New Testament in a Year
Yesu Aweruzidwa kuti Aphedwe
19 Kenaka Pilato anatenga Yesu namukwapula mwankhanza. 2 Asilikali analuka nkhata yaminga ndi kumuveka pamutu pake. Kenaka anamuveka mkanjo wapepo 3 ndipo ankapita kwa Iye mobwerezabwereza ndi kumanena kuti, “Moni mfumu ya Ayuda?” Ndipo amamumenya makofi.
4 Pilato anatulukanso ndipo anati kwa Ayuda, “Taonani, ine ndikumubweretsa kuti inu mudziwe kuti ine sindikupeza chifukwa chomuyimbira mlandu.” 5 Pamenepo Yesu anatuluka atavala nkhata yaminga ndi mkanjo wapepo ndipo Pilato anawawuza kuti, “Nayu munthu uja!”
6 Atangomuona Iye akulu a ansembe ndi akuluakulu ena anafuwula kuti, “Mpachikeni! Mpachikeni!”
Koma Pilato anayankha kuti, “Inu mutengeni ndi kumupachika. Koma ine sindikupeza chifukwa chomuyimbira mlandu.”
7 Ayuda anayimirira nati, “Ife tili ndi lamulo, ndipo molingana ndi lamulolo, Iyeyu ayenera kuphedwa chifukwa akudzitcha kuti ndi Mwana wa Mulungu.”
8 Pilato atamva zimenezi, anachita mantha kwambiri, 9 ndipo anabwereranso mʼnyumba yaufumu. Iye anafunsa Yesu kuti, “Kodi umachokera kuti?” Koma Yesu sanayankhe. 10 Pilato anati, “Kodi ukukana kundiyankhula ine? Kodi sukuzindikira kuti ine ndili ndi mphamvu yokumasula ndiponso mphamvu yokupachika?”
11 Yesu anayankha kuti, “Inu simukanakhala ndi mphamvu pa Ine akanapanda kukupatsani kumwamba. Nʼchifukwa chake amene wandipereka Ine kwa inu ndiye wochimwa kwambiri.”
12 Kuyambira pamenepo Pilato anayesa kuti amumasule Yesu, koma Ayuda anapitirira kufuwula kuti, “Ngati mumumasula munthuyu kuti apite, inu si bwenzi la Kaisara.”
13 Pilato atamva zimenezi, iye anamutulutsa Yesu kunja ndi kukhala pansi pa mpando wa woweruza pamalo otchedwa Mwala Wowaka (umene pa Chiaramaiki ndi Gabata). 14 Linali tsiku lokonzekera Sabata la Paska ndipo nthawi inali ora lachisanu ndi chimodzi masana.
Pilato anati kwa Ayuda, “Nayi mfumu yanu.”
15 Koma iwo anafuwula kuti, “Choka nayeni! Choka nayeni! Mpachikeni!”
Pilato anafunsa kuti, “Kodi ine ndipachike mfumu yanuyi?”
Akulu a ansembe anayankha kuti, “Ife tilibe mfumu ina koma Kaisara.”
16 Pomaliza Pilato anamupereka kwa iwo kuti akapachikidwe. Choncho asilikali anamutenga Yesu.
Kupachikidwa kwa Yesu
17 Atanyamula mtanda wake, anapita kumalo otchedwa “Malo a Bade” (mʼChiaramaiki amatchedwa Gologota). 18 Pamenepo iwo anamupachika Iye pamodzi ndi anthu ena awiri, mmodzi mbali ina ndi wina mbali inanso ndipo Yesu pakati.
19 Pilato analemba chikwangwani chomwe anachikhoma pa mtandapo. Panalembedwa mawu akuti, yesu wa ku nazareti, mfumu ya ayuda. 20 Ayuda ambiri anawerenga chikwangwanichi, pakuti pamalo pamene Yesu anapachikidwapo panali pafupi ndi mzinda ndipo chikwangwanicho chinalembedwa mu Chiaramaiki, Chilatini ndi Chigriki. 21 Kenaka mkulu wa ansembe wa Ayuda anakadandaula kwa Pilato nati, “Musalembe kuti ‘Mfumu ya Ayuda,’ koma kuti munthuyu amadzitcha kuti ndi mfumu ya Ayuda.”
22 Pilato anayankha kuti, “Chimene ine ndalemba, ndalemba.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.