi chidziwitso chake ndi zozama kwambiri!
    Ndani angazindikire maweruzidwe ake,
    ndipo njira zake angazitulukire ndani?
34 “Kodi wadziwa ndani maganizo a Ambuye?
    Kapena ndani anakhalapo mlangizi wake?”
35 “Kodi ndani anapereka mphatso kwa Mulungu,
    kuti Mulunguyo amubwezere iye?”
36 Pakuti zinthu zonse nʼzochokera kwa Iye, nʼzolengedwa ndi Iye ndipo zimabweretsa ulemerero kwa Iye.
    Kwa Iye kukhale ulemerero mpaka muyaya! Ameni.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.