Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 99

99 Yehova akulamulira,
    mitundu ya anthu injenjemere;
Iye wakhala pa mpando wake waufumu, pakati pa akerubi,
    dziko lapansi ligwedezeke.
Mʼziyoni wamkulu ndi Yehova;
    Iye ndi wokwezeka pamwamba pa mitundu yonse ya anthu.
Anthu atamande dzina lanu lalikulu ndi loopsa kwambiri,
    Iye ndi woyera.

Mfumu yamphamvu, iyo imakonda chilungamo
    Inu mwakhazikitsa khalidwe losakondera;
mwachita zolungama ndi zoyenera mwa Yakobo.
Kwezani Yehova Mulungu wathu
    ndipo mulambireni pa mapazi ake;
    Iye ndi woyera.

Mose ndi Aaroni anali ena mwa ansembe ake,
    Samueli anali pamodzi ndi iwo amene anayitana pa dzina lake;
iwo anayitana Yehova
    ndipo Iyeyo anawayankha.
Iye anayankhula nawo kuchokera mʼchipilala cha mtambo;
    iwo anasunga malamulo ake ndi zophunzitsa zomwe anawapatsa.

Inu Yehova Mulungu wathu,
    munawayankha iwo;
Inu kwa Israeli munali Mulungu wokhululuka,
    ngakhale munawalanga pa zochita zawo zoyipa.
Kwezani Yehova Mulungu wathu
    ndipo mumulambire pa phiri lake loyera,
    pakuti Yehova Mulungu wathu ndi woyera.

Deuteronomo 9:1-5

Osati Chifukwa cha Kulungama kwa Israeli

Mvera Israeli. Watsala pangʼono kuwoloka Yorodani ndi kukathamangitsa mitundu ikuluikulu ndi yamphamvu kuposa iweyo, imene mizinda yake ndi ikuluikulu yokhala ndi makoma ofika mpaka kumwamba. Anthuwo ndi ataliatali, Aanaki! Ukudziwa za iwo ndipo unamvapo zikunenedwa kuti, “Ndani amene angalimbane ndi Aanaki?” Koma khulupirira lero kuti Yehova Mulungu wako amene ali patsogolo pako ali ngati moto wonyeketsa. Adzawononga iwowo ndipo adzawagonjetsa iweyo ukuona. Pamenepo udzawathamangitsa ndi kuwakantha mwamsanga, monga momwe Yehova wakulonjezera.

Yehova Mulungu wako akadzawapirikitsa pamaso pako, usadzanene mu mtima mwako kuti, “Yehova wandibweretsa kuno kudzalanda dziko lino chifukwa cha kulungama kwanga.” Ayi, koma ndi chifukwa cha kuyipa kwa anthu amene Yehova ati awapirikitse pamaso pako. Sukalowa ndi kutenga dziko lawolo chifukwa cha kulungama kwako kapena kukhulupirika kwako koma chifukwa cha kuyipa kwa anthuwo. Yehova Mulungu wako awapirikitsa pamaso pako kuti akwaniritse zimene analumbira kwa makolo ako Abrahamu, Isake ndi Yakobo.

Machitidwe a Atumwi 3:11-16

Petro Ayankhula kwa Anthu

11 Wopempha uja akuyenda pamodzi ndi Petro ndi Yohane, anthu onse anadabwa ndipo anawathamangira iwo kumalo wotchedwa Khonde la Solomoni. 12 Petro ataona zimenezi anawawuza kuti, “Inu Aisraeli, chifukwa chiyani mukudabwa ndi zimene zachitikazi? Bwanji mukuyangʼana ife ngati kuti tamuyendetsa munthuyu ndi mphamvu yathu kapena chifukwa cha kupembedza kwathu? 13 Mulungu wa Abrahamu, Isake ndi Yakobo, Mulungu wa makolo athu, wamulemekeza mtumiki wake Yesu. Amene inu munamukana pamaso pa Pilato ndi kumupereka Iye kuti aphedwe, ngakhale kuti Pilato anafuna kuti amumasule. 14 Koma inu munamukana Woyera ndi Wolungamayo ndipo munapempha kuti akumasulireni munthu wakupha anthu. 15 Inu munapha mwini moyo, koma Mulungu anamuukitsa kwa akufa. Ife ndife mboni za zimenezi. 16 Mwachikhulupiriro mʼdzina la Yesu, munthu uyu amene mukumuona ndi kumudziwa analimbikitsidwa. Mʼdzina la Yesu ndi chikhulupiriro chimene chili mwa iye chamuchiritsa kwathunthu, monga nonse mukuona.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.