New Testament in a Year
22 Koma alonda aja atafika kundende, sanawapezemo. Iwo anabwerera nakawafotokozera 23 kuti, “Tinakapeza ndende ili chitsekere ndithu, ndi alonda atayimirira pa khomo, koma pamene tinatsekula zitseko, sitinapezemo munthu aliyense mʼkatimo.” 24 Mkulu wa alonda a Nyumba ya Mulungu ndi akulu a ansembe atamva zimenezi anathedwa nzeru, osadziwa kuti zimenezi zidzatha bwanji.
25 Ndipo wina anabwera ndi kuti, “Taonani! Anthu aja amene munawatsekera mʼndende ali ku Nyumba ya Mulungu ndipo akuphunzitsa anthu.” 26 Pamenepo mkulu wa alonda pamodzi ndi alonda anakawatenga atumwi. Sanakawatenge mwaukali, chifukwa amaopa kuti anthu angawaponye miyala.
27 Atafika nawo atumwi aja, anawayimika pamaso pa Bwalo Lalikulu kuti afunsidwe mafunso ndi mkulu wa ansembe. 28 Iye anati, “Ife tinakuletsani kuti musaphunzitsenso mʼdzina ili, koma inu mwadzaza Yerusalemu ndi chiphunzitso chanu, ndipo mukufuna kutisenzetsa imfa ya munthu ameneyu.”
29 Petro ndi atumwi enawo anayankha kuti, “Ife tiyenera kumvera Mulungu osati anthu! 30 Mulungu wa makolo athu anamuukitsa Yesu, amene inu munamupha pomupachika pa mtengo. 31 Mulungu anamukweza Iye ku dzanja lake lamanja kukhala Mfumu ndi Mpulumutsi kuti Iye apatse Aisraeli mtima wolapa ndi chikhululukiro cha machimo. 32 Ife ndife mboni za zimenezi, ndiponso Mzimu Woyera amene Mulungu anapereka kwa iwo akumvera Iye.”
33 Akuluakuluwo atamva zimenezi anakwiya kwambiri nafuna kuwapha. 34 Koma Mfarisi wina dzina lake Gamalieli, mphunzitsi wa malamulo, amene anthu onse amamulemekeza, anayimirira ndi kulamula kuti atumwiwo ayambe apita panja. 35 Ndipo iye anawuza bwalolo kuti, “Aisraeli, taganizani bwino, zimene mukufuna kuchita kwa anthu awa. 36 Pakuti masiku a mʼmbuyomu kunali Teuda amene anadzitchukitsa, ndipo anthu pafupifupi 400 anamutsatira. Iye anaphedwa ndipo omutsatira akewo anabalalitsidwa, zonse zinatheratu. 37 Pambuyo pake, nthawi ya kalembera kunalinso Yudasi wa ku Galileya, ndipo anatsogolera gulu la anthu amene anawukira, iyenso anaphedwa ndipo anthu ake onse anabalalitsidwa. 38 Chifukwa chake pa nkhani iyi ndikuwuzani kuti, alekeni anthuwa ndipo aloleni apite! Pakuti ngati zimene akuganiza kapena kuchita ndi zochokera kwa munthu zidzalephera. 39 Koma ngati ndi zochokera kwa Mulungu inu simudzatha kuwaletsa anthu awa: inu mwina muzapezeka kuti mukulimbana ndi Mulungu.”
40 Akuluakulu enawo anavomerezana naye. Iwo anayitana atumwi aja ndipo anawakwapula kwambiri. Ndipo anawalamula kuti asayankhulenso mʼdzina la Yesu ndipo anawamasula.
41 Iwo anachoka ku Bwalo Lalikulu akukondwa chifukwa anayesedwa oyenera kunyozedwa chifukwa cha dzina la Yesu. 42 Ndipo tsiku ndi tsiku, sanaleke kuphunzitsa ndi kulalikira mʼNyumba ya Mulungu komanso nyumba ndi nyumba, Uthenga Wabwino wa kuti Yesu ndi Khristu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.