Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 45:10-17

10 Tamvera, iwe mwana wa mkazi ganizira ndipo tchera khutu;
    iwala anthu ako ndi nyumba ya abambo ako.
11 Mfumu yathedwa nzeru chifukwa cha kukongola kwako;
    mulemekeze pakuti iyeyo ndiye mbuye wako.
12 Mwana wa mkazi wa ku Turo adzabwera ndi mphatso,
    amuna a chuma adzafunafuna kukoma mtima kwako.

13 Wokongola kwambiri ndi mwana wa mfumu ali mʼchipinda mwake,
    chovala chake ndi cholukidwa ndi thonje ndi golide.
14 Atavala zovala zamaluwamaluwa akupita naye kwa mfumu;
    anamwali okhala naye akumutsatira
    ndipo abweretsedwa kwa inu.
15 Iwo akuwaperekeza ndi chimwemwe ndi chisangalalo;
    akulowa mʼnyumba yaufumu.

16 Ana ako aamuna adzatenga malo a makolo ako;
    udzachititsa kuti akhale ana a mfumu mʼdziko lonse.
17 Ndidzabukitsa mbiri yako mʼmibado yonse;
    choncho mitundu yonse idzakutamanda ku nthawi za nthawi.

Genesis 27:18-29

18 Yakobo anapita kwa abambo ake ndipo anati, “Abambo anga.”

Ndipo anayankha, “Eya, kodi ndiwe mwana wanga uti?”

19 Yakobo anati kwa abambo ake, “Ndine Esau mwana wanu woyamba. Ndachita monga munandiwuzira. Chonde dzukani ndi kukhala tsonga kuti mudyeko nyama ndakukonzeraniyi kuti tsono mundidalitse.”

20 Isake anafunsa mwana wake, “Wayipeza msanga chotere bwanji mwana wanga?”

Iye anayankha, “Yehova Mulungu wanu anandithandiza kuti ndiyipeze.”

21 Pamenepo Isake anati kwa Yakobo, “Tabwera pafupi ndikukhudze mwana wanga, kuti ndidziwedi ngati uli mwana wanga Esau kapena ayi.”

22 Yakobo anasendera kufupi ndi abambo ake Isake ndipo anamukhudza nati, “Mawuwa ndi mawu a Yakobo koma mikonoyi ndi mikono ya Esau.” 23 Sanamuzindikire, popeza mikono yake inali ndi ubweya ngati ya mʼbale wake Esau; choncho anamudalitsa. 24 Isake anafunsa, “Kodi ndiwedi mwana wanga Esau?”

Yakobo anayankha, “Inde ndine.”

25 Ndipo iye anati, “Mwana wanga, patseko nyama yakoyo ndidye kuti ndikudalitse.”

Yakobo anabwera ndi nyama ija kwa Isake ndipo anadya. Kenaka anamupatsanso vinyo ndipo anamwa. 26 Tsono Isake anati kwa Yakobo, “Bwera kuno mwana wanga undipsompsone.”

27 Choncho anapita namupsompsona. Apa Isake anamva fungo la zovala zake, ndipo anamudalitsa nati,

“Haa, fungo la mwana wanga
    lili ngati fungo la munda
    umene Yehova waudalitsa.
28 Mulungu akugwetsere mame akumwamba
    ndipo minda yako ibale tirigu wambiri
    ndi vinyo watsopano.
29 Mitundu ya anthu ikutumikire iwe
    ndipo anthu akugwadire iwe.
Ukhale wolamula abale ako,
    ndipo ana aamuna a amayi ako akugwadire.
Amene akutemberera iwe atembereredwe
    ndipo amene adalitsa iwe adalitsike.”

Luka 10:21-24

21 Nthawi imeneyo Mzimu Woyera anadzaza Yesu ndi chimwemwe ndipo anati, “Ine ndikulemekeza Inu, Atate Ambuye a kumwamba ndi dziko lapansi, chifukwa mwawabisira anthu anzeru ndi ophunzira zinthu izi ndipo mwaziwulula kwa ana aangʼono. Inde, Atate, pakuti munachita zimenezi mwachifuniro chanu.

22 “Atate anga anapereka zinthu zonse mʼmanja mwanga. Palibe amene amadziwa Mwana kupatula Atate yekha, ndipo palibe amene amadziwa Atate kupatula Mwana yekha, ndiponso amene Mwanayo akufuna kumuwululira.”

23 Kenaka anatembenukira kwa ophunzira ake nawawuza iwo okha kuti, “Ndi odala maso amene akuona zimene mukuonazi. 24 Pakuti kunena zoona aneneri ambiri ndi mafumu anafunitsitsa kuona zimene mukuonazi koma sanazione, ndi kumva zimene mukumvazi koma sanazimve.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.