Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Old/New Testament

Each day includes a passage from both the Old Testament and New Testament.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
2 Samueli 23-24

Mawu Otsiriza a Davide

23 Nawa mawu otsiriza a Davide:

“Mawu a Davide mwana wa Yese,
    mawu a munthu amene wakwezedwa ndi Wammwambamwamba,
munthu wodzozedwa ndi Mulungu wa Yakobo,
    woyimba nyimbo za Israeli:

“Mzimu wa Yehova unayankhula kudzera mwa ine;
    mawu ake anali pakamwa panga.
Mulungu wa Israeli anayankhula,
    Thanthwe la Israeli linati kwa ine:
‘Pamene munthu alamulira anthu mwachilungamo,
    pamene alamulira moopa Mulungu,
amakhala ngati kuwala kwa mmamawa,
    mmawa wopanda mitambo,
monga kuwala pamene mvula yaleka kugwa
    imene imameretsa udzu mʼnthaka.’

“Kodi banja langa silolungama pamaso pa Mulungu?
    Kodi Iye sanachite pangano losatha ndi ine,
    lokonzedwa ndi lotetezedwa mbali zonse?
Kodi sadzakwaniritsa chipulumutso changa,
    ndi kundipatsa chokhumba changa chilichonse?
Koma anthu oyipa ndiwo ayenera kutayidwa kunja ngati minga,
    imene sitengedwa ndi manja.
Aliyense amene wayikhudza mingayo
    amayidula pogwiritsa ntchito chigwandali kapena ndodo ya mkondo;
    nayitentha pa moto.”

Ankhondo Otchuka a Davide

Nawa mayina a ankhondo amphamvu a Davide:

Yosebu-Basebeti wa ku Takemoni mkulu wa atsogoleri a ankhondo atatu. Iye anapha ndi mkondo ankhondo 800 nthawi imodzi.

Wotsatana naye anali Eliezara mwana wa Dodo Mwahohi. Monga mmodzi mwa ankhondo atatu amphamvu a Davide, iye anali ndi Davide pamene anazunza Afilisti amene anasonkhana ku Pasi-Damimu kuchita nkhondo. Kenaka ankhondo a Israeli anabwerera mʼmbuyo. 10 Koma iye anayima osasuntha ndipo anakantha Afilisti mpaka mkono wake unatopa ndipo unakanirira ku lupanga lake. Yehova anapereka chigonjetso chachikulu pa tsiku limenelo. Asilikali anabwerera kwa Eliezara, kukatenga katundu wa anthu ophedwa.

11 Wotsatana naye anali Sama mwana wa Age Mharari. Pamene Afilisti anasonkhana pamalo pamene panali munda wa mphodza, ankhondo a Israeli anathawa Afilistiwo. 12 Koma Sama anayima pakati pa mundawo. Iye anawuteteza nakantha Afilistiwo ndipo Yehova anawapambanitsa koposa.

13 Pa nthawi yokolola, atatu mwa atsogoleri makumi atatu anabwera kwa Davide ku phanga la Adulamu, pamene gulu la Afilisti linali litamanga misasa mʼchigwa cha Refaimu. 14 Nthawi imeneyo Davide anali mu linga, ndipo boma la Afilisti linali ku Betelehemu. 15 Davide analakalaka madzi ndipo anati, “Haa, pakanapezeka munthu wokanditungira madzi a mʼchitsime chomwe chili pafupi ndi chipata cha ku Betelehemu!” 16 Choncho anthu amphamvu atatuwa anadutsa mizere ya Afilisti, natunga madzi amene anali mʼchitsime chomwe chinali pafupi ndi chipata cha ku Betelehemu nabwera nawo kwa Davide. Koma iye anakana kumwa. Mʼmalo mwake anathira pansi pamaso pa Yehova. 17 Iye anati, “Inu Yehova, musalole kuti ine ndichite chinthu ichi! Kodi awa si magazi a anthu amene anayika miyoyo yawo pachiswe?” Ndipo Davide sanamwe madziwo.

Zimenezi ndi zimene anachita anthu amphamvu atatuwo.

18 Abisai mʼbale wa Yowabu mwana wa Zeruya ndiye anali mtsogoleri wa anthu atatuwa. Iye anapha ndi mkondo ankhondo 300, choncho iyeyo anali wotchuka pakati pa anthu atatu aja. 19 Kodi iyeyo sanali wolemekezeka koposa? Iye anakhala mtsogoleri wawo ngakhale kuti sanali mʼgulu la anthu atatu aja.

20 Benaya mwana wa Yehoyada wa ku Kabizeeli anali munthu wolimba mtima amene anachita zinthu zamphamvu. Iye anakantha ankhondo awiri otchuka a ku Mowabu. Tsiku lina kukuzizira kwambiri, iye analowa mʼdzenje ndi kuphamo mkango. 21 Ndipo iye anakanthanso Mwigupto wamkulu msinkhu. Ngakhale kuti Mwiguptoyo anali ndi mkondo mʼdzanja mwake, Benaya anapita kukamenyana naye ali ndi chibonga chokha mʼmanja. Iye analanda mkondo mʼdzanja la Mwiguptoyo ndi kumupha ndi mkondo wake womwe. 22 Izi ndi zamphamvu zimene Benaya mwana wa Yehoyada anachita. Iyeyo analinso wotchuka ngati anthu atatu amphamvu aja. 23 Iye ankalemekezedwa kuposa wina aliyense mwa anthu makumi atatu aja, koma sanali mʼgulu la anthu atatu aja. Ndipo Davide anamuyika kukhala woyangʼanira asilikali omuteteza.

24 Mʼgulu la anthu makumi atatu aja munalinso awa:

Asaheli mʼbale wa Yowabu,

Elihanani mwana wa Dodo wa ku Betelehemu,

25 Sama Mharodi,

Elika Mherodi,

26 Helezi Mpaliti,

Ira mwana wa Ikesi wa ku Tekowa,

27 Abiezeri wa ku Anatoti,

Sibekai Mhusati,

28 Zalimoni Mwahohi,

Maharai Mnetofa,

29 Heledi mwana wa Baana Mnetofa,

Itai mwana wa Ribai wa ku Gibeya ku Benjamini,

30 Benaya Mpiratoni,

Hidayi wa ku zigwa za Gaasi.

31 Abi-Aliboni Mwaribati,

Azimaveti Mbarihumi,

32 Eliyahiba Msaaliboni,

ana a Yaseni,

Yonatani, 33 mwana wa Sama Mharari,

Ahiamu mwana wa Sarari Mharari,

34 Elifeleti mwana wa Ahasibai Mmaakati,

Eliamu mwana wa Ahitofele Mgiloni,

35 Heziro wa ku Karimeli,

Paarai Mwaribi,

36 Igala mwana wa Natani wa ku Zoba,

mwana wa Hagiri,

37 Zeleki Mwamoni,

Naharai wa ku Beeroti, mnyamata wonyamula zida za Yowabu mwana wa Zeruya,

38 Ira Mwitiri,

Garebu Mwitiri,

39 ndi Uriya Mhiti.

Onse pamodzi analipo 37.

Davide Awerenga Ankhondo

24 Nthawi inanso Yehova anawakwiyira Aisraeli ndipo anawutsa mtima wa Davide kuti awavutitse ndipo anati, “Pita kawerenge Aisraeli ndi Ayuda.”

Choncho mfumu inati kwa Yowabu pamodzi ndi atsogoleri a ankhondo amene anali nawo. “Pitani pakati pa mafuko onse a Israeli kuyambira ku Dani mpaka ku Beeriseba kuti mukawerenge anthu omenya nkhondo ndi cholinga choti ndidziwe chiwerengero chawo.”

Koma Yowabu anayankha mfumu kuti, “Yehova Mulungu wanu achulukitse ankhondo anu kukhala miyandamiyanda, ndipo alole inu mbuye wanga mfumu mudzazione zimenezi. Koma nʼchifukwa chiyani inu mbuye wanga mfumu mukufuna kuchita zimenezi?”

Komabe mawu a mfumu anapambana mawu a Yowabu ndi atsogoleri a ankhondo. Choncho anachoka pamaso pa mfumu kupita kukawerenga anthu omenya nkhondo mu Israeli.

Atawoloka Yorodani, iwo anamanga misasa yawo pafupi ndi Aroeri kummwera kwa mzinda wa ku chigwa ndipo kenaka iwo anapita ku dziko la Gadi mpaka ku Yazeri. Iwo anapita ku Giliyadi ndi ku chigwa cha Tahitimu Hodisi ndipo anapitirira mpaka ku Dani Yaani ndi madera ozungulira Sidoni. Kenaka iwo anapita molunjika linga la ku Turo ndi ku mizinda yonse ya Ahivi ndi Akanaani. Pomaliza anapita ku Beeriseba ku Negevi wa ku Yuda.

Atayendayenda mʼdziko lonse anabwerera ku Yerusalemu patapita miyezi isanu ndi inayi ndi masiku makumi awiri.

Yowabu anapereka chiwerengero cha anthu ankhondo kwa mfumu: Mu Israeli munali anthu 800,000 amphamvu amene amadziwa kugwiritsa ntchito lupanga ndipo mu Yuda munali anthu 500,000.

10 Davide anatsutsika mu mtima mwake atatha kuwerenga anthuwo ndipo anapemphera kwa Yehova kuti, “Ine ndachimwa kwambiri pa zimene ndachita. Tsono Yehova, ndikupempha kuti mukhululuke kulakwa kwa mtumiki wanu. Ine ndachita zopusa kwambiri.”

11 Davide asanadzuke mmawa mwake mawu a Yehova anafika kwa mneneri Gadi, mlosi wa Davide kuti, 12 “Pita ukamuwuze Davide kuti, ‘Yehova akuti, Ine ndikukupatsa zinthu zitatu izi. Usankhepo chimodzi pa zimenezi choti ndikuchitire.’ ”

13 Choncho Gadi anapita kwa Davide ndipo anati kwa iye, “Kodi mungakonde kuti mʼdziko mwanu mukhale njala kwa zaka zitatu? Kapena kuti mukhale mukuthawa adani anu kwa miyezi itatu? Kapena kuti mʼdziko muno mukhale mliri kwa masiku atatu? Tsopano, ganizirani bwino ndipo musankhe chomwe mudzamuyankhe amene wandituma.”

14 Davide anati kwa Gadi, “Ine ndavutika kwambiri mu mtima mwanga. Ife atilange ndi Yehova pakuti chifundo chake ndi chachikulu, koma ndisalangidwe ndi anthu.”

15 Choncho Yehova anabweretsa mliri pa Aisraeli, kuyambira mmawa mpaka pa nthawi imene anafuna mwini wake, ndipo unapha anthu 70,000 kuyambira ku Dani mpaka ku Beeriseba. 16 Pamene mngelo anatambasula dzanja lake kuti awononge Yerusalemu, Yehova anamva chisoni chifukwa cha zowawazo ndipo anati kwa mngelo amene ankawononga anthu uja, “Basi kwakwanira! Leka kuwononga.” Nthawi imeneyo mngelo wa Yehova anali atayima pamalo opunthira tirigu a Arauna Myebusi.

17 Davide ataona mngelo amene ankakantha anthu uja, anati kwa Yehova, “Ine ndi amene ndachimwa. Ine mʼbusa ndiye ndachita zoyipa. Anthuwa ali ngati nkhosa zosalakwa. Kodi iwowa achita chiyani? Langani ineyo pamodzi ndi banja langa.”

Davide Amanga Guwa la Nsembe

18 Tsiku limenelo Gadi anapita kwa Davide ndi kukanena kuti, “Pitani kamangeni guwa lansembe la Yehova pamalo opunthira tirigu a Arauna Myebusi.” 19 Ndipo Davide anapita monga momwe Yehova anamulamulira kudzera mwa Gadi. 20 Arauna atayangʼana ndi kuona mfumu ndi anthu ake akubwera kumene kunali iye, iyeyo anatuluka ndi kuwerama pamaso pa mfumu mpaka nkhope yake kugunda pansi.

21 Arauna anati, “Nʼchifukwa chiyani mbuye wanga mfumu mwabwera kwa mtumiki wanu?”

Davide anayankha kuti, “Kudzagula malo ako opunthira tirigu kuti ndimangire Yehova guwa lansembe kuti mliri uli pa anthuwa usiye.”

22 Arauna anati kwa Davide, “Mbuye wanga mfumu mutenge chilichonse chimene chikukondweretseni ndi kuchipereka nsembe. Nazi ngʼombe zazimuna za nsembe yopsereza, nazi zopunthira tirigu ndi magoli angʼombe kuti zikhale nkhuni. 23 Inu mfumu, Arauna akupereka zonsezi kwa inu mfumu.” Arauna anatinso kwa iye, “Yehova Mulungu wanu akuvomerezeni.”

24 Koma mfumu inayankha Arauna kuti, “Ayi, Ine ndikunenetsa kuti ndikulipira. Sindidzapereka kwa Yehova Mulungu wanga nsembe yopsereza imene sindinavutikire.”

Kotero Davide anagula malo wopunthira tiriguwo ndi ngʼombe ndipo anapereka kwa Araunayo masekeli asiliva makumi asanu. 25 Davide anamanga guwa lansembe la Yehova pamenepo ndipo anaperekapo nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano. Ndipo Yehova anayankha pempherolo mʼmalo mwa dziko lonse, ndipo mliri unatha pa Aisraeli.

Luka 19:1-27

Zakeyu Apulumutsidwa

19 Yesu analowa mu Yeriko napitirira. Kunali munthu kumeneko dzina lake Zakeyu; iye anali mkulu wa wolandira msonkho ndipo anali wolemera. Iye ankafuna kuona Yesu kuti ndani, koma pokhala wamfupi sanathe chifukwa cha gulu la anthu. Choncho iye anathamangira patsogolo ndipo anakwera mu mtengo wamkuyu kuti amuone Iye, pakuti Yesu ankadutsa njira imeneyo.

Yesu atafika pa malopo, anayangʼana mmwamba ndipo anati kwa iye, “Zakeyu, tsika msangamsanga. Ine ndiyenera kukhala mʼnyumba mwako lero.” Ndipo nthawi yomweyo anatsika ndipo anamulandira mosangalala.

Anthu onse ataona zimenezi anayamba kungʼungʼudza, nati, “Iye akupita kuti akakhale mlendo wa wochimwa.”

Koma Zakeyu anayimirira ndipo anati kwa Ambuye, “Taonani Ambuye! Theka la chuma changa ndipereka kwa osauka ndipo ngati ndinamubera wina aliyense pa chilichonse, ndidzamubwezera mochulukitsa kanayi.”

Yesu anati kwa iye, “Lero chipulumutso chafika mʼnyumba ino, chifukwa munthu uyu nayenso ndi mwana wa Abrahamu. 10 Pajatu Mwana wa Munthu anabwera kudzafunafuna ndi kupulumutsa chotayikacho.”

Antchito Opindula Mosiyana

11 Pamene iwo ankamvera izi, Iye anapitiriza kuwawuza fanizo, chifukwa Iye anali kufupi ndi Yerusalemu ndipo anthu ankaganiza kuti ufumu wa Mulungu ukanaoneka nthawi yomweyo. 12 Iye anati, “Munthu wa banja laufumu anapita ku dziko lakutali kukadzozedwa ufumu ndipo kenaka abwerenso kwawo. 13 Tsono iye anayitana antchito ake khumi ndi kuwapatsa ndalama khumi. Iye anati, ‘Gwiritsani ntchito ndalama izi mpaka nditabwerera.’

14 “Koma anthu ake anamuda ndipo anatuma nthumwi pambuyo pake kukanena kuti, ‘Sitikufuna munthuyu kuti akhale mfumu yathu.’

15 “Iye analandira ufumuwo ngakhale zinali zotero, ndipo anabwerera kwawo. Kenaka iye anatumiza uthenga kwa antchito ake amene anawapatsa ndalama aja, ndi cholinga chakuti adziwe chimene anapindula nazo.

16 “Woyamba anabwera ndipo anati, ‘Bwana ndalama zanu zapindula khumi zina.’

17 “Bwana wakeyo anayankha kuti, Wachita bwino wantchito wabwino. ‘Chifukwa wakhulupirika pa zinthu zazingʼono, lamulira mizinda khumi.’

18 “Wachiwiri anabwera ndipo anati, ‘Bwana, ndalama zanu zapindula zisanu zina.’

19 “Bwana anayankha kuti, ‘Iwe lamulira mizinda isanu.’

20 “Kenaka wantchito wina anabwera ndipo anati, ‘Bwana, ndalama yanu nayi; ine ndinayibisa ndi kuyisunga mʼkansalu. 21 Ine ndimakuopani, chifukwa ndinu munthu wowuma mtima. Inu mumatenga chimene simunachiyike ndi kukolola chimene simunadzale.’

22 “Bwana wake anayankha kuti, ‘Ine ndikukuweruza iwe ndi mawu ako omwewo. Ndiwe wantchito woyipa. Kani umadziwa kuti ndine munthu wowuma mtima ndi wotenga chimene sindinasungitse, ndi kukolola chimene sindinadzale? 23 Nanga nʼchifukwa chiyani sunasungitse ndalama yanga, kuti ine pobwera, ndidzayitenge ndi chiwongoladzanja?’

24 “Ndipo iye anawuza amene anayimirira pafupi kuti, ‘Tengani ndalama yake ndi kumupatsa amene ali ndi ndalama khumiyo!’ ”

25 Iwo anati, “Bwana iyeyu ali nazo kale khumi!”

26 Iye anayankha kuti, “Ndikukuwuzani kuti, aliyense amene ali nazo, adzapatsidwa zambiri, koma amene alibe, adzalandidwa ngakhale chimene ali nacho. 27 Tsono adani anga aja amene sankafuna kuti ndikhale mfumu yawo, abweretseni pano ndi kuwapha ine ndikuona.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.