Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.
139 Inu Yehova, mwandisanthula
ndipo mukundidziwa.
2 Inu mumadziwa pamene ndikhala pansi ndi pamene ndidzuka;
mumazindikira maganizo anga muli kutali.
3 Mumapenyetsetsa pamene ndikutuluka ndi kugona kwanga;
mumadziwa njira zanga zonse.
4 Mawu asanatuluke pa lilime langa
mumawadziwa bwinobwino, Inu Yehova.
5 Mumandizinga kumbuyo ndi kutsogolo komwe;
mwasanjika dzanja lanu pa ine.
6 Nzeru zimenezi ndi zopitirira nzeru zanga,
ndi zapamwamba kuti ine ndizipeze.
7 Kodi ndingapite kuti kufuna kuzemba Mzimu wanu?
Kodi ndingathawire kuti kuchoka pamaso panu?
8 Ndikakwera kumwamba, Inu muli komweko;
ndikakagona ku malo a anthu akufa, Inu muli komweko.
9 Ngati ndiwulukira kotulukira dzuwa,
ngati ndikakhala ku malekezero a nyanja,
10 kumenekonso dzanja lanu lidzanditsogolera,
dzanja lanu lamanja lidzandigwiriziza.
11 Ndikanena kuti, “Zoonadi, mdima udzandibisa ndithu
ndipo kuwunika kukhale mdima mondizungulira,”
12 komabe mdimawo sudzakhala mdima kwa Inu;
usiku udzawala ngati masana,
pakuti mdima uli ngati kuwunika kwa Inu.
23 Santhuleni, Inu Mulungu ndipo mudziwe mtima wanga;
Yeseni ndipo mudziwe zolingalira zanga.
24 Onani ngati muli mayendedwe aliwonse oyipa mwa ine,
ndipo munditsogolere mʼnjira yanu yamuyaya.
21 “Ine ndidzaonetsa ulemerero wanga pakati pa anthu a mitundu ina, ndipo adzaona mmene ndidzawalangire ndikadzayika dzanja langa pa iwo. 22 Kuyambira tsiku limenelo mpaka mʼtsogolo Aisraeli adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wawo. 23 Ndipo anthu a mitundu ina adzadziwa kuti anthu a Israeli anatengedwa ukapolo chifukwa cha tchimo lawo, chifukwa anali osakhulupirika kwa Ine. Choncho Ine ndinawabisira nkhope yanga ndi kuwapereka kwa adani awo. Motero anaphedwa pa nkhondo. 24 Ndinawachita zimenezi chifukwa cha kunyansa kwawo ndi zolakwa zawo, ndipo ndinawabisira nkhope yanga.
25 “Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Tsopano ndidzakhazikanso pa bwino banja la Yakobo. Ndidzachitira chifundo Aisraeli onse, ndipo ndidzateteza dzina langa loyera. 26 Anthuwo akadzakhala mwamtendere mʼdziko lawo popanda wina wowaopseza, pamenepo adzayiwala zamanyazi zawo zimene zinawachitikira chifukwa chosandikhulupirira Ine. 27 Ndidzawabwezeranso kwawo kuchokera pakati pa anthu a mitundu ina ndipo ndidzawasonkhanitsa kuchokera ku mayiko a adani awo. Poteropo ndidzaonetsa pamaso pa anthu a mitundu yambiri kuti ndine Woyera. 28 Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wawo, ngakhale kuti ndinawapereka ku ukapolo pakati pa anthu a mitundu ina. Ine ndidzawasonkhanitsanso ku dziko lawo osasiyako wina mʼmbuyo. 29 Ine sindidzawabisiranso nkhope yanga, pakuti ndidzathira Mzimu wanga pa Aisraeli. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.”
Kukhazikika kwa Malonjezo a Mulungu
13 Pamene Mulungu ankamulonjeza Abrahamu, popeza panalibe wamkulu womuposa, amene akanamutchula ndikulumbira mwa Iye, analumbira mwa Iye yekha kuti, 14 “Ine ndidzakudalitsa ndithu, ndipo ndidzakupatsa zidzukulu zambiri.” 15 Ndipo Abrahamu atayembekezera mofatsa, analandira zimene anamulonjezazo.
16 Anthu amalumbira mʼdzina la wina amene akuwaposa, ndipo lumbiro lotere limatsimikizira zomwe zayankhulidwa ndi kuthetsa mikangano yonse. 17 Momwemonso Mulungu pofuna kutsimikizira anthu amene adzalandire lonjezo, kuti Iye sangasinthe maganizo, anatsimikiza lonjezo lakelo ndi lumbiro. 18 Mulungu anachita zinthu ziwiri, lonjezo ndi lumbiro, zimene sizingathe kusintha ndipo Mulungu sangathe kunama. Choncho Mulungu akutilimbikitsa mtima ife amene tinathawira kwa Iye kuti tichigwiritsitse chiyembekezo chimene tinalandira. 19 Chiyembekezo chimenechi tili nacho ngati nangula wa moyo wathu. Nʼchokhazikika ndi chosagwedezeka ndipo chimalowa mʼkatikati mwa malo opatulika, kuseri kwa chinsalu chotchinga. 20 Yesu anatitsogolera kupita kumeneko, nalowako mʼmalo mwathu. Iye anasanduka Mkulu wa ansembe onse wamuyaya, monga mwa dongosolo la unsembe wa Melikizedeki.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.