Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Old/New Testament

Each day includes a passage from both the Old Testament and New Testament.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Estere 3-5

Chiwembu cha Hamani Chopha a Yuda

Zitachitika izi, mfumu Ahasiwero anamukweza Hamani mwana wa Hamedata Mwagagi, anamulemekeza ndikumupatsa mpando wa ulemu kuposa nduna zina zonse. Atumiki onse a mfumu amene anali pa chipata cha nyumba ya mfumu ankagwadira ndi kuweramira Hamani monga mwa lamulo la mfumu. Koma Mordekai sankamugwadira kapena kumuweramira.

Kenaka atumiki a mfumu amene anali pa chipata anafunsa Mordekai kuti, “Kodi nʼchifukwa chiyani sumvera lamulo la mfumu?” Tsiku ndi tsiku ankayankhula naye koma iye sanamverebe. Choncho anamuwuza Hamani kuti aone ngati angavomereze khalidwe lotere la Mordekai, popeza anawawuza kuti anali Myuda.

Hamani ataona kuti Mordekai sankamugwadira kapena kumuweramira, anapsa mtima kwambiri. Hamani atamva kuti Mordekai anali Myuda, anatsimikiza kuti ndi kosakwanira kulanga Mordekai yekha. Mʼmalo mwake anapeza njira yowonongera Ayuda onse okhala mʼdziko lonse limene mfumu Ahasiwero ankalamulira.

Mwezi woyamba, umene ndi mwezi wa Nisani, chaka cha khumi ndi chiwiri cha ufumu wa Ahasiwero anachita maere, otchedwa Purimu pamaso pa Hamani kuti apeze tsiku ndi mwezi woyenera. Ndipo maere anagwera pa mwezi wa khumi ndi chiwiri ndiwo mwezi wa Adara.

Kenaka Hamani anakawuza mfumu Ahasiwero kuti, “Pali mtundu wina wa anthu umene unabalalika ndipo wamwazikana pa mitundu ina mʼzigawo zonse za ufumu wanu umene miyambo yawo ndi yosiyana ndi ya anthu ena onse ndiponso amene safuna kumvera malamulo a mfumu, kotero si chinthu cha phindu kuti mfumu iwalekerere anthu otere. Ngati chingakukomereni mfumu, ikani lamulo kuti tiwawononge, ndipo ndidzalipira matalente 10,000 asiliva mosungiramo chuma cha mfumu za anthu amene adzachite ntchito imeneyi.”

10 Choncho mfumu inavula mphete yodindira ku chala chake ndi kumupatsa Hamani mwana wa Hamedata Mwagagi, mdani wa Ayuda. 11 Mfumu inati kwa Hamani, “Sunga ndalamazo, ndipo uchite ndi anthuwo monga ufunira.”

12 Alembi analemba zonse zimene Hamani analamula mʼmakalata opita kwa akazembe a mfumu, abwanamkubwa a zigawo zonse ndi kwa oyangʼanira mtundu uliwonse wa anthu. Kalatazo zinali za mʼchiyankhulo cha mtundu uliwonse ndipo zinalembedwa mʼdzina la Mfumu Ahasiwero ndi kusindikizidwa ndi mphete yake. 13 Makalatawa anawatumiza amithenga ku zigawo zonse za mfumu kuti awononge, aphe ndi kufafaniziratu a Yuda onse, anyamata, anthu okalamba, ana ndi amayi, pa tsiku limodzi la 13 la mwezi wa Adara ndipo alande katundu wawo. 14 Mwachidule kalatayi inanena kuti mawu olembedwamowo anayenera kuperekedwa ngati lamulo mʼchigawo chilichonse ndi kuti anthu a mtundu uliwonse adziwe ndi kukhala okonzeka pa tsikulo.

15 Potsata lamulo la mfumu, amithenga aja anapita mwachangu ndipo lamuloli linaperekedwanso ku Susa, likulu la dziko. Mfumu ndi Hamani anakhala pansi ndikumamwa, koma mzinda onse wa Susa unasokonezeka.

Mordekai a Pempha Estere kuti Athandize

Mordekai atamva zonse zimene zinachitika, anangʼamba zovala zake, navala chiguduli ndi kudzola phulusa, ndipo analowa mu mzinda, akulira mokweza ndi mowawidwa mtima. Ndipo anapita ndi kuyima pa chipata cha mfumu, chifukwa panalibe wina aliyense amaloledwa kulowa pa chipata cha mfumu atavala chiguduli. Chigawo chilichonse kumene mawu a mfumu ndi lamulo lake zinafika, kunali maliro akulu pakati pa Ayuda. Iwo ankasala zakudya, kulira mofuwula ndi kumadandaula. Ambiri anavala ziguduli ndi kudzola phulusa.

Anamwali otumikira mfumukazi Estere ndi adindo ake ofulidwa atabwera ndi kumuwuza za Mordekai, anavutika kwambiri. Estere anamutumizira zovala kuti avale ndi kuti avule chiguduli chake koma Mordekai sanalole zimenezo. Kenaka Estere anayitana Hataki, mmodzi wa adindo a mfumu ofulidwa amene anayikidwa kuti azimutumikira kuti apite kwa Mordekai kuti akamve chimene chimamuvuta komanso chifukwa chochitira zimenezi.

Choncho Hataki anapita kwa Mordekai ku bwalo la mzinda patsogolo pa chipata cha mfumu. Mordekai anamuwuza zonse zimene zinamuchitikira kuphatikizapo mtengo weniweni wa ndalama zimene Hamani analonjeza kupereka mosungira chuma cha mfumu za anthu amene adzawononge a Yuda. Mordekai anamupatsanso imodzi mwa makalata a ulamuliro wonena za chiwembuchi amene anawasindikiza ku Susa kukamuonetsa ndi kumufotokozera zonse Estere. Anamuwuzanso kuti akamudandaulire kuti akapite kwa mfumu kukapempha chifundo ndi kuyidandaulira chifukwa cha anthu a mtundu wake.

Hataki anabwerera ndi kumufotokozera Estere zimene Mordekai ananena. 10 Ndipo Estere anamutuma Hataki kuti akanene kwa Mordekai kuti, 11 “Atumiki onse amfumu ndi anthu a zigawo za mfumu ankadziwa kuti mwamuna kapena mkazi aliyense akalowa ku bwalo lake la mʼkati mosayitanidwa ndi mfumu pali lamulo limodzi: lamuloli ndi lakuti aphedwe. Zimasintha pokhapokha ngati mfumu iloza munthuyo ndi ndodo yagolide kuti akhale ndi moyo. Koma papita masiku makumi atatu ndisanayitanidwe ndi mfumu.”

12 Tsono Mordekai anawuzidwa mawu a Estere. 13 Kenaka Mordekai anawawuza kuti akamuyankhe Estere motere: “Usaganize kuti iwe wekha mwa Ayuda onse udzapulumuka chifukwa chakuti uli mʼnyumba ya mfumu. 14 Pakuti ngati ukhalatu chete nthawi ino, chithandizo ndi chipulumutso cha Ayuda zidzachokera kwina nʼkutheka kuti iwe ndi a pa banja la makolo ako mudzafa. Ndipo adziwa ndani mwina unalowa ufumu chifukwa cha nthawi ngati imeneyi?”

15 Pamenepo Estere anatumiza yankho ili kwa Mordekai: 16 “Pitani, mukasonkhanitse pamodzi Ayuda onse amene ali mu Susa ndipo mundisalire chakudya. Musadye kapena kumwa kwa masiku atatu, usiku ndi usana. Ine ndi anamwali anga onditumikira tidzasala chakudya monga inu. Izi zikachitika, ine ndidzapita kwa mfumu, ngakhale kutero ndikutsutsana ndi lamulo. Ndipo ngati nʼkufa ndife ndithu.”

17 Choncho Mordekai anapita ndi kuchita monga Estere anamupemphera.

Pempho la Estere kwa Mfumu

Tsiku lachitatu Estere anavala zovala zake zaufumu ndipo anayima mʼbwalo la mʼkati la nyumba yaufumu choyangʼana ku chipinda chachikulu cha mfumu. Mfumu inakhala pa mpando waufumu mʼchipinda chachikulu moyangʼana ku chipata cholowera mʼnyumba yaufumu. Mfumu itaona Estere atayima mʼbwalomo inakondwera naye ndipo anamuloza ndi ndodo yagolide imene inali mʼdzanja lake. Choncho Estere anayandikira ndi kukhudza msonga ya ndodoyo.

Kenaka mfumu inati kwa iye, “Kodi mukufuna chiyani, inu mfumukazi Estere? Nanga pempho lanu ndi chiyani? Ngakhale mutapempha theka la ufumu, ndidzakupatsani.”

Ndipo Estere anayankha kuti, “Ngati chingakukomereni, mfumu, mubwere lero pamodzi ndi Hamani kuphwando limene ndakonzera inu mfumu.”

Mfumu inati, “Muwuzeni abwere Hamani msanga, kotero kuti tichite monga Estere wapempha.”

Choncho mfumu ndi Hamani anafika kuphwando limene Estere anakonza. Akumwa vinyo, mfumu inamufunsano Estere kuti, “Kodi ukupempha chiyani tsopano? Chimene uti upemphe ndikupatsa. Chopempha chako ndi chiti? Ngakhale utafuna mpaka theka la ufumu, ndidzakupatsa.”

Estere anayankha kuti, “Pempho langa ndi chofuna changa ndi ichi: Ngati mwandikomera mtima mfumu ndiponso ngati chingakukondweretseni mfumu kundipatsa chimene ndapempha ndi kuchita zimene ndifuna, mubwere mawa inu mfumu ndi Hamani ku phwando limene ndidzakukonzerani. Ndipo ndidzakuyankhani mfumu funso lanu.”

Mkwiyo wa Hamani Ukulabe pa Mordekai

Tsiku limenelo Hamani anatuluka wokondwa ndi wosangalala kwambiri. Koma ataona Mordekai pa chipata cha mfumu ndi kuti sanayimirire kapena kumupatsa ulemu pamene iye amadutsa, Hamani anamukwiyira kwambiri, 10 komabe Hamani anadziletsa ndipo anapita ku nyumba kwake.

Anayitana abwenzi ake pamodzi ndi mkazi wake Zeresi. 11 Hamani anawawuza za kuchuluka kwa chuma chake ndi kuti anali ndi ana aamuna ambiri. Anawawuzanso za mmene mfumu inamukwezera ndi kumuyika kukhala woposa nduna ndi olemekezeka onse. 12 Hamani anawonjeza kuti, “Ndipotu si zokhazi. Ndine ndekha amene ndayitanidwa pamodzi ndi mfumu kuphwando limene mfumukazi Estere anatikonzera. Ndipo mawa wandiyitananso pamodzi ndi mfumu. 13 Koma zonsezi sindikhutira nazo ndikamaona nthawi zonse Myuda uja Mordekai atakhala pa chipata cha mfumu.”

14 Mkazi wake Zeresi ndi abwenzi ake onse aja anamuwuza kuti, “Anthu apange mtanda wotalika mamita 23 ndipo mmawa upemphe mfumu kuti anthu akhomerepo Mordekai. Kenaka upite ndi mfumu kuphwando mokondwa.” Hamani anakondwera ndi uphungu umenewu ndipo mtanda unapangidwa.

Machitidwe a Atumwi 5:22-42

22 Koma alonda aja atafika kundende, sanawapezemo. Iwo anabwerera nakawafotokozera 23 kuti, “Tinakapeza ndende ili chitsekere ndithu, ndi alonda atayimirira pa khomo, koma pamene tinatsekula zitseko, sitinapezemo munthu aliyense mʼkatimo.” 24 Mkulu wa alonda a Nyumba ya Mulungu ndi akulu a ansembe atamva zimenezi anathedwa nzeru, osadziwa kuti zimenezi zidzatha bwanji.

25 Ndipo wina anabwera ndi kuti, “Taonani! Anthu aja amene munawatsekera mʼndende ali ku Nyumba ya Mulungu ndipo akuphunzitsa anthu.” 26 Pamenepo mkulu wa alonda pamodzi ndi alonda anakawatenga atumwi. Sanakawatenge mwaukali, chifukwa amaopa kuti anthu angawaponye miyala.

27 Atafika nawo atumwi aja, anawayimika pamaso pa Bwalo Lalikulu kuti afunsidwe mafunso ndi mkulu wa ansembe. 28 Iye anati, “Ife tinakuletsani kuti musaphunzitsenso mʼdzina ili, koma inu mwadzaza Yerusalemu ndi chiphunzitso chanu, ndipo mukufuna kutisenzetsa imfa ya munthu ameneyu.”

29 Petro ndi atumwi enawo anayankha kuti, “Ife tiyenera kumvera Mulungu osati anthu! 30 Mulungu wa makolo athu anamuukitsa Yesu, amene inu munamupha pomupachika pa mtengo. 31 Mulungu anamukweza Iye ku dzanja lake lamanja kukhala Mfumu ndi Mpulumutsi kuti Iye apatse Aisraeli mtima wolapa ndi chikhululukiro cha machimo. 32 Ife ndife mboni za zimenezi, ndiponso Mzimu Woyera amene Mulungu anapereka kwa iwo akumvera Iye.”

33 Akuluakuluwo atamva zimenezi anakwiya kwambiri nafuna kuwapha. 34 Koma Mfarisi wina dzina lake Gamalieli, mphunzitsi wa malamulo, amene anthu onse amamulemekeza, anayimirira ndi kulamula kuti atumwiwo ayambe apita panja. 35 Ndipo iye anawuza bwalolo kuti, “Aisraeli, taganizani bwino, zimene mukufuna kuchita kwa anthu awa. 36 Pakuti masiku a mʼmbuyomu kunali Teuda amene anadzitchukitsa, ndipo anthu pafupifupi 400 anamutsatira. Iye anaphedwa ndipo omutsatira akewo anabalalitsidwa, zonse zinatheratu. 37 Pambuyo pake, nthawi ya kalembera kunalinso Yudasi wa ku Galileya, ndipo anatsogolera gulu la anthu amene anawukira, iyenso anaphedwa ndipo anthu ake onse anabalalitsidwa. 38 Chifukwa chake pa nkhani iyi ndikuwuzani kuti, alekeni anthuwa ndipo aloleni apite! Pakuti ngati zimene akuganiza kapena kuchita ndi zochokera kwa munthu zidzalephera. 39 Koma ngati ndi zochokera kwa Mulungu inu simudzatha kuwaletsa anthu awa: inu mwina muzapezeka kuti mukulimbana ndi Mulungu.”

40 Akuluakulu enawo anavomerezana naye. Iwo anayitana atumwi aja ndipo anawakwapula kwambiri. Ndipo anawalamula kuti asayankhulenso mʼdzina la Yesu ndipo anawamasula.

41 Iwo anachoka ku Bwalo Lalikulu akukondwa chifukwa anayesedwa oyenera kunyozedwa chifukwa cha dzina la Yesu. 42 Ndipo tsiku ndi tsiku, sanaleke kuphunzitsa ndi kulalikira mʼNyumba ya Mulungu komanso nyumba ndi nyumba, Uthenga Wabwino wa kuti Yesu ndi Khristu.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.