New Testament in a Year
20 Aliyense akhale monga analili pamene Mulungu anamuyitana.
21 Kodi munali kapolo pamene Mulungu anakuyitanani? Musavutike nazo zimenezi. Koma ngati mutapeza mwayi woti mulandire ufulu, ugwiritseni ntchito mwayiwo. 22 Pakuti amene anali kapolo pamene amayitanidwa ndi Ambuye, ndi mfulu wa Ambuye; chimodzimodzinso amene anali mfulu pamene anayitanidwa, ndi kapolo wa Khristu. 23 Munagulidwa ndi mtengowapatali, choncho musakhalenso akapolo a anthu. 24 Abale, aliyense angokhala pamaso pa Mulungu monga momwe analili pamene Mulungu anamuyitana.
Osakwatiwa
25 Tsopano za anamwali: Ine ndilibe lamulo lochokera kwa Ambuye, koma ndipereka maganizo anga monga ngati munthu amene mwachifundo cha Ambuye ndine wodalirika. 26 Chifukwa cha masautso a masiku ano, ndikuganiza kuti nʼkwabwino kuti munthu akhale monga mmene alili. 27 Kodi ndinu wokwatira? Musalekane. Kodi ndinu wosakwatira? Musafunefune mkazi. 28 Komabe ngati mukwatira simunachimwe; ndipo ngati namwali akwatiwa sanachimwenso. Koma amene walowa mʼbanja adzakumana ndi zovuta zambiri mʼmoyo uno, ndipo sindikufuna kuti inu mukumane ndi zovutazi.
29 Abale, chimene ndikutanthauza nʼchakuti nthawi yatha. Kuyambira tsopano anthu okwatira akhale ngati sanakwatire. 30 Amene akulira akhale monga ngati sakulira. Amene akukondwa akhale ngati sakukondwa. Amene akugula zinthu akhale ngati alibe zinthuzo. 31 Amene akugwiritsa ntchito zinthu za dziko lapansi lino, akhale ngati sizikuwakhudza. Pakuti dziko lapansi lino mmene lilirimu, likupita.
32 Ine ndikufuna kuti mumasuke ku nkhawa zanu. Munthu wosakwatira amangolabadira za Ambuye, mmene angakondweretsere Ambuyewo. 33 Koma wa pa banja amalabadira za dziko lapansi lino, mmene angakondweretsere mkazi wake, 34 ndipo chifukwa ichi amatanganidwa kwambiri. Mkazi wosakwatiwa kapena namwali, amalabadira za Ambuye. Cholinga chake ndi kudzipereka kwa Ambuye mʼthupi ndi mu uzimu momwe. Koma mkazi wokwatiwa amalabadira za dziko lapansi lino, mmene angakondweretsere mwamuna wake. 35 Ndikunena izi kufuna kuthandiza inu nomwe osati kukupanikizani. Ine ndikufuna mukhale moyenera mosadzigawa pa kudzipereka kwanu kwa Ambuye.
36 Ngati wina akuganiza kuti akumulakwira namwali yemwe anapalana naye ubwenzi, ndipo ngati chilakolako chake chikunka chikulirakulirabe, ndipo akuona kuti nʼkofunika kumukwatira, ayenera kuchita monga wafunira, kutero si kuchimwa ayi. 37 Koma ngati wina motsimikiza mtima wake, popanda womukakamiza, koma akuchita mwa chifuniro chake, ndipo watsimikiza mtima kuti samukwatira namwaliyo, munthuyu akuchitanso chokhoza. 38 Choncho amene akukwatira namwali amene ali naye pa ubwenzi, akuchita bwino, koma amene sangakwatire namwaliyo akuchita bwino koposa.
39 Mkazi amamangika ndi lamulo la ukwati nthawi zonse pamene mwamuna wake ali ndi moyo. Koma mwamuna wake akamwalira, ali ndi ufulu kukwatiwa ndi wina aliyense amene akumufuna, koma mwamunayo akhale wa mwa Ambuye. 40 Mʼmaganizo anga, mkaziyo adzakhala wokondwa koposa ngati atangokhala wosakwatiwa. Ndipo ndikuganiza kuti inenso ndili naye Mzimu wa Mulungu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.