Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Nyimbo ya Mariya
46 Ndipo Mariya anati:
“Moyo wanga ulemekeza Ambuye.
47 Ndipo mzimu wanga ukondwera mwa Mulungu Mpulumutsi wanga,
48 pakuti wakumbukira
kudzichepetsa kwa mtumiki wake.
Kuyambira tsopano mibado yonse idzanditcha wodala,
49 pakuti Wamkuluyo wandichitira ine zinthu zazikulu,
dzina lake ndi loyera.
50 Chifundo chake chifikira kwa iwo amene amuopa Iye
kufikira mibadomibado.
51 Iye wachita zamphamvu ndi dzanja lake;
Iye anabalalitsa iwo amene ali onyada mʼmaganizo awo.
52 Iye anachotsa olamulira pa mipando yawo yaufumu,
koma wakweza odzichepetsa.
53 Iye wakhutitsa a njala ndi zinthu zabwino
koma anachotsa olemera wopanda kanthu.
54 Iye anathandiza mtumiki wake Israeli,
pokumbukira chifundo chake.
55 Kwa Abrahamu ndi zidzukulu zake ku nthawi zonse
monga ananena kwa makolo athu.”
Banja la Elikana
1 Panali munthu wina wochokera ku Ramataimu, Mzofimu wa ku dziko la mapiri la Efereimu. Iyeyu dzina lake anali Elikana ndipo anali mwana wa Yerohamu, mwana wa Elihu, mwana wa Tohu, mwana wa Zufu wa fuko la Efereimu. 2 Iye anali ndi akazi awiri, Hana ndi Penina. Penina anali ndi ana, koma Hana analibe.
3 Chaka ndi chaka Elikana ankachoka ku mudzi kwawo kupita ku Silo kukapembedza ndi kukapereka nsembe kwa Yehova Wamphamvuzonse. Ku Siloko kunali ana awiri a Eli, Hofini ndi Finehasi amene anali ansembe a Yehova. 4 Tsiku lopereka nsembe likafika Elikana amapereka magawo a nsembeyo kwa mkazi wake Penina ndi kwa ana ake onse aamuna ndi aakazi. 5 Ngakhale ankamukonda Hana, koma ankamupatsa gawo limodzi popeza Yehova sanamupatse ana. 6 Tsono popeza Yehova sanamupatse Hana ana, mkazi mnzakeyo ankamuyamba dala ndi cholinga chomukwiyitsa. 7 Izi zimachitika chaka ndi chaka. Hana ankati akamapita ku Nyumba ya Yehova mkazi mnzakeyo ankamunyogodola. Choncho Hana ankangokhalira kulira osafuna ndi kudya komwe. 8 Tsono mwamuna wake Elikana ankamufunsa kuti, “Hana ukulira chifukwa chiyani? Wakhumudwa ndi chiyani kuti sukufuna ndi kudya komwe? Kodi ine kwa iwe sindili woposa ana aamuna khumi?”
9 Tsiku lina atatha kudya ndi kumwa ku Silo kuja, Hana anayimirira kukapemphera. Nthawiyi nʼkuti wansembe Eli atakhala pa mpando pa khomo la Nyumba ya Yehova. 10 Hana anavutika mʼmoyo mwake, ndipo anapemphera kwa Yehova akulira kwambiri. 11 Ndipo iye analumbira kuti, “Inu Yehova Wamphamvuzonse, ngati muyangʼana kusauka kwa mtumiki wanune, ndi kuyankha pemphero langa osandiyiwala ine mtumiki wanu pondipatsa mwana wamwamuna, ine ndidzamupereka mwanayo kwa inu Yehova masiku onse a moyo wake. Lumo silidzapita pa mutu pake.”
12 Akupemphera choncho kwa Yehova, Eli ankamuyangʼana pakamwa. 13 Hana ankapemphera chamumtima ndipo milomo yake inkangogwedera koma mawu ake samamveka. Choncho Eli anaganiza kuti anali ataledzera. 14 Ndipo anamufunsa Hana kuti, “Kodi mukhala chiledzerere mpaka liti? Pitani, ayambe wakuchokani vinyo mwamwayo.”
15 Koma Hana anayankha kuti, “Sichoncho mbuye wanga. Ndakhala ndikumukhuthulira Yehova chisoni changa. Sindinamwe vinyo kapena chakumwa choledzeretsa chilichonse, popeza nthawi yonseyi ndakhala ndikupereka kwa Yehova nkhawa yayikulu ndi mavuto anga. 16 Musaganize kuti mtumiki wanu ndi kukhala mkazi wachabechabe. Ine ndakhala ndi kupereka nkhawa yanga yayikulu ndi zowawa zanga.”
17 Eli anayankha, “Pitani mu mtendere, ndipo Mulungu wa Israeli akupatseni zimene mwamupemphazo.”
18 Hana anati, “Mundikomerebe mtima mtumiki wanune.” Kenaka anachoka nakadya, ndipo sanaonekenso wachisoni.
Kupembedza mʼTenti ya Dziko Lapansi
9 Pangano loyamba lija linali ndi malamulo okhudza chipembedzo, ndi malo opembedzeramo omangidwa ndi anthu. 2 Anthu ankamanga chihema. Mʼchipinda choyamba munali choyikapo nyale, tebulo ndi buledi woperekedwa kwa Mulungu. Chipinda chimenechi chinkatchedwa Malo Opatulika. 3 Kuseri kwa chinsalu chotchinga chachiwiri kunkatchedwa Malo Opatulika kwambiri. 4 Mʼmenemo munali guwa lansembe lagolide lofukizirapo lubani. Munalinso Bokosi la Chipangano lokutidwa ndi golide. Mʼbokosimo munali mʼphika wagolide mʼmene ankasungiramo mana ndi ndodo ya Aaroni imene inaphuka ija, ndiponso miyala ya pangano. 5 Pamwamba pa bokosilo panali zifanizo za angelo otchedwa akerubi aulemerero, ataphimba chivundikiro cha bokosilo chimene chinali malo okhululukirapo machimo. Koma nʼzosatheka tsopano kufotokoza zinthu mwatsatanetsatane.
6 Zinthu zonsezi zitakonzedwa, ansembe ankalowamo mʼchipinda choyamba chija nthawi ndi nthawi kumatumikiramo. 7 Koma Mkulu wa ansembe yekha ndiye ankalowa chipinda chachiwiri chija kamodzi kokha pa chaka. Iye sankalowamo wopanda magazi. Magaziwo ankapereka nsembe kwa Mulungu chifukwa cha iye mwini ndiponso chifukwa cha machimo a anthu amene ankachita mosazindikira. 8 Mwa njira imeneyi Mzimu Woyera ankaonetsa kuti njira yolowera ku malo opatulika inali isanaonetsedwe pamene Chihema choyamba chinali chilipo. 9 Zimenezi nʼzofanizira chabe, ndipo zinkalozera nthawi ino, kusonyeza kuti mphatso ndi nsembe zimene zinkaperekedwa sizinkachotsa chikumbumtima cha wopembedzayo. 10 Inali nkhani ya zakudya, ya zakumwa ndi ya miyambo yosiyanasiyana ya masambidwe. Anali malamulo akunja kokha mpaka pa nthawi imene anakonzanso zonse mwatsopano.
Magazi a Yesu
11 Koma Khristu atafika monga Mkulu wa ansembe wa zinthu zokoma zimene zilipo tsopano, Iye analowa mʼChihema chachikulu ndiponso changwiro chimene sichinamangidwe ndi munthu, ndiye kuti sichili pansi pano. 12 Iye sanalowemo ndi magazi ambuzi yayimuna, ana angʼombe amphongo, koma analowa Malo Opatulika kamodzi kokha ndi magazi ake, atatikonzera chipulumutso chosatha. 13 Ngati magazi ambuzi yayimuna, angʼombe yayimuna ndi phulusa la mwana wangʼombe wamkazi zimati zikawazidwa pa odetsedwa zimawayeretsa kotero kuti amakhala oyeretsedwa ku thupi, 14 nʼkoposa kotani magazi a Khristu, amene mwa Mzimu wamuyaya anadzipereka yekha kwa Mulungu kukhala nsembe yopanda chilema. Iye adzayeretsa chikumbumtima chathu pochotsa ntchito za imfa, kuti ife titumikire Mulungu wamoyo.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.