Old/New Testament
Davide, Nabala ndi Abigayeli
25 Samueli anamwalira, ndipo Aisraeli onse anasonkhana kudzalira maliro ake ndipo anamuyika mʼmanda ku mudzi kwawo ku Rama.
Ndipo Davide anapita ku chipululu cha Parani. 2 Kunali munthu wina wolemera kwambiri ku Maoni amene malo ake a ntchito anali ku Karimeli. Iyeyu anali ndi mbuzi 1,000 ndi nkhosa 3,000. 3 Dzina lake linali Nabala ndipo anali wa fuko la Kalebe. Dzina la mkazi wake linali Abigayeli. Anali mkazi wanzeru ndi wokongola, koma mwamuna wake, wa banja la Kalebe, anali wowuma mtima ndi wamwano pa zochita zake.
4 Davide anamva akanali ku chipululu kuti Nabala akumeta nkhosa. 5 Choncho anatuma anyamata khumi nawawuza kuti, “Pitani kwa Nabala ku Karimeli ndipo mukamulonjere mʼdzina langa. 6 Mukamuwuze kuti, ‘Mtendere ukhale ndi inu, banja lanu pamodzi ndi zonse zimene muli nazo.
7 “ ‘Tsono ndamva kuti muli ndi anthu ometa nkhosa. Pamene abusa anu anali nafe kuno, sitinawachite china chilichonse choyipa, ndipo sanasowe kanthu pa nthawi yonse imene anali ku Karimeli. 8 Muwafunse antchito anu ndipo akuwuzani. Kotero akomereni mtima anyamata anga, pakuti tabwera pa nthawi yachikondwerero. Chonde apatseniko antchito anuwo ndi mwana wanu Davide chilichonse chimene mungakhale nacho.’ ”
9 Anyamata a Davide aja atafika, anamuwuza Nabala zonse zimene Davide anayankhula. Ndipo anadikira yankho.
10 Nabala anayankha anyamata a Davide kuti, “Kodi Davide ndi ndani? Mwana wa Yese ndi ndani? Masiku ano pali antchito ambiri amene akuthawa kwa mabwana awo. 11 Nditengerenji buledi, madzi ndi nyama zimene ndaphera anthu anga ometa nkhosa ndi kuzipereka kwa anthu amene sindikudziwa kumene achokera?”
12 Choncho anyamata a Davide aja anatembenuka nabwerera. Atafika anafotokozera Davide mawu onse a Nabala. 13 Davide anawuza anthu ake kuti, “Aliyense amangirire lupanga lake!” Choncho aliyense anamangirira lupanga lake. Davidenso anamangirira lupanga lake. Anthu pafupifupi 400 ndiwo anapita ndi Davide, pamene anthu 200 anatsala ndi katundu.
14 Tsono mmodzi mwa antchito anawuza Abigayeli mkazi wa Nabala kuti, “Davide anatumiza amithenga kuchokera ku chipululu kudzalonjera mbuye wathu, koma iye anawalalatira. 15 Komatu anthuwa anatichitira zabwino kwambiri. Sanatizunze, ndipo nthawi yonse imene tinali nawo ku busa sitinasowe kanthu. 16 Ankatitchinjiriza ngati mpanda usiku ndi usana nthawi yonse tinkaweta nkhosa. 17 Tsono onani chimene mungachite, chifukwa zimenezi zingadzetse tsoka pa mbuye wathu pamodzi ndi nyumba yake. Paja mbuye athu aja ndi munthu wa khalidwe loyipa moti palibe amene angathe kuyankhula naye.”
18 Ndipo Abigayeli sanataye nthawi. Iye anatenga malofu a buledi 200, matumba a chikopa awiri a vinyo, nkhosa zisanu zowotcheratu, makilogalamu 17 a tirigu wokazinga, makeke a mphesa zowuma 100, ndiponso makeke a nkhuyu 200, ndipo anazisenzetsa abulu. 19 Kenaka anawuza antchito ake kuti, “Tsogolani, ine ndikutsatirani.” Koma sanawuze mwamuna wake Nabala.
20 Mayi uja atakwera pa bulu wake ndi kufika pa tsinde la phiri, anangoona Davide ndi ankhondo ake akubwera kunali iye. Choncho anakumana nawo. 21 Nthawiyi nʼkuti Davide atanena kuti, “Kani ndinalondera pachabe katundu wa munthu uyu mʼchipululu muja! Ndipotu palibe kanthu nʼkamodzi komwe kake kamene kanasowa. Tsono wandibwezera zoyipa mʼmalo mwa zabwino. 22 Mulungu andilange kwambiri ngati pofika mmawa nditakhale nditasiyako ngakhale munthu mmodzi mwa onse amene ali nawo.”
23 Abigayeli ataona Davide, anatsika pa bulu wake mofulumira ndipo anadzigwetsa pansi pamaso pa Davide. 24 Ali chigonere choncho pa mapazi a Davide anati, “Mbuye wanga, kulakwa kukhale pa ine ndekha. Chonde lolani kuti mdzakazi wanune ndiyankhule nanu, ndipo mumve mawu a ine mdzakazi wanu. 25 Mbuye wanga musasamale za mwamuna wanga Nabala, munthu wa khalidwe loyipa. Iyeyu ali monga dzina lake liliri. Monga dzina lake litanthauza kuti chitsiru, ndiye kuti zake zonse ndi zauchitsiru basi. Koma ine mdzakazi wanu, sindinawaone anthu amene mbuye wanga munawatuma. 26 Tsono mbuye wanga muli apa, ndikulumbira pali Yehova wamoyo amene wakuletsani kuti musakhetse magazi a munthu ndi kulipsira nokha, kuti adani anu amene afuna kukuchitani zoyipa adzakhale ngati Nabala. 27 Choncho, nazi mphatso zimene mdzakazi wanu ndabwera nazo kwa mbuye wanga kuti zipatsidwe kwa anyamata amene muli nawo. 28 Chonde khululukani zolakwa za ine mdzakazi wanu. Ndithu Yehova adzakhazikitsa banja la mbuye wanga mu ufumu, popeza mukumenya nkhondo ya Yehova. Choncho choyipa sichidzapezeka mwa inu masiku onse a moyo wanu. 29 Ngati munthu wina akuwukirani ndi kukulondani, Yehova Mulungu wanu adzateteza moyo wa mbuye wanga monga mmene munthu asungira chuma mʼphukusi, koma moyo wa adani anu adzawutaya kutali monga momwe munthu amaponyera mwala ndi legeni. 30 Yehova adzakuchitirani mbuye wanga zabwino zonse zimene anakulonjezani. Adzakuyikani kukhala wolamulira Aisraeli. 31 Zikadzatero, inu mbuye wanga simudzakhala ndi chikumbumtima choti munakhetsa magazi kapena kulipsira popanda chifukwa. Koma Yehova akadzakuchitirani zabwino zonsezi musadzandiyiwale ine mdzakazi wanu.”
32 Tsono Davide anawuza Abigayeli kuti, “Alemekezeke Yehova Mulungu wa Israeli, amene wakutuma iwe lero kuti ukumane nane. 33 Yehova akudalitseni chifukwa cha nzeru zanu pondiletsa lero kuti ndisakhetse magazi ndi kubwezera adani anga ndi manja anga. 34 Kunena zoona, pali Yehova Wamoyo, Mulungu wa Israeli, amene wandiletsa kuti ndisakupwetekeni, mukanapanda kubwera msanga kudzakumana nane, palibe munthu aliyense wamwamuna wa Nabala akanasiyidwa wamoyo pakucha mmawa.”
35 Ndipo Davide analandira kwa mayiyo zimene anamutengera ndipo anati, “Pitani kwanu mu mtendere. Ine ndamva mawu anu ndipo ndavomera zimene mwapempha.”
36 Abigayeli atabwerera kwa Nabala anamupeza ali mʼnyumba akuchita mphwando ngati la mfumu. Iye anali atakondwa kwambiri popeza anali ataledzera kwambiri. Choncho mkazi wakeyo sanamuwuze kalikonse mpaka mmawa kutacha. 37 Tsono mmawa, mowa utamuchoka Nabala, mkazi wake anamuwuza zonse. Pomwepo mtima wake unaleka kugunda ndipo unawuma gwaa ngati mwala. 38 Patapita masiku khumi, Yehova anakantha Nabala ndipo anafa.
39 Pamene Davide anamva kuti Nabala wamwalira, iye anati, “Alemekezeke Yehova, walipsira Nabala chipongwe chimene anandichita ndipo anandiletsa ine mtumiki wake kuti ndisachite choyipa. Yehova wabwezera pamutu pa Nabala choyipa chimene iye anachita.”
Kenaka Davide anatumiza mawu kwa Abigayeli, kumupempha kuti akhale mkazi wake. 40 Anyamata a Davide atafika ku Karimeli anawuza Abigayeli kuti, “Davide watituma kwa iwe kuti tikutenge ukhale mkazi wake.”
41 Abigayeli anagwada nagunditsa nkhope yake pansi ndipo anati, “Ine mdzakazi wa mbuye wanga ndakonzeka kutumikira ngakhale kusambitsa mapazi a anyamata ake.” 42 Motero Abigayeli ananyamuka mofulumira nakwera bulu wake. Tsono iye pamodzi ndi anamwali ake asanu amene ankamutumikira, anatsagana ndi amithenga a Davide aja ndipo anakakhala mkazi wake wa Davide. 43 Davide nʼkuti atakwatiranso Ahinoamu wa ku Yezireeli ndipo onse awiri anali akazi ake. 44 Koma Sauli anali atakwatitsa Mikala, mkazi wa Davide kwa Paliti mwana wa Laisi wa ku Galimu.
Davide Apewa Kupha Sauli Kachiwiri
26 Anthu a ku Zifi anapita kwa Sauli ku Gibeya nati, “Davide akubisala ku phiri la Hakila, limene limayangʼanana ndi Yesimoni.”
2 Choncho Sauli ananyamuka pamodzi ndi ankhondo ake 3,000 napita ku chipululu cha Zifi kukafunafuna Davide ku chipululuko. 3 Sauli anamanga msasa wake mʼmbali mwa njira yopita ku phiri la Hakila moyangʼanana ndi Yesimoni. Koma Davide anali mʼchipululumo. Davide ataona kuti Sauli amamulondola mpaka kumeneko, 4 iye anatumiza anthu okazonda ndipo anapeza kuti Sauli wafikadi ndithu.
5 Tsono Davide ananyamuka napita kumalo kumene Sauli anamanga misasa. Iye anaona pamene Sauli ndi Abineri mwana wa Neri mkulu wa ankhondo anagona. Sauli anagona mʼkati mwa tenti ndipo asilikali anagona momuzungulira.
6 Ndipo Davide anafunsa Ahimeleki Mhiti ndi Abisai mwana wa Zeruya, mʼbale wa Yowabu kuti, “Ndani adzapita nane ku msasa kwa Sauli?”
Abisai anayankha kuti, “Ine ndidzapita nanu.”
7 Choncho Davide ndi Abisai anapita ku misasa ya ankhondowo usiku. Atafika anangopeza Sauli ali gone mu msasa wake mkondo wake atawuzika pansi pafupi ndi mutu wake, Abineri ndi ankhondo onse anali atagona momuzungulira.
8 Abisai anawuza Davide kuti, “Lero Mulungu wapereka mdani wanu mʼmanja mwanu. Tsopano ndiloleni ndimukhomere pansi ndi mkondo wangawu kamodzinʼkamodzi. Sindimulasa kawiri.”
9 Koma Davide anamuyankha Abisai kuti, “Usamuphe! Ndani adzapha wodzozedwa wa Yehova ndi kupezeka wosalakwa? 10 Davide anati, Pali Yehova wamoyo, Yehova mwini ndiye adzamukanthe, mwina tsiku lake lomwalira lidzafika, kapena adzapita ku nkhondo nakaphedwa komweko. 11 Koma Yehova andiletse kuti ndisapweteke wodzozedwa wa Yehova. Tsopano tingotenga mkondo umene uli ku mutu kwakewo ndi botolo la madzilo ndipo tizipita.”
12 Motero Davide anatenga mkondo ndi botolo lamadzi zimene zinali ku mutu kwa Sauli ndipo anachoka. Palibe amene anaona zimenezi kapena kudziwa, ndipo palibenso amene anadzuka. Onse anali mʼtulo, chifukwa Yehova anawagonetsa tulo tofa nato.
13 Pambuyo pake Davide anadutsa nakakwerera mbali ina ya phiri, ndi kuyimirira pamwamba pa phiri patali. Pakati pawo panali mpata waukulu. 14 Davide anayitana gulu lankhondo ndi Abineri mwana wa Neri nawafunsa kuti, “Kodi sundiyankha ine Abineri?”
Abineri anayankha kuti, “Ndiwe yani amene ukuyitana mfumu?”
15 Davide anamufunsa Abineri kuti, “Kodi sindiwe mwamuna? Ndipo wofanana nawe ndani mu Israeli? Nʼchifukwa chiyani sunateteze mbuye wako mfumu? Munthu wina anabwera kumeneko. 16 Chimene wachita iwe si chabwino. Pali Yehova wamoyo iwe ndi asilikali ako muyenera kufa chifukwa simunateteze mbuye wanu, wodzozedwa wa Yehova. Tayangʼanayangʼana. Uli kuti mkondo wa mfumu ndi botolo lamadzi zimene zinali kumutu kwa mfumu?”
17 Sauli anazindikira mawu a Davide ndipo anafunsa kuti, “Kodi amenewa ndi mawu ako Davide mwana wanga?”
Davide anayankha, “Inde ndi anga, mbuye wanga mfumu. 18 Nʼchifukwa chiyani mbuye wanga mukundilonda ine mtumiki wanu? Kodi ine ndachita chiyani ndipo ndapezeka ndi cholakwa chotani? 19 Tsopano mbuye wanga mfumu tamverani mawu a mtumiki wanu. Ngati ndi Yehova wautsa mtima wanu kuti mundiwukire, ndiye alandire chipepeso. Koma ngati ndi anthu amene achita zimene, ndiye Yehova awatemberere popeza andipirikitsa lero kundichotsa mʼdziko la Yehova, namati, ‘Pita kapembedze milungu ina.’ 20 Tsopano musalole kuti magazi anga akhetsedwe kutali ndi Yehova pakuti mfumu ya Israeli yatuluka kudzafunafuna ine nsabwe, monga mmene munthu asakira nkhwali ku mapiri.”
21 Ndipo Sauli anati, “Ine ndachimwa. Bwerera mwana wanga Davide. Sindidzakuchitanso choyipa popeza lero wauwona moyo wanga ngati wamtengowapatali. Taona, ndachita zauchitsiru ndipo ndachimwa kwambiri.”
22 Davide anayankha kuti, “Nawu mkondo wanu, mfumu. Tumani mmodzi wa anyamata anu abwere adzatenge. 23 Yehova amadalitsa munthu aliyense wolungama ndi wokhulupirika. Yehova anakuperekani lero mʼmanja mwanga, koma ine sindinakhudze wodzozedwa wa Yehova. 24 Monga momwe ine lero ndachitira kuwuyesa moyo wanu ngati wamtengowapatali, momwemonso Yehova awuyese moyo wanga wamtengowapatali ndipo andipulumutse mʼmavuto anga onse.”
25 Ndipo Sauli anawuza Davide kuti, “Yehova akudalitse iwe Davide mwana wanga. Udzachita zinthu zazikulu ndipo udzapambana.”
Choncho Davide anayenda njira yake ndipo Sauli anabwerera kwawo.
Chuma cha Kumwamba
32 “Musachite mantha, inu kagulu kankhosa, pakuti zinakondweretsa Atate anu kuti akupatseni ufumu. 33 Gulitsani zonse zimene muli nazo, ndipo ndalama zake mupereke kwa osauka. Dzipezereni zikwama zandalama zimene sizidzatha, ndi kudzikundikira chuma chomwe sichidzatha kumwamba, kumene mbala sizingafikeko, ndipo dzimbiri silingawononge. 34 Popeza kumene kuli chuma chanu, mtima wanunso udzakhala komweko.”
Kukhala a Atcheru
35 “Khalani okonzekeratu ndipo nyale zanu ziziyaka, 36 ngati anthu oyembekezera kubwera kwa mbuye wawo kuchokera kuphwando la ukwati, kuti pamene afika ndi kugogoda akhoza nthawi yomweyo kumutsekulira chitseko. 37 Zidzakhala bwino kwa antchitowo amene mbuye wawo pobwera adzawapeze akudikira. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti adzakonzekera kuwatumikira, adzakhala nawo pa tebulo ndipo adzabwera ndi kuwatumikira. 38 Zidzakhala bwino kwa antchitowo amene mbuye wawo adzawapeze ali okonzeka, ngakhale iye atabwera pa ora lachiwiri kapena lachitatu usiku. 39 Koma zindikirani izi: Ngati mwini nyumba akanadziwa ora limene mbala ibwera, sakanalola kuti nyumba yake ithyoledwe. 40 Inunso muyenera kukhala okonzeka, chifukwa Mwana wa Munthu adzabwera pa ora limene simukumuyembekezera Iye.”
Wantchito Wokhulupirika ndi Wosakhulupirika
41 Petro anafunsa kuti, “Kodi mukunena fanizoli kwa ife, kapena kwa aliyense?”
42 Ambuye anayankha kuti, “Kodi tsono woyangʼanira wokhulupirika ndi wanzeru ndani? Kodi ndi amene mbuye wake wamuyika kukhala oyangʼanira antchito ake kuti aziwapatsa ndalama yachakudya pa nthawi yake yoyenera? 43 Zidzamukhalira bwino wantchito amene mbuye wake adzamupeza akuchita zimene pamene iye abwera. 44 Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti adzamuyika kukhala woyangʼanira katundu wake yense. 45 Koma tiyerekeze kuti wantchitoyo aziganiza mu mtima mwake kuti, ‘Bwana wanga akuchedwa kwambiri kubwera,’ ndipo kenaka ndi kuyamba kumenya antchito aamuna ndi aakazi ndi kudya, kumwa ndi kuledzera. 46 Mbuye wake adzabwera tsiku limene iye sakumuyembekezera ndi ora limene iye sakudziwa. Iye adzamulanga ndi kumusiya kumalo kumene kuli osakhulupirira.
47 “Wantchito amene amadziwa chifuniro cha mbuye wake koma wosakonzeka kapena wosachita chimene mbuye wake akufuna adzakwapulidwa zikwapu zambiri. 48 Koma wantchito amene sadziwa koma nʼkuchita zinthu zoyenera chilango, adzakwapulidwa zikwapu zochepa. Aliyense amene anapatsidwa zambiri, adzayenera kubwezanso zambiri; ndipo amene anamusungitsa zambiri, adzamulamula kuti abweze zambirinso.”
Za Kugawikana
49 “Ine ndabwera kudzayatsa moto pa dziko lapansi, ndipo ndikanakonda ukanayaka kale. 50 Koma Ine ndiyenera kubatizidwa, ndipo ndikusautsika mu mtima mpaka utachitika! 51 Kodi mukuganiza kuti Ine ndinabwera kudzabweretsa mtendere pa dziko lapansi? Ayi, Ine ndikukuwuzani kuti, ndinabweretsa kugawikana. 52 Kuyambira tsopano mpaka mʼtsogolo mʼbanja limodzi mudzakhala anthu asanu ndipo adzawukirana wina ndi mnzake, atatu kuwukira awiri, ndipo awiri kuwukira atatu. 53 Anthu adzawukirana. Abambo kudzawukira mwana wawo wamwamuna, mwana wawoyo adzawukira abambo ake. Amayi adzawukira mwana wawo wamkazi, mwana wawoyo adzawukira amayi ake. Amayi adzawukira mpongozi wawo wamkazi, mpongoziyo adzawukira amayiwo.”
Kumasulira Nthawi
54 Iye anati kwa gulu la anthu, “Pamene mukuona mtambo ukukwera kummawa, nthawi yomweyo inu mumati, ‘kugwa mvula,’ ndipo imagwadi. 55 Ndipo pamene mphepo yakummwera ikuwomba, inu mumati ‘kutentha’ ndipo kumaterodi. 56 Achiphamaso inu! Inu mumadziwa kutanthauzira maonekedwe a dziko lapansi ndi thambo. Zikutheka bwanji kuti simukudziwa kumasulira kwa nthawi ino?
57 “Bwanji simukuzindikira nokha zoyenera kuchita? 58 Pamene mukupita kwa woweruza ndi amene munalakwirana naye, yesetsani kwambiri kuti muyanjane naye mʼnjiramo, chifukwa mukapanda kutero akhoza kukutengerani ku bwalo la milandu ndipo woweruzayo adzakuperekani kwa woyangʼanira ndende, ndipo woyangʼanira ndendeyo adzakuponyani mʼndende. 59 Ine ndikuwuzani kuti, simudzatulukamo mpaka mutalipira ndalama zonse.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.