New Testament in a Year
30 Tsopano nʼkuti Yesu asanalowe mʼmudzi, koma anali akanali pa malo pamene Marita anakumana naye. 31 Ayuda amene ankamutonthoza Mariya mʼnyumba, anaona mmene iye anayimira mofulumira ndi kutuluka kunja, iwo anamutsata akuganizira kuti ankapita ku manda kukalirira kumeneko.
32 Mariya anafika pamalo pamene panali Yesu ndipo atamuona, anagwa pa mapazi ake ndipo anati, “Ambuye mukanakhala muli kuno mlongo wanga sakanamwalira.”
33 Yesu ataona iye akulira, ndi Ayuda amene anabwera naye akuliranso, anakhudzidwa kwambiri ndi kuvutika mu mzimu. 34 Iye anafunsa kuti, “Kodi mwamuyika kuti?”
Iwo anayankha kuti, “Ambuye tiyeni mukaone.”
35 Yesu analira.
36 Pamenepo Ayuda anati, “Taonani mmene Iye anamukondera Lazaro!”
37 Koma ena a iwo anati, “Iye amatsekula maso a munthu wosaona, kodi sakanakhoza kuletsa kuti munthu uyu asamwalire?”
Yesu Aukitsa Lazaro
38 Yesu atakhudzidwanso kwambiri anafika ku manda. Manda akewo anali phanga ndipo anatsekapo ndi mwala. 39 Yesu anati, “Chotsani mwala.”
Marita mlongo wa womwalirayo anati, “Koma Ambuye, nthawi ino wayamba kununkha, pakuti wakhala mʼmenemu masiku anayi.”
40 Kenaka Yesu anati, “Kodi Ine sindinakuwuze kuti ngati iwe ukhulupirira, udzaona ulemerero wa Mulungu?”
41 Choncho iwo anachotsa mwalawo. Kenaka Yesu anayangʼana kumwamba ndikuti, “Atate, Ine ndikukuthokozani chifukwa mumandimvera. 42 Ine ndimadziwa kuti Inu mumandimvera nthawi zonse, koma Ine ndanena izi chifukwa cha anthu amene ayima pano, kuti iwo akhulupirire kuti Inu munandituma Ine.”
43 Yesu atanena izi, Iye anayitana ndi mawu ofuwula kuti, “Lazaro, tuluka!” 44 Munthu womwalirayo anatuluka, womangidwa miyendo ndi manja ndi nsalu za ku manda, ndi nkhope yake yokulungidwa nsalu.
Yesu anawawuza kuti, “Mʼmasuleni, ndipo muloleni apite.”
Ayuda Apangana za Kupha Yesu
45 Choncho Ayuda ambiri amene anabwera kudzamuchereza Mariya ndi kuona zimene Yesu anachita anamukhulupirira Iye. 46 Koma ena a iwo anapita kwa Afarisi ndi kukawawuza zimene Yesu anachita. 47 Kenaka akulu a ansembe ndi Afarisi anayitanitsa msonkhano wa akulu olamulira.
Iwo anafunsa kuti, “Kodi ife tikuchita chiyani? Pano pali munthu uyu akuchita zizindikiro zodabwitsa zambiri. 48 Ngati ife timuleka kuti apitirize chotere, aliyense adzamukhulupirira Iye, ndipo kenaka Aroma adzabwera ndi kudzatenga malo athu pamodzi ndi dziko lathu.”
49 Kenaka mmodzi wa iwo, dzina lake Kayafa, amene anali mkulu wa ansembe chaka chimenecho, anayankhula kuti, “Inu simukudziwa kanthu kalikonse! 50 Inu simukuzindikira kuti kuli bwino kwa inu kuti munthu mmodzi afe mʼmalo mwa anthu kusiyana ndi kuti mtundu wonse uwonongeke.”
51 Iye sananene izi mwa iye yekha, koma monga mkulu wa ansembe chaka chimenecho ananenera kuti Yesu anayanera kufera mtundu wa Ayuda, 52 ndipo osati mtundu okhawo komanso kwa ana ena a Mulungu onse obalalikana, kuti awabweretse pamodzi ndi kuwapanga kukhala amodzi. 53 Choncho kuyambira tsiku limeneli iwo anakonzekera za kuti amuphe.
54 Chifukwa cha ichi Yesu sanayendenso moonekera pakati pa Ayuda. Mʼmalo mwake Iye anapita ku chigawo cha kufupi ndi chipululu, ku mudzi wa Efereimu, kumene Iye anakhalako ndi ophunzira ake.
55 Nthawi ya Paska wa Ayuda itayandikira, ambiri anakwera kupita ku Yerusalemu kuchokera ku madera a ku midzi chifukwa cha mwambo wa kuyeretsedwa Paska asanafike. 56 Iwo anapitiriza kumufunafuna Yesu, ndipo pamene ankayimirira mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu anafunsana wina ndi mnzake kuti, “Kodi ukuganiza chiyani? Kodi Iye sabwera konse kuphwando?” 57 Koma akulu a ansembe ndi Afarisi anapereka lamulo kuti ngati wina aliyense adziwe kumene kunali Yesu, iye akawawuze kuti akamugwire.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.