Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

New Testament in a Year

Read the New Testament from start to finish, from Matthew to Revelation.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Yohane 3:19-36

19 Ndipo chiweruzo ndi ichi: kuwunika kunabwera mʼdziko lapansi, koma anthu anakonda mdima mʼmalo mwa kuwunikako, chifukwa ntchito zawo zinali zoyipa. 20 Aliyense wochita zoyipa amadana ndi kuwunika, ndipo sabwera poyera chifukwa cha mantha kuti ntchito zake zingaonekere. 21 Koma aliyense wokhala mu choonadi amabwera ku kuwunika, kuti zionekere poyera zimene iye wachita zachitika kudzera mwa Mulungu.”

Yohane Mʼbatizi Achita Umboni za Yesu

22 Zitatha izi, Yesu ndi ophunzira ake anapita mʼmadera a ku midzi ya ku Yudeya, kumene Iye anakhala kanthawi akubatiza. 23 Ndipo Yohane amabatizanso ku Ainoni kufupi ndi Salimu, chifukwa kumeneko kunali madzi ambiri ndipo anthu amabwererabwererabe kudzabatizidwa. 24 (Apa nʼkuti Yohane asanatsekeredwe mʼndende). 25 Mkangano unabuka pakati pa ophunzira ena a Yohane ndi Ayuda ena pa zamwambo wodziyeretsa wa Ayuda. 26 Iwo anabwera kwa Yohane anati, “Rabi, munthu uja munali naye mbali inayo ya mu mtsinje wa Yorodani, amene munamuchitira umboni, taonani naye akubatizanso, ndipo aliyense akupita kwa Iye.”

27 Atamva zimenezi, Yohane anayankha kuti, “Munthu amalandira chokhacho chapatsidwa kwa iye kuchokera kumwamba. 28 Inuyo ndinu mboni zanga kuti ine ndinati, ‘Ine sindine Khristu koma ndatumidwa patsogolo pa Iye.’ 29 Mwini wake wa mkwatibwi ndi mkwati. Ndipo bwenzi lamkwati limadikira ndi kumvetsera iye, ndipo amakondwa akamva mawu a mkwatiyo. Ine changa ndi chimwemwe ndipo ndine wosangalala kwambiri. 30 Nʼkoyenera kuti Iyeyo akule, ine ndichepe.

31 “Iye wochokera kumwamba ndi wapamwamba pa onse: iye wochokera mʼdziko lapansi ndi wa dziko lapansi, ndipo amayankhula monga mmodzi wa adziko lapansi. Iye wochokera kumwamba ndi wopambana onse. 32 Iye achita umboni pa zimene waziona ndi kuzimva, koma palibe avomereza umboni wake. 33 Munthu amene amawulandira akutsimikizira kuti Mulungu ndi woona. 34 Pakuti amene Mulungu wamutuma amayankhula mawu a Mulungu; Mulungu wamupatsa Mzimu Woyera mopanda malire. 35 Atate amakonda Mwana ndipo apereka zonse mʼmanja mwake. 36 Aliyense wokhulupirira Mwanayo ali ndi moyo wosatha, koma iye amene samvera Mwanayo sadzawuona moyo, pakuti mkwiyo wa Mulungu umakhala pa iye.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.