Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 35:11-28

11 Mboni zopanda chisoni zinayimirira,
    zinandifunsa zinthu zimene sindikuzidziwa.
12 Iwo anandibwezera zoyipa pa zabwino
    ndipo anasiya moyo wanga pa chisoni.
13 Koma pamene iwo ankadwala, ine ndinavala chiguduli
    ndi kudzichepetsa ndekha posala zakudya.
Pamene mapemphero anga anabwerera kwa ine osayankhidwa,
14     ndinayendayenda ndi kulira maliro,
    kumulira ngati bwenzi langa kapena mʼbale wanga.
Ndinaweramitsa mutu wanga mosweka mtima
    kukhala ngati ndikulira amayi anga.
15 Koma pamene ndinaphunthwa, iwo anasonkhana mosangalala;
    ondithira nkhondo anasonkhana kutsutsana nane, ineyo osadziwa.
    Iwo sanasiye kundiyankhulira mawu onyoza.
16 Monga anthu osapembedza, iwo anandinyoza mwachipongwe;
    anandikukutira mano awo.
17 Ambuye, mpaka liti mudzakhala mukungoyangʼana?
    Landitsani moyo wanga ku chiwonongeko chawo,
    moyo wanga wopambana ku mikango.
18 Ndidzakuyamikani mu msonkhano waukulu;
    pakati pa gulu lalikulu la anthu ndidzakutamandani.

19 Musalole adani anga onyenga
    akondwere chifukwa cha masautso anga;
musalole kuti amene amadana nane popanda chifukwa
    andiyangʼane chamʼmbali mondinyoza.
20 Iwowo sayankhula mwamtendere,
    koma amaganizira zonamizira
    iwo amene amakhala mwabata mʼdziko.
21 Iwo amandiseka mofuwula ndipo amati, “Haa! Haa!
    Ndipo ndi maso athuwa ife taziona.”

22 Yehova mwaona zimenezi; musakhale chete.
    Ambuye musakhale kutali ndi ine.
23 Dzukani, ndipo nyamukani kunditeteza!
    Mulimbane nawo chifukwa cha ine, Mulungu wanga ndi Ambuye anga.
24 Onetsani kusalakwa kwanga mwa chilungamo chanu, Inu Yehova Mulungu wanga.
    Musalole kuti akondwere chifukwa cha mavuto anga.
25 Musalole kuti aganize kuti, “Amati atani, zachitika monga momwe timafunira!”
    Kapena kunena kuti, “Tamutha ameneyu basi.”

26 Onse amene amakondwera ndi masautso anga
    achite manyazi ndi kusokonezeka.
Onse amene amadzikweza kufuna kundipambana,
    avekedwe manyazi ndi mnyozo ngati zovala.
27 Koma amene amakondwera chifukwa chakuti ndine wosalakwa,
    afuwule mwachimwemwe ndi chisangalalo.
Nthawi zonse azinena kuti, “Yehova akwezeke,
    Iye amene amakondwera ndi kupeza bwino kwa mtumiki wake.”
28 Pakamwa panga padzayankhula za chilungamo chanu
    ndi za matamando anu tsiku lonse.

Eksodo 35:1-29

Malamulo Osunga Sabata

35 Mose anasonkhanitsa gulu lonse la Aisraeli ndipo anawawuza kuti, “Zinthu zimene Yehova wakulamulirani kuti muzichite ndi izi: Muzigwira ntchito zanu pa masiku asanu ndi limodzi, koma tsiku la chisanu ndi chiwiri likhale la Sabata, tsiku lanu lopuma, lopatulika kwa Yehova. Aliyense amene adzagwira ntchito iliyonse pa tsikuli ayenera kuphedwa. Pa tsiku la Sabata musakoleze moto paliponse pamene mukhala.”

Zopereka ku Malo Opatulika

Mose ananena kwa gulu lonse la Aisraeli kuti, “Zimene Yehova wakulamulirani ndi izi: Kuchokera pa zomwe muli nazo, mutenge chopereka cha Yehova. Aliyense amene ali ndi mtima wofuna kupereka abweretse kwa Yehova zopereka izi: Golide, siliva ndi mkuwa; nsalu zobiriwira, zapepo, zofiira, nsalu zofewa; ubweya wambuzi; zikopa za nkhosa zazimuna za utoto wofiira ndi zikopa za akatumbu; matabwa amtengo wa mkesha, mafuta anyale a olivi, zonunkhiritsa mafuta odzozera ndi zopangira lubani wonunkhira; miyala yokongola ya mtundu wa onikisi ndi ina yabwino yoyika pa Efodi ndi pa chovala cha pachifuwa.

10 “Anthu onse aluso pakati panu abwere ndi kupanga zonse zimene Yehova walamula: 11 Chihema ndi tenti yake ndiponso chophimba chake, ngowe zake, maferemu ake, mitanda yake, mizati yake ndi matsinde ake; 12 Bokosi la Chipangano pamodzi ndi mitengo yake yonyamulira ndiponso chovundikira chake cha bokosilo ndi nsalu zophimba bokosilo; 13 tebulo pamodzi ndi mitengo yake yonyamulira pamodzi ndi zipangizo zake zonse ndiponso buledi wokhala pamaso pa Yehova; 14 choyikapo nyale yowunikira pamodzi ndi zipangizo zake, nyale ndi mafuta anyalezo; 15 guwa lofukizira lubani pamodzi ndi mitengo yake yonyamulira, mafuta odzozera ndi lubani onunkhira; nsalu yotchinga pa khomo lolowera mʼchihema; 16 guwa lansembe yopsereza pamodzi ndi sefa yamkuwa, mitengo yake yonyamulira ndi zipangizo zake zonse, beseni losambira lamkuwa ndi miyendo yake; 17 nsalu yotchingira bwalo pamodzi ndi mizati yake ndi matsinde ake, ndiponso nsalu yotchingira pa khomo lolowera ku bwalo; 18 zikhomo za tenti ya chihema ndiponso za bwalo, ndi zingwe zake; 19 zovala zolukidwa zovala potumikira kumalo opatulika, zovala zopatulika za wansembe, Aaroni pamodzi ndi za ana ake aamuna pamene akutumikira monga ansembe.”

20 Kenaka gulu lonse la Aisraeli linachoka pamaso pa Mose, 21 ndipo aliyense amene anakhudzidwa mu mtima mwake nafuna kupereka, anabwera kudzapereka chopereka kwa Yehova cha ntchito yokonza tenti ya msonkhano, cha ntchito zonse za mʼtentimo ndi cha zovala zopatulika. 22 Onse amene anali ndi mtima wofuna, amuna ndi amayi omwe anabwera kudzapereka zodzikometsera zagolide za mtundu uliwonse: zomangira zovala, ndolo, mphete ndi zokometsera. Onse anapereka golide wawo monga nsembe yoweyula pamaso pa Yehova. 23 Aliyense amene anali ndi nsalu ya mtundu wa mtambo, yapepo kapena yofiira kapena yofewa, yosalala, kapena ubweya wambuzi, zikopa za nkhosa zonyika mu utoto wofiira kapena zikopa anazibweretsa. 24 Onse amene anapereka chopereka cha siliva kapena mkuwa anabweretsa monga chopereka kwa Yehova. Ndipo aliyense amene anali ndi matabwa a mtengo wa mkesha kuti awagwiritse ntchito mbali ina iliyonse ya ntchitoyo, anabweretsa. 25 Mayi aliyense waluso analuka ndi manja ake ndi kubweretsa chomwe analuka cha mtundu wa mtambo, chapepo kapena chofiira kapena chofewa, chosalala. 26 Ndipo amayi onse amene anali ndi mtima wofuna ndipo anali ndi luso analuka ubweya wa mbuzi. 27 Atsogoleri anabweretsa miyala ya onikisi ndi miyala yokongola yoyika pa efodi ndi chovala chapachifuwa. 28 Anabweretsanso zonunkhiritsa ndiponso mafuta owunikira a olivi ndi odzozera ndi zofukizira zonunkhira. 29 Aisraeli onse aamuna ndi aakazi amene anali ndi mtima wofuna, anabweretsa kwa Yehova chopereka chaufulu ku ntchito yonse ya Yehova imene analamulira kudzera mwa Mose kuti achite.

Machitidwe a Atumwi 10:9-23

Masomphenya a Petro

Mmawa mwake, nthawi ili ngati 12 koloko anthuwo atayandikira mzindawo, Petro anakwera pa denga kukapemphera. 10 Iye anamva njala ndipo anafuna chakudya, ndipo akukonza chakudyacho, iye anachita ngati wakomoka. 11 Iye anaona kuthambo kutatsekuka, ndi chinthu china chikutsitsidwa pansi chooneka ngati chinsalu chachikulu chomangidwa pa msonga zake zinayi. 12 Mʼmenemo munali nyama zonse zamiyendo inayi pamodzinso ndi zokwawa za dziko lapansi ndiponso mbalame zamlengalenga. 13 Petro anamva mawu akuti, “Petro, dzuka, ipha nudye.”

14 Petro anayankha kuti, “Ayi, Ambuye! Ine sindinadyepo kanthu kosayeretsedwa kapena konyansa.”

15 Petro anamvanso kachiwiri mawu akuti, “Usachiyese chonyansa chimene Mulungu wachiyeretsa.”

16 Zimenezi zinachitika katatu ndipo nthawi yomweyo chinsalu chija chinatengedwanso kupita kumwamba.

17 Petro akuganizira za tanthauzo la masomphenyawo, anthu amene Korneliyo anawatuma anapeza kumene kunali nyumba ya Simoni ndipo anayima pa chipata. 18 Iwo anayitana nafunsa ngati Simoni amene amadziwika ndi dzina loti Petro amakhala kumeneko.

19 Petro akuganizirabe za masomphenyawo, Mzimu Woyera anati kwa iye, “Simoni, anthu atatu akukufunafuna. 20 Dzuka, tsika. Usakayike upite nawo pakuti ndawatuma ndine.”

21 Petro anatsika ndipo anati kwa anthuwo, “Amene mukufunayo ndine. Mwabwera kuno chifukwa chiyani?”

22 Anthuwo anayankha kuti, “Ife tachokera kwa Korneliyo, mkulu woyangʼanira asilikali 100. Iye ndi munthu wolungama ndiponso woopa Mulungu, amene amalemekezedwa ndi Ayuda onse. Mngelo woyera anamuwuza kuti mupite ku nyumba yake kuti akamve mawu amene inu mukanene.” 23 Pamenepo Petro anawalowetsa mʼnyumba ndipo anawasamala ngati alendo ake. Mmawa mwake Petro ananyamuka napita nawo ndipo abale ena a ku Yopa anapita naye pamodzi.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.