Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Ndakatulo ya Asafu.
78 Inu anthu anga imvani chiphunzitso changa;
mvetserani mawu a pakamwa panga.
2 Ndidzatsekula pakamwa panga mʼmafanizo,
ndidzayankhula zinthu zobisika, zinthu zakalekale
3 zimene tinazimva ndi kuzidziwa,
zimene makolo athu anatiwuza.
4 Sitidzabisira ana awo,
tidzafotokozera mʼbado wotsatira
ntchito zotamandika za Yehova,
mphamvu zake, ndi zozizwitsa zimene Iye wachita.
12 Iyeyo anachita zodabwitsa makolo athu akuona,
mʼdziko la Igupto, mʼchigawo cha Zowani.
13 Anagawa nyanja pakati ndi kudutsitsapo iwowo,
Iye anachititsa madzi kuyima chilili ngati khoma.
14 Anawatsogolera ndi mtambo masana
ndi kuwala kwa moto usiku wonse.
15 Iye anangʼamba miyala mʼchipululu
ndi kuwapatsa madzi ochuluka ngati a mʼnyanja zambiri;
16 Anatulutsa mitsinje kuchokera mʼmingʼalu ya miyala
ndi kuyenda madzi ngati mitsinje.
Yoswa Alowa Mʼmalo mwa Mose
12 Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Kwera phiri la Abarimu kuti ukaone dziko limene ndalipereka kwa Aisraeli. 13 Ukakaliona udzamwalira ngati Aaroni mʼbale wako, 14 chifukwa pamene anthu anawukira ku madzi a Meriba mʼchipululu cha Zini, inu nonse simunamvere lamulo londilemekeza Ine ngati Woyera pamaso pawo.” (Awa anali madzi a ku Meriba ku Kadesi mʼchipululu cha Zini).
Amufunsa Yesu za Ulamuliro Wake
27 Iwo anafikanso ku Yerusalemu, ndipo pamene Yesu amayenda mʼmabwalo a Nyumba ya Mulungu, akulu a ansembe, aphunzitsi amalamulo ndi akuluakulu anabwera kwa Iye. 28 Iwo anafunsa kuti, “Mukuchita izi ndi ulamuliro wanji? Ndipo anakupatsani ulamuliro umenewu ndi ndani?”
29 Yesu anayankha kuti, “Ndikufunsani funso limodzi. Mundiyankhe, ndipo ndikuwuzani ndi ulamuliro wanji umene ndikuchitira izi. 30 Ubatizo wa Yohane, unali wochokera kumwamba, kapena kwa anthu? Ndiwuzeni.”
31 Iwo anakambirana pakati pawo ndipo anati, “Tikati, ‘Wochokera kumwamba,’ atifunsa kuti, ‘Nanga nʼchifukwa chiyani simunamukhulupirire?’ 32 Koma ife tikati, ‘Wochokera kwa anthu.’ ” (Amaopa anthu, pakuti aliyense amakhulupirira kuti Yohane analidi mneneri).
33 Ndipo anamuyankha Yesu kuti, “Sitikudziwa.”
Yesu anati, “Nanenso sindikuwuzani kuti ndi ulamuliro wanji ndichitira zimenezi.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.