Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

New Testament in a Year

Read the New Testament from start to finish, from Matthew to Revelation.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Machitidwe a Atumwi 8:1-25

Ndipo Saulo anavomerezana nawo pa imfa ya Stefano.

Kuzunzika kwa Mpingo

Tsiku lomwelo, mpingo wa mu Yerusalemu unayamba kuzunzidwa, ndipo onse, kupatulapo atumwi, anabalalikira ku madera onse a Yudeya ndi Samariya. Anthu okonda Mulungu anayika maliro a Stefano ndipo anamulira kwambiri. Koma Saulo anayamba kuwononga mpingo. Amapita nyumba ndi nyumba, ndipo amagwira amuna ndi amayi ndi kukawatsekera ku ndende.

Filipo ku Samariya

Okhulupirira amene anabalalika amalalikira konse kumene amapita. Filipo anapita ku mzinda wa ku Samariya ndipo analalikira za Khristu kumeneko. Gulu la anthu litamva Filipo akulalikira komanso kuona zizindikiro zozizwitsa zimene ankazichita, onse anamvetsetsa zimene iye amanena. Mizimu yoyipa inatuluka mwa anthu ambiri ikufuwula kwambiri ndipo ambiri amene anali akufa ziwalo ndi olumala anachiritsidwa. Kotero munali chimwemwe chachikulu mu mzindawo.

Simoni Wamatsenga

Koma mu mzindawo munali munthu dzina lake Simoni, amene amachita za matsenga ndi kudabwitsa anthu a mu Samariya. Iye amadzitamandira kuti ndi wopambana, 10 ndipo anthu onse, aakulu ndi aangʼono anamumvera ndi kunena kuti, “Munthu uyu ndi mphamvu ya Mulungu yotchedwa Mphamvu yayikulu.” 11 Anthu amamutsata chifukwa kwa nthawi yayitali amawadabwitsa ndi matsenga akewo. 12 Koma atakhulupirira Filipo akulalikira Uthenga Wabwino wa ufumu wa Mulungu ndiponso dzina la Yesu Khristu, anthuwo anabatizidwa amuna ndi amayi. 13 Nayenso Simoni anakhulupirira ndipo anabatizidwa, natsatira Filipo kulikonse, ndipo anadabwa kwambiri pamene anaona zizindikiro zazikulu ndi zozizwitsa.

14 Atumwi a ku Yerusalemu atamva kuti anthu a ku Samariya analandira Mawu a Mulungu, anatumiza Petro ndi Yohane. 15 Atafika anawapempherera kuti alandire Mzimu Woyera, 16 chifukwa Mzimu Woyera anali asanafike pa wina aliyense wa iwo; anali atangobatizidwa mʼdzina la Ambuye Yesu. 17 Ndipo Petro ndi Yohane anasanjika manja awo pa iwo, ndipo analandira Mzimu Woyera.

18 Simoni ataona kuti Mzimu anaperekedwa kwa iwo atumwi atawasanjika manja, iye anafuna kuwapatsa ndalama ndipo anati, 19 “Inenso ndipatseni mphamvu imeneyi kuti aliyense amene ndimusanjika manja anga azilandira Mzimu Woyera.”

20 Petro anayankha kuti, “Ndalama zako utayike nazo pamodzi, chifukwa unaganiza kuti ungathe kugula mphatso ya Mulungu ndi ndalama! 21 Ulibe gawo kapena mbali pa utumikiwu, chifukwa mtima wako suli wolungama pamaso pa Mulungu. 22 Lapa zoyipa zakozi ndipo upemphere kwa Ambuye. Mwina adzakukhululukira maganizo a mu mtima mwako. 23 Pakuti ine ndikuona kuti ndiwe wowawidwa mtima ndiponso kapolo wa tchimo.”

24 Ndipo Simoni anayankha, “Mundipempherere kwa Ambuye kuti zisandigwere izi mwanenazi.”

25 Atatha kuchitira umboni ndi kulalikira mawu a Ambuye, Petro ndi Yohane anabwerera ku Yerusalemu, atalalikira Uthenga Wabwino mʼmidzi yambiri ya Asamariya.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.