New Testament in a Year
Amugwira Yesu
47 Pamene Iye ankayankhulabe, gulu la anthu linabwera, ndipo munthu wotchedwa Yudasi, mmodzi wa khumi ndi awiriwo analitsogolera. Iye anamuyandikira Yesu kuti amupsompsone. 48 Koma Yesu anamufunsa kuti, “Yudasi, kodi ukupereka Mwana wa Munthu ndi mpsopsono?”
49 Otsatira Yesu ataona zimene zimati zichitike, anati, “Ambuye, kodi timenyane ndi malupanga athu?” 50 Ndipo mmodzi wa iwo anatema wantchito wamkulu wa ansembe, nadula khutu lake lamanja.
51 Koma Yesu anayankha kuti, “Zisachitikenso zimenezi!” Ndipo Iye anakhudza khutu la munthuyo ndi kumuchiritsa.
52 Kenaka Yesu anafunsa akulu a ansembe, akuluakulu oyangʼanira Nyumba ya Mulungu ndi akuluakulu ena amene anabwerawo kuti, “Kodi Ine ndikutsogolera gulu lowukira kuti mubwere ndi malupanga ndi zibonga? 53 Tsiku lililonse ndinali nanu mʼmabwalo a mʼNyumba ya Mulungu ndipo inu simunandigwire. Koma iyi ndi nthawi yanu pamene mdima ukulamulira.”
Petro Akana Yesu
54 Pamenepo anamugwira Iye, napita naye ndipo anamutengera ku nyumba ya mkulu wa ansembe. Petro anamutsatira patali. 55 Koma pamene anasonkha moto pakati pa bwalo la milandu, anakhala onse pansi ndipo Petro anakhalanso pansi. 56 Mtsikana wantchito anamuona atakhala nawo pafupi ndi moto. Iye anamuyangʼanitsitsa ndipo anati, “Munthu uyu anali ndi Yesu.”
57 Koma Petro anakana nati, “Mtsikana, ine sindimudziwa ameneyu.”
58 Patatha kanthawi pangʼono, wina wake anamuona ndipo anati, “Iwenso ndiwe mmodzi mwa iwo.”
Petro anayankha kuti, “Munthu iwe, ayi sindine.”
59 Patatha pafupifupi ora limodzi, munthu winanso anati, “Zoonadi, munthu uyu anali ndi Iye, pakuti ndi mu Galileya.”
60 Petro anayankha kuti, “Munthu iwe, sindikudziwa zimene ukunena apa.” Pamene iye ankayankhula, tambala analira. 61 Ambuye anachewuka namuyangʼanitsitsa Petro. Pamenepo Petro anakumbukira mawu amene Ambuye anayankhula kwa iye kuti, “Asanalire tambala lero lino, udzandikana Ine katatu.” 62 Ndipo iye anapita panja nakalira kwambiri.
Asilikali Amuchita Chipongwe Yesu
63 Anthu amene ankalonda Yesu anayamba kumuchita chipongwe ndi kumumenya. 64 Anamumanga mʼmaso ndi kumufunsa kuti, “Tanenera! Wakumenya iwe ndi ndani?” 65 Ndipo iwo anamunena zachipongwe zambiri.
Yesu Pamaso pa Pilato ndi Herode
66 Kutacha, bungwe la akuluakulu, pamodzi ndi akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo, anakumana pamodzi, ndipo anamuyika Yesu patsogolo pawo. 67 Iwo anati, “Tiwuze, ngati ndiwe Khristu.”
Yesu anayankha kuti, “Ine nditakuwuzani simungandikhulupirire. 68 Ine nditakufunsani inu, simungandiyankhe. 69 Koma kuyambira tsopano, Mwana wa Munthu adzakhala ku dzanja lamanja la Mulungu wamphamvu.”
70 Onse anafunsa kuti, “Ndiye kuti ndiwe Mwana wa Mulungu?”
Iye anayankha kuti, “Mwanena ndinu kuti Ndine.”
71 Pamenepo iwo anati, “Nanga tikufuniranjinso umboni wina? Ife tamva kuchokera pa milomo yake.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.