Old/New Testament
Kumangidwanso kwa Guwa la Nsembe
3 Utafika mwezi wa chisanu ndi chiwiri Aisraeli atakhala kale mʼmidzi yawo, anthu anasonkhana ku Yerusalemu ndi cholinga chimodzi. 2 Kenaka Yesuwa mwana wa Yozadaki ndi ansembe anzake pamodzi ndi Zerubabeli mwana wa Sealatieli ndi abale ake anayamba kumanga guwa lansembe la Mulungu wa Israeli. Anatero pofuna kuti aziperekapo nsembe zopsereza monga analembera mʼbuku la Mose, munthu wa Mulungu uja. 3 Ndi mantha ndi mantha chifukwa cha anthu a mʼmayikomo, iwo anamanga guwalo pa maziko ake akale, ndipo anapereka nsembe zopsereza kwa Mulungu pa guwapo mmawa ndi madzulo. 4 Ankasunga tsiku la chikondwerero cha misasa monga momwe zinalembedwera. Ankaperekanso nsembe za tsiku ndi tsiku monga mwa chiwerengero chake potsata mwambo wake wa tsiku ndi tsiku monga zinalembedwa. 5 Pambuyo pake, ankapereka nsembe zopsereza, nsembe zopereka pa nthawi ya mwezi watsopano ndi za pa masiku onse a chikondwerero oyikidwa kutamandira Yehova, kudzanso nsembe zaufulu zopereka kwa Yehova. 6 Kuyambira pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiwiri, iwo anayambanso kupereka nsembe zopsereza kwa Yehova, ngakhale kuti maziko a Nyumba ya Yehova anali asanamangidwe.
Kumangidwanso kwa Nyumba ya Mulungu
7 Ndipo anapereka ndalama kwa amisiri a miyala ndi kwa amisiri a matabwa, ndi chakudya, chakumwa ndi mafuta kwa anthu a ku Sidoni ndi a ku Turo, kuti abweretse mitengo ya mkungudza pa nyanja kuchokera ku Lebanoni mpaka ku Yopa. Zonsezi anachita malinga ndi chilolezo chimene analandira kuchokera kwa Koresi, mfumu ya Peresiya.
8 Tsono mu chaka chachiwiri atabwera ku Yerusalemu, ku malo akale a Nyumba ya Yehova, mwezi wachiwiri Zerubabeli mwana wa Sealatieli, Yesuwa mwana wa Yozadaki pamodzi ndi abale awo onse, ansembe, Alevi ndi onse amene anabwera ku Yerusalemu kuchokera ku ukapolo, anayamba kugwira ntchito. Iwo anasankha Alevi a zaka zoyambira makumi awiri kuti aziyangʼanira ntchito ya kumanga Nyumba ya Yehova. 9 Yesuwa ndi ana ake aamuna kudzanso abale ake, Kadimieli ndi ana ake (ana a Yuda) onse pamodzi anasenza udindo woyangʼanira antchito ku Nyumba ya Mulungu, kuphatikizanso ana a Henadadi komanso Alevi, ana awo ndi abale awo.
10 Amisiri omanga nyumba atamanga maziko a Nyumba ya Yehova, ansembe anabwera akuyimba malipenga, atavala zovala zaunsembe. Ndipo Alevi, zidzukulu za Asafu, anadza akuyimba matambolini ndi kutenga udindo wawo wotamanda Yehova, potsata malangizo a Davide mfumu ya Aisraeli. 11 Iwo ankayimba motamanda ndi mothokoza Yehova nyimbo iyi:
“Yehova ndi wabwino;
chikondi chake pa Israeli ndi chamuyaya.”
Ndipo anthu onse ankafuwula kwambiri kumutamanda Yehova, chifukwa maziko a Nyumba ya Yehova anali kumangidwa. 12 Koma ambiri mwa ansembe, Alevi ndiponso atsogoleri amabanja, akuluakulu amene anaona Nyumba ya Yehova yakale, analira mokweza pamene anaona maziko a nyumbayi akumangidwa. Komanso ena ambiri ankafuwula mosangalala. 13 Choncho panalibe amene ankatha kusiyanitsa liwu lofuwula mokondwerera ndi liwu la anthu olira, chifukwa anthuwo ankafuwula kwambiri. Ndipo liwu lofuwulalo limamveka kutali.
Atsutsa za Kumanganso Nyumba ya Yehova
4 Adani a Yuda ndi Benjamini anamva kuti anthu obwera ku ukapolo aja akumangira Nyumba Yehova, Mulungu wa Israeli. 2 Tsono anapita kwa Zerubabeli ndi kwa atsogoleri a mabanja awo ndi kunena kuti, “Mutilole kuti tikuthandizeni kumangaku chifukwa ife timapembedza Mulungu wanu monga momwe mumachitira inu, ndipo takhala tikupereka nsembe kwa Iye kuyambira nthawi ya Esrahadoni, mfumu ya ku Asiriya, amene anabwera nafe kuno.”
3 Koma Zerubabeli, Yesuwa ndi atsogoleri ena otsala a mabanja a Aisraeli anayankha kuti, “Inu simungatithandize kumangira Nyumba Yehova, Mulungu wathu. Tokha tidzamumangira Nyumba Yehova, Mulungu wa Aisraeli, monga mfumu Koresi, mfumu ya Perisiya inatilamulira.”
4 Tsono anthu a mʼdzikomo anayamba kuchititsa ulesi anthu a ku Yuda, ndi kuwachititsa mantha kuti aleke ntchito yomangayo. 5 Analemba alangizi ena kuti alepheretse cholinga chawo pa ntchitoyo pa nthawi yonse ya Koresi, mfumu ya ku Perisiya, ndiponso mpaka pamene Dariyo mfumu ya ku Perisiya ankalamulira dzikolo.
Kutsutsa Kwina pa Nthawi ya Ahasiwero ndi Aritasasita
6 Mfumu Ahasiwero atangoyamba kulamulira dzikolo, adani aja analemba kalata yoneneza anthu a Yuda ndi Yerusalemu.
7 Ndiponso mʼnthawi ya Aritasasita mfumu ya Perisiya, Bisilamu, Mitiredati, Tabeeli ndi anzawo ena analemba kalata inanso kwa Aritasasita. Kalatayo inalembedwa mʼChiaramu ndipo ankatanthauzira poyiwerenga.
8 Rehumu mkulu wankhondo ndi Simisai mlembi, nawonso analemba kalata yawo yoneneza anthu a ku Yerusalemu kwa mfumu Aritasasita. Anayilemba motere:
9 Kalata yochokera kwa Rehumu, mkulu wa gulu lankhondo, mlembi Simisai ndi anzawo awa: oweruza, nduna, akuluakulu ena, anthu a ku Peresiya, Ereki, Babuloni, Susa mʼdziko la Elamu, 10 ndi mitundu ina imene mkulu wolemekezeka, Osanipara anayisamutsa ndi kuyikhazika mʼmizinda ya Samariya ndi mʼmadera ena apatsidya la Yufurate.
11 Mawu a mʼkalata ya kwa Aritasasita anali awa:
Kwa mfumu Aritasasita:
Kuchokera kwa atumiki anu, anthu a kutsidya kwa Yufurate:
12 Amfumu tati mudziwe kuti Ayuda amene anabwera kuno kuchokera kwanuko apita ku Yerusalemu ndipo akumanganso mzinda wa anthu owukira ndi oyipa uja. Akumaliza makoma ake ndipo akukonzanso maziko.
13 Kuwonjeza apo amfumu mudziwe kuti ngati amalize kumanganso mzindawu ndi kukonzanso makoma ake, adzaleka kukhoma msonkho, kulipira ndalama zakatundu olowa mʼdziko kapena msonkho wina uliwonse, ndipo chuma cha thumba la ufumu chidzachepa. 14 Popeza tsono ife timadya nawo kwa mfumu sitiyenera tizingoonerera zinthu zochititsa mfumu manyazi. Nʼchifukwa chake tikutumiza uthenga kwa inu a mfumu kuti mudziwe zonse. 15 Choncho pachitike kafukufuku mʼbuku la mbiri yakale ya makolo anu. Mʼbuku la mbiri zakale mudzapezamo ndi kuwerenga kuti mzinda umenewu ndi waupandu, wosautsa mafumu ndi nduna zamʼmadera zomwe. Kuyambira kale wakhala ukuwukira ulamuliro uliwonse. Nʼchifukwa chake mzinda umenewu anawuwononga. 16 Tsono tikukudziwitsani amfumu kuti ngati mzinda umenewu umangidwanso ndi makoma ake nʼkutsirizidwanso ndiye kuti inu simudzalamuliranso chigawo cha patsidya pa Yufurate.
17 Mfumu inatumiza yankho ili:
Mkulu wa gulu lankhondo Rehumu, mlembi Simisai ndi anzanu onse amene akukhala ku Samariya ndi mʼzigawo zina zonse za Patsidya pa Yufurate.
Landirani moni.
18 Kalata imene munatumiza ija yawerengedwa bwino lomwe pamaso panga. 19 Ine nditalamula kuti afufuze nkhaniyi kwapezekadi kuti mzinda umenewu uli ndi mbiri yowukira mafumu ndi kuti zaupandu ndi zowukira zinkachitikadi mʼmenemo. 20 Mafumu amphamvu akhala akulamulira Yerusalemu ndi chigawo chonse cha Patsidya pa Yufurate. Iwo ankalandira msonkho ndi kulipira ndalama zakatundu olowa mʼdziko pa kanthu kena kalikonse. 21 Tsopano inu khazikitsani lamulo kuti anthu amenewo asiye ntchitoyo, asamangenso mzindawo mpaka ine nditalamula 22 Musachedwe kuchita zimenezi. Kodi ine ndingalole bwanji kuti zowononga zotere zikule ndi kupweteka ine mfumu?
23 Kalata ya mfumu Aritasasitayi itangowerengedwa pamaso pa Rehumu ndi Simisai mlembi uja, ndi anzawo onse, iwo anapita msangamsanga ku Yerusalemu kukawaletsa Ayuda aja mwamphamvu kuti asapitirire ntchito yawo.
24 Motero ntchito yomanga Nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu inayimitsidwa mpaka chaka cha chiwiri cha ulamuliro wa Dariyo mfumu ya ku Perisiya.
Kalata ya Tatenai Yopita kwa Dariyo
5 Nthawi imeneyo aneneri Hagai ndi Zekariya, mwana wa Ido, ankayankhula kwa Ayuda okhala mʼdziko la Yuda ndi mu Yerusalemu mʼdzina la Mulungu wa Israeli, amene anali nawo. 2 Pambuyo pake Zerubabeli mwana wa Sealatieli ndi Yesuwa mwana wa Yozadaki ananyamuka nakayambanso kumanga Nyumba ya Mulungu mu Yerusalemu. Ndipo aneneri a Mulungu anali nawo pamodzi, kuwathandiza.
3 Pa nthawi imeneyo Tatenai, bwanamkubwa wa chigawo cha patsidya pa Yufurate pamodzi ndi Setari-Bozenai ndi anzawo anapita kwa iwo ndi kukawafunsa kuti, “Anakulolani ndani kuti mumangenso Nyumba imeneyi ndi kutsiriza khoma lake?” 4 Anawafunsanso kuti, “Kodi anthu amene akumanga nyumbayi mayina awo ndani?” 5 Koma Mulungu wawo amayangʼanira atsogoleri Ayuda, motero kuti anthu aja anaganiza kuti asawaletse kumanga Nyumbayo mpaka atalembera mfumu Dariyo kalata ndi kulandira yankho lake.
6 Iyi ndi kalata imene Tatenai bwanamkubwa wa dera la patsidya pa Yufurate, ndiponso Setari-Bozenai ndi anzake, akazembe amene anali mʼchigawo cha patsidya pa Yufurate, anatumiza kwa mfumu Dariyo 7 Analemba kalatayo motere:
Kwa mfumu Dariyo:
Mukhale ndi mtendere wonse.
8 Amfumu mudziwe kuti ife tinapita ku dziko la Yuda ku Nyumba ya Mulungu wamkulu. Nyumbayo ikumangidwa ndi miyala ikuluikulu ndipo akuyala matabwa pa makoma. Ntchitoyi ikugwiridwa mwachangu ndipo ikuyenda bwino kwambiri mwautsogoleri wawo.
9 Ndipo tinawafunsa atsogoleriwo kuti, “Anakulolezani kuti mumangenso Nyumbayi ndi kutsiriza makoma ake ndani?” 10 Tinawafunsanso mayina a atsogoleri awo, kuti tikalemba mayina atsogoleriwo tidzakudziwitseni kuti muwadziwe.
11 Yankho limene anatipatsa ndi ili:
“Ife ndife atumiki a Mulungu wa kumwamba ndi wa dziko lapansi, ndipo tikumanganso Nyumba imene mfumu ina yamphamvu ya Israeli inamanga ndi kuyitsiriza zaka zambiri zapitazo. 12 Koma chifukwa chakuti makolo athu anakwiyitsa Mulungu wakumwamba, Iye anawapereka kwa Nebukadinezara Mkalideya, mfumu ya Babuloni, amene anawononga Nyumbayi ndi kutenga anthu onse kupita nawo ku ukapolo ku Babuloni.
13 “Komabe chaka choyamba cha Koresi, mfumu ya ku Babuloni, mfumu Koresiyo anapereka lamulo lakuti Nyumba ya Mulunguyi imangidwenso. 14 Ndipo ziwiya zagolide ndi zasiliva za ku Nyumba ya Mulungu zimene Nebukadinezara anazitenga mʼNyumba ya Mulungu ku Yerusalemu ndi kukaziyika mʼnyumba ya milungu ya ku Babuloni, anakazichotsa ku nyumba ya milungu ya ku Babuloniko ndi kuzipereka kwa Sesibazara, amene mfumu inamusankha kukhala bwanamkubwa. 15 Tsono mfumuyo inamuwuza kuti, ‘Tenga ziwiyazi ukaziyike mʼNyumba ya Mulungu ku Yerusalemu. Ndipo Nyumba ya Mulunguyo ikamangidwenso pa maziko ake akale.’
16 “Choncho Sesibazarayo anabwera ndi kumanga maziko a Nyumba ya Mulunguyo mu Yerusalemu. Kuyambira tsiku limenelo mpaka lero yakhala ikumangidwa ndipo sinathebe.”
17 Nʼchifukwa chake ngati chingakukomereni amfumu, pachitike kafukufuku mʼnyumba yaufumu mosungira chuma ndi mabuku okhudza mbiri ya Babuloni kuti tione ngati mfumu Koresi inalamuladi za kumanganso Nyumba ya Mulungu mu Yerusalemu. Kenaka amfumu mutiwuze zomwe zikukondweretsani kuti mugamule pa nkhani imeneyi.
Yesu Auka kwa Akufa
20 Mmamawa tsiku loyamba la sabata, kukanali kamdimabe, Mariya wa ku Magadala anapita ku manda ndipo anaona kuti mwala unali utachotsedwa pa khomo la manda. 2 Choncho anabwerera akuthamanga kwa Simoni Petro ndi wophunzira winayo, amene Yesu anamukonda, ndipo anati, “Iwo amuchotsa Ambuye mʼmanda, ndipo ife sitikudziwa kumene iwo amuyika Iye!”
3 Choncho Petro ndi wophunzira winayo ananyamuka kupita ku manda. 4 Onse awiri anathamanga pamodzi koma wophunzira winayo anamupitirira Petro, nafika ku manda moyambirira. 5 Ndipo mmene anawerama nasuzumira mʼkati mwa manda anaona nsalu zili potero koma sanalowemo. 6 Kenaka Simoni Petro, amene anali pambuyo pake, anafika ndi kulowa mʼmanda. Iye anaona nsaluzo zili pamenepo, 7 pamodzinso ndi nsalu imene anakulungira nayo mutu wa Yesu. Nsaluyi inali yopindidwa pa yokha yosiyanitsidwa ndi inayo. 8 Pomaliza wophunzira winayo, amene anafika ku manda moyambirira, analowanso mʼkati, iye anaona ndi kukhulupirira. 9 (Iwo sanazindikire kuchokera mʼmalemba kuti Yesu anayanera kuuka kuchokera kwa akufa).
Yesu Aonekera kwa Mariya wa ku Magadala
10 Kenaka ophunzira anabwerera ku nyumba zawo, 11 koma Mariya anayima kunja kwa manda akulira. Pamene akulira, anawerama ndi kusuzumira mʼmanda 12 ndipo anaona angelo awiri atavala zoyera, atakhala pamene panali mtembo wa Yesu, mmodzi kumutu ndi wina kumapazi.
13 Iwo anamufunsa iye kuti, “Amayi, nʼchifukwa chiyani mukulira?”
Iye anati, “Amuchotsa Mbuye wanga, ndipo ine sindikudziwa kumene iwo amuyika.” 14 Atanena izi, iye anatembenuka ndipo anaona Yesu atayima potero koma iye sanazindikire kuti anali Yesu.
15 Iye anati, “Amayi, mukulira chifukwa chiyani? Ndani amene mukumufunafuna?”
Poganiza kuti anali mwini munda, iye anati, “Bwana, ngati inu mwamuchotsa, ndiwuzeni kumene mwamuyika, ndipo ine ndikamutenga.”
16 Yesu anati kwa iye, “Mariya.”
Anatembenukira kwa Iye nafuwula mu Chiaramaiki kuti, “Raboni!” (kutanthauza Mphunzitsi).
17 Yesu anati, “Usandigwire Ine, pakuti sindinapite kwa Atate. Mʼmalo mwake pita kwa abale anga ndikukawawuza kuti, ndikupita kwa Atate ndi kwa Atate anunso, kwa Mulungu wanga ndi Mulungu wanunso.”
18 Mariya wa ku Magadala anapita kwa ophunzira ndi uthenga wakuti, “Ndamuona Ambuye!” Iye anawawuza iwo kuti Yesu ananena zinthu izi kwa iye.
Yesu Aonekera kwa Ophunzira ake Tomasi Palibe
19 Madzulo a tsiku limenelo limene linali loyamba la Sabata ophunzira ake ali pamodzi, atatseka ndi kukhoma zitseko chifukwa choopa Ayuda, Yesu anabwera ndi kuyima pakati pawo nati, “Mtendere ukhale nanu!” 20 Iye atatha kunena izi, anawaonetsa manja ake ndi mʼnthiti mwake. Ophunzira anasangalala kwambiri pamene anaona Ambuye.
21 Yesu anatinso, “Mtendere ukhale nanu! Monga Atate anandituma Ine, Inenso ndikukutumani.” 22 Ndi mawu amenewo Iye anawapumira ndipo anati, “Landirani Mzimu Woyera. 23 Ngati mukhululukira aliyense machimo ake, iwo akhululukidwa; ngati simuwakhululukira, iwo sanakhululukidwe.”
Yesu Aonekera kwa Tomasi
24 Koma Tomasi (otchedwa Didimo), mmodzi wa khumi ndi awiriwo, sanali ndi ophunzira pamene Yesu anabwera. 25 Ophunzira enawo atamuwuza Tomasi kuti iwo anaona Ambuye, iye ananenetsa kuti, “Pokhapokha nditaona zizindikiro za misomali mʼmanja ake ndi kuyikamo chala changa mʼmene munali misomali ndi kukhudza dzanja langa mʼnthiti mwake, ine sindidzakhulupirira.”
26 Patapita sabata, ophunzira ake analinso mʼnyumbamo ndipo Tomasi anali nawo. Ngakhale makomo anali otsekedwa, Yesu anabwera nayima pakati pawo, ndipo anati, “Mtendere ukhale nanu!” 27 Kenaka anati kwa Tomasi, “Ika chala chako apa; ona manja anga. Tambasula dzanja lako ndi kukhudza mʼnthiti mwanga. Leka kukayika, khulupirira.”
28 Tomasi anati kwa Iye, “Ambuye wanga ndi Mulungu wanga!”
29 Kenaka Yesu anamuwuza kuti, “Kodi wakhulupirira chifukwa wandiona Ine? Ndi odala amene amakhulupirira ngakhale asanaone.”
Cholinga cha Uthenga Wabwino wa Yohane
30 Yesu anachita zodabwitsa zambiri pamaso pa ophunzira ake zimene sizinalembedwe mʼbuku lino. 31 Koma izi zalembedwa kuti mukhulupirire kuti Yesu ndi Khristu, Mwana wa Mulungu, ndi kuti mukakhulupirira mukhale nawo moyo mʼdzina lake.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.