Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
2 Samueli 7:1-11

Lonjezo la Mulungu kwa Davide

Mfumu itakhazikika mʼnyumba yake yaufumu, Yehova atayipatsa mpumulo kwa adani ake onse woyizungulira, mfumuyo inawuza mneneri Natani kuti, “Ine pano ndikukhala mʼnyumba yomanga ndi mitengo ya mkungudza, pomwe Bokosi la Mulungu lili mu tenti.”

Natani anayankha mfumu kuti, “Chitani chilichonse chimene chili mu mtima mwanu chifukwa Yehova ali nanu.”

Usiku umenewo mawu a Yehova anafika kwa Natani ndipo anati,

“Pita kamuwuze mtumiki wanga Davide kuti, ‘Yehova akunena kuti: kodi ndiwe amene udzandimangira Ine nyumba yokhalamo? Ine sindinakhalepo mʼnyumba kuyambira tsiku limene ndinatulutsa Aisraeli mʼdziko la Igupto mpaka lero lino. Ndakhala ndikuyenda uku ndi uku ndipo mokhala mwanga munali mu tenti. Konse ndakhala ndikuyenda ndi Aisraeli onse, kodi ndinanenapo kwa wina aliyense atsogoleri awo, amene ndinamulamula kuweta anthu anga Aisraeli kuti, nʼchifukwa chiyani simunandimangire nyumba ya mitengo ya mkungudza?’ ”

“Ndipo tsopano umuwuze mtumiki wanga Davide kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse akuti: Ine ndinakutenga ku busa ukuweta nkhosa kuti ukhale mtsogoleri wa anthu anga Aisraeli. Ineyo ndinali nawe kulikonse kumene unkapita, ndipo ndachotsa adani ako onse pamaso pako. Tsopano ndidzakuza dzina lako kuti likhale mʼgulu la mayina a anthu otchuka kwambiri pa dziko lapansi. 10 Ndipo ndidzawapatsa malo anthu anga Aisraeli ndipo ndidzawadzala pamalo awoawo kuti asadzavutitsidwenso. Anthu oyipa sadzawazunzanso monga ankachitira poyamba paja, 11 monga akhala akuchitira kuchokera nthawi imene ndinasankha atsogoleri a anthu anga Aisraeli. Ine ndidzakupatsaninso mpumulo kwa adani anu onse.

“ ‘Yehova akulengeza kwa iwe kuti Iye mwini adzakhazikitsa banja lako:

2 Samueli 7:16

16 Nyumba yako ndi ufumu wako zidzakhala zamuyaya pamaso panga. Mpando wako waufumu udzakhazikika kwamuyaya!’ ”

Luka 1:46-55

Nyimbo ya Mariya

46 Ndipo Mariya anati:

“Moyo wanga ulemekeza Ambuye.
47     Ndipo mzimu wanga ukondwera mwa Mulungu Mpulumutsi wanga,
48 pakuti wakumbukira
    kudzichepetsa kwa mtumiki wake.
Kuyambira tsopano mibado yonse idzanditcha wodala,
49     pakuti Wamkuluyo wandichitira ine zinthu zazikulu,
    dzina lake ndi loyera.
50 Chifundo chake chifikira kwa iwo amene amuopa Iye
    kufikira mibadomibado.
51 Iye wachita zamphamvu ndi dzanja lake;
    Iye anabalalitsa iwo amene ali onyada mʼmaganizo awo.
52 Iye anachotsa olamulira pa mipando yawo yaufumu,
    koma wakweza odzichepetsa.
53 Iye wakhutitsa a njala ndi zinthu zabwino
    koma anachotsa olemera wopanda kanthu.
54 Iye anathandiza mtumiki wake Israeli,
    pokumbukira chifundo chake.
55 Kwa Abrahamu ndi zidzukulu zake ku nthawi zonse
    monga ananena kwa makolo athu.”

Masalimo 89:1-4

Ndakatulo ya Etani, wa banja la Ezara.

89 Ndidzayimba za chikondi chachikulu cha Yehova kwamuyaya;
    ndi pakamwa panga ndidzachititsa kuti kukhulupirika kwanu kudziwike ku mibado yonse.
Ndidzalalikira kuti chikondi chanu chidzakhazikika mpaka muyaya,
    kuti Inu munakhazikitsa kukhulupirika kwanu kumwamba kwenikweniko.

Inu munati, “Ndachita pangano ndi wosankhidwa wanga,
    ndalumbira kwa Davide mtumiki wanga kuti,
‘Ndidzakhazikitsa zidzukulu zako mpaka muyaya.
    Ndidzachititsa kuti mpando wako waufumu ukhazikike ku mibado yonse,’ ”
            Sela.

Masalimo 89:19-26

19 Kale munayankhula mʼmasomphenya,
    kwa anthu anu okhulupirika munati,
“Ndapatsa mphamvu wankhondo;
    ndakweza mnyamata wochokera pakati pa anthu.
20 Ndamupeza mtumiki wanga Davide;
    ndamudzoza ndi mafuta opatulika.
21 Dzanja langa lidzamuchirikiza;
    zoonadi, mkono wanga udzamupatsa mphamvu.
22 Adani sadzamulamula kuti apereke msonkho;
    anthu oyipa sadzamusautsa.
23 Ndidzaphwanya adani ake pamaso pake
    ndi kukantha otsutsana naye.
24 Chikondi changa chokhulupirika chidzakhala naye,
    ndipo kudzera mʼdzina langa nyanga yake idzakwezedwa.
25 Ndidzayika dzanja lake pa nyanja,
    dzanja lake lamanja pa mitsinje.
26 Iyeyo adzafuwula kwa Ine kuti, ‘Ndinu Atate anga,
    Mulungu wanga, Thanthwe ndi Chipulumutso changa.’

Aroma 16:25-27

25 Tsopano kwa Iye amene ali ndi mphamvu yokhazikitsa monga mwa uthenga wanga wabwino ndikulalikidwa kwa Yesu Khristu, monga mwa vumbulutso lachinsinsi chobisika kwa nthawi yayitali, 26 koma tsopano chavumbulutsidwa ndi kudziwika kudzera mʼMalemba a uneneri mwa lamulo la Mulungu wosatha, kuti mitundu yonse ikhulupirire ndi kumvera Iye, 27 kwa Mulungu yekhayo wanzeru kukhale ulemerero kwamuyaya kudzera mwa Yesu Khristu! Ameni.

Luka 1:26-38

Aneneratu za Kubadwa kwa Yesu

26 Mwezi wachisanu ndi chimodzi, Mulungu anatuma mngelo Gabrieli ku Nazareti, mudzi wa ku Galileya, 27 kwa namwali wopalidwa ubwenzi ndi Yosefe, wa fuko la Davide. Dzina la namwaliyo linali Mariya. 28 Mngeloyo anafika kwa iye nati, “Moni, inu amene Ambuye wakukomerani mtima kwambiri! Ambuye ali ndi inu.”

29 Mariya anavutika kwambiri ndi mawu awa ndipo anadabwa ndi kulonjera kotere. 30 Koma mngeloyo anati kwa iye, “Usachite mantha Mariya, pakuti wapeza chisomo pamaso Mulungu. 31 Udzakhala woyembekezera ndipo udzabala mwana wamwamuna ndipo udzamupatse dzina loti Yesu. 32 Iye adzakhala wamkulu ndipo adzatchedwa Mwana wa Wammwambamwamba. Ambuye Mulungu adzamupatsa Iye mpando waufumu wa abambo ake Davide, 33 ndipo adzalamulira pa nyumba ya Yakobo ku nthawi zonse; ufumu wake sudzatha.”

34 Mariya anafunsa mngeloyo kuti, “Izi zingatheke bwanji popeza ine sindidziwa mwamuna?”

35 Mngelo anayankha kuti, “Mzimu Woyera adzabwera pa iwe ndipo mphamvu ya Wammwambamwamba idzakuphimba, ndipo Woyerayo amene adzabadwe adzatchedwa Mwana wa Mulungu. 36 Ngakhale Elizabeti mʼbale wako adzakhala ndi mwana mu ukalamba wake ndipo iye amene amati ndi wosabereka, uno mwezi wake wachisanu ndi chimodzi. 37 Pakuti palibe chinthu chosatheka ndi Mulungu.”

38 Mariya anayankha kuti, “Ine ndine mtumiki wa Ambuye. Zikhale kwa ine monga mwanenera.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.