New Testament in a Year
26 Chikwangwani cholembedwapo mlandu wake chinali choti: mfumu ya ayuda. 27 Achifwamba awiri anapachikidwanso pamodzi ndi Iye, wina kumanja kwake ndi wina kumanzere kwake. 28 (Ndipo malemba anakwaniritsidwa amene amati, “Iye anayikidwa mʼgulu la anthu oyipa).” 29 Amene amadutsa pafupi anamunenera mawu amwano, akupukusa mitu yawo ndi kuti, “Haa! Iwe amene udzawononga Nyumba ya Mulungu ndi kuyimanganso masiku atatu, 30 tsika kuchoka pa mtandapo ndipo udzipulumutse wekha!”
31 Chimodzimodzinso akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo anamunyoza Iye pakati pawo. Iwo anati, “Anapulumutsa ena, koma sangathe kudzipulumutsa yekha! 32 Musiyeni Khristu, Mfumu ya Aisraeli, atsike tsopano kuchoka pa mtanda, kuti ife tione ndi kukhulupirira.” Iwonso amene anapachikidwa naye pamodzi anamulalatira.
Imfa ya Yesu
33 Pa ora lachisanu ndi chimodzi masana mdima unabwera pa dziko lonse mpaka pa ora lachisanu ndi chinayi masana. 34 Pa ora lachisanu ndi chinayi Yesu analira mofuwula kuti, “Eloi, Eloi, lama sabakitani?” Kutanthauza kuti, “Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji Ine?”
35 Ena amene anali pafupi atamva izi anati, “Tamverani, akuyitana Eliya.”
36 Munthu wina anathamanga, natenga chinkhupule atachiviyika mu vinyo wosasa, anachizika ku mtengo, ndi kumupatsa Yesu kuti amwe. Munthuyo anati, “Musiyeni yekha tsopano. Tiyeni tione ngati Eliya angabwere kudzamutsitsa.”
37 Ndi mawu ofuwula, Yesu anapuma komaliza.
38 Chinsalu chotchinga cha mʼNyumba ya Mulungu chinangʼambika pakati kuyambira pamwamba mpaka pansi. 39 Ndipo Kenturiyo, amene anayima patsogolo pa Yesu, atamva kulira kwake ndi kuona mmene anafera anati, “Zoonadi, uyu anali Mwana wa Mulungu.”
40 Amayi ena anali patali kuonerera. Pakati pawo panali Mariya Magadalena, Mariya amayi a Yakobo wamngʼono ndi Yose ndi Salome. 41 Amayi awa ankamutsatira Iye mu Galileya ndi kumutumikira Iye pa zosowa zake. Amayi enanso ambiri amene anabwera naye ku Yerusalemu analinso pomwepo.
Yesu Ayikidwa Mʼmanda
42 Linali Tsiku Lokonzekera (kunena kuti, tsiku lomwe limatsatizana ndi Sabata). Choncho madzulo atayandikira, 43 Yosefe wa ku Arimateyu, mkulu wolamulira odziwika bwino, amene amadikirira ufumu wa Mulungu, anapita kwa Pilato molimba mtima ndi kukapempha mtembo wa Yesu. 44 Pilato anadabwa pakumva kuti anali atamwalira kale. Anayitana Kenturiyo, namufunsa ngati Yesu anali atamwalira kale. 45 Atawuzidwa ndi Kenturiyo kuti zinali motero, anapereka mtembowo kwa Yosefe. 46 Choncho Yosefe anagula nsalu yabafuta, natsitsa thupi, ndipo analikulunga mʼnsalu, naliyika mʼmanda amene anawagoba pa mwala. Kenaka anagubuduza mwala umene anatseka nawo mandawo. 47 Mariya Magadalena ndi Mariya amayi a Yose anaona kumene anamuyika Yesu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.