New Testament in a Year
Chisankho Chopambana cha Mulungu
9 Ine ndikunena zoona mwa Khristu. Sindikunama ndipo chikumbumtima changa kudzera mwa Mzimu Woyera chikundichitira umboni. 2 Ndili ndi chisoni chachikulu ndipo ndikumva kupwetekeka kosalekeza mu mtima mwanga. 3 Pakuti ndikanafuna ine mwini nditatembereredwa ndi kuchotsedwa mwa Khristu chifukwa cha abale anga, amene ndi a mtundu wanga, 4 anthu Aisraeli. Iwo anasankhidwa kukhala ana. Mulungu anawapatsa ulemerero, anachita nawo mapangano, kuwapatsa Malamulo, Nyumba yopembedzeramo ndi malonjezano ake. 5 Awo ndi makolo athu. Kuchokera kwa iwo mʼthupi ndi kumene kunachokera makolo a Khristu Yesu amene ndi Mulungu wolamulira zinthu zonse, alemekezeke mpaka muyaya! Ameni.
6 Sikuti mawu a Mulungu analephera. Pakuti si onse obadwa mwa Israeli amene ndi Israeli. 7 Kapena kuti ana ake chifukwa anachokera mwa Abrahamu. Koma zidzukulu zako zidzachokera mwa Isake. 8 Kutanthauza kuti, si ana obadwa mʼthupi amene ndi ana a Mulungu koma ndi ana a lonjezano amene amatengedwa kukhala zidzukulu za Abrahamu. 9 Pakuti Mulungu analonjeza ponena kuti, “Pa nthawi yake ngati yomwe ino chaka chamawa ndidzabweranso, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna.”
10 Ndipo si pokhapo ayi. Ana awiri a Rebeka aja abambo awo anali mmodzi, kholo lathu Isake. 11 Komabe, ana amapasawa asanabadwe kapena asanachite chilichonse chabwino kapena choyipa, nʼcholinga choti chifuniro cha Mulungu chosankhiratu munthu aliyense chipitirire, 12 osati chifukwa cha ntchito za munthu koma chifuniro cha Iye mwini, anawuza Rebeka kuti, “Wamkulu adzatumikira wamʼngʼono.” 13 Monga momwe kwalembedwa kuti, “Ine ndinakonda Yakobo, koma ndinamuda Esau.”
14 Nanga tsono tidzanena chiyani? Kodi Mulungu ndi osalungama? Ayi, ndi pangʼono pomwe! 15 Pakuti Mulungu anawuza Mose kuti,
“Ine ndidzachitira chifundo amene ndikufuna kumuchitira chifundo,
ndipo ndidzakomera mtima amene ndikufuna kumukomera mtima.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.