Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 105:1-6

105 Yamikani Yehova, itanani dzina lake;
    lalikirani pakati pa anthu a mitundu ina zimene Iye wachita.
Imbirani Iye, imbani matamando kwa Iyeyo;
    fotokozani za machitidwe ake onse odabwitsa.
Munyadire dzina lake loyera;
    mitima ya iwo amene amafunafuna Yehova ikondwere.
Dalirani Yehova ndi mphamvu zake;
    funafunani nkhope yake nthawi yonse.

Kumbukirani zodabwitsa zimene Iye anazichita,
    zozizwitsa zake ndi maweruzo amene anapereka,
inu zidzukulu za Abrahamu mtumiki wake,
    inu ana a Yakobo, osankhika ake.

Masalimo 105:37-45

37 Yehova anatulutsa Israeli, atatenga siliva ndi golide wambiri,
    ndipo pakati pa mafuko awo palibe mmodzi amene anafowoka.
38 Dziko la Igupto linakondwa pamene iwo anachoka,
    pakuti kuopsa kwa Israeli kunawagwera iwo.
39 Iye anatambasula mitambo ngati chofunda chawo,
    ndi moto owawunikira usiku.
40 Iwo anapempha, ndipo Iye anawabweretsera zinziri
    ndipo anawakhutitsa ndi chakudya chochokera kumwamba.
41 Iye anatsekula thanthwe, ndipo madzi anatuluka;
    ngati mtsinje anayenda mʼchipululu.

42 Pakuti anakumbukira lonjezo lake loyera limene
    linaperekedwa kwa Abrahamu mtumiki wake.
43 Iye anatulutsa anthu ake akukondwera,
    osankhika ake akufuwula mwachimwemwe;
44 Iye anawapatsa mayiko a anthu a mitundu ina
    ndipo anakhala olowamʼmalo a zimene ena anazivutikira,
45 kuti iwo asunge malangizo ake
    ndi kutsatira malamulo ake.

Tamandani Yehova.

Eksodo 15:22-27

Madzi a ku Mara ndi Elimu

22 Ndipo Mose anatsogolera Israeli kuchoka ku nyanja yofiira ndi kupita ku chipululu cha Suri. Anayenda mʼchipululu masiku atatu wosapeza madzi. 23 Ndipo anafika ku Mara. Koma sanathe kumwa madzi akumeneko chifukwa anali owawa. (Ndi chifukwa chake malowo amatchedwa Mara). 24 Tsono anthu aja anadandaulira Mose ndi kumufunsa kuti, “Kodi tikumwa chiyani?”

25 Ndipo Mose anapemphera kwa Yehova, ndipo Yehova anamuonetsa kamtengo. Iye anakaponya mʼmadzimo ndipo madzi anakhala abwino.

Kumeneko Yehova anawayikira lamulo ndi maweruziro. Kumenekonso Yehova anawayesa. 26 Yehova anati, “Ngati inu mudzamvetsa bwino mawu anga, kuchita zolungama, kumvera malamulo anga ndi kusamalitsa zimene ndikukuwuzani ndiye kuti Ine sindidzayika pa inu matenda amene ndinayika pa anthu a ku Igupto popeza ndine Yehova amene ndimakuchiritsani.”

27 Kenaka anafika ku Elimu, kumene kunali akasupe khumi ndi awiri ndi mitengo ya migwalangwa makumi asanu ndi awiri, ndipo anamanga misasa yawo kumeneko pafupi ndi madzi.

2 Akorinto 13:1-4

Mawu Otsiriza ndi Ochenjeza

13 Uwu ndi ulendo wachitatu ndikubwera kudzakuyenderani. “Nkhani itsimikizike ndi umboni wa anthu awiri kapena atatu.” Ndinakuchenjezani kale pamene ndinali nanu ulendo wachiwiri uja. Tsopano ndikubwereza ndisanafike. Ndikabweranso sindidzachitira chifundo amene anachimwa poyamba paja kapena wina aliyense amene anachimwa, popeza mufuna chitsimikizo chakuti Khristu akuyankhula kudzera mwa ine. Iye siwofowoka pofuna kuchita nanu koma ndi wamphamvu pakati panu. Pofuna kutsimikizira, anapachikidwa ali wofowoka koma ali ndi moyo mwamphamvu ya Mulungu. Chomwechonso, ife ndife ofowoka mwa Iye, koma tidzakhala ndi moyo pamodzi naye ndi mphamvu ya Mulungu, potumikira pakati panu.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.