New Testament in a Year
Za Kusudzula
10 Ndipo Yesu anachoka pamalowo ndi kupita kudera la Yudeya ndi kutsidya la mtsinje wa Yorodani. Magulu a anthu anabweranso kwa Iye, ndipo monga mwachizolowezi chake anawaphunzitsa.
2 Afarisi ena anabwera kudzamuyesa pomufunsa kuti, “Kodi malamulo amalola kuti mwamuna asiye mkazi wake?”
3 Iye anayankha kuti, “Kodi Mose anakulamulani chiyani?”
4 Iwo anati, “Mose amaloleza mwamuna kulemba kalata ya chisudzulo ndi kumuchotsa mkazi.”
5 Yesu anayankha kuti, “Mose anakulemberani lamulo ili chifukwa chakuwuma kwa mitima yanu. 6 Koma pachiyambi cha chilengedwe, Mulungu ‘analenga iwo, mwamuna ndi mkazi.’ 7 ‘Pa chifukwa ichi mwamuna adzasiya abambo ake ndi amayi ake nakaphatikana ndi mkazi wake, 8 ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi.’ Potero sali awirinso, koma mmodzi. 9 Chifukwa chake chimene Mulungu wachilumikiza pamodzi, munthu wina asachilekanitse.”
10 Pamene analinso mʼnyumba, ophunzira anamufunsa Yesu za izi. 11 Iye anayankha kuti, “Aliyense amene aleka mkazi wake ndi kukakwatira wina achita chigololo kulakwira mkaziyo. 12 Ndipo akasiya mwamuna wake ndi kukakwatiwa ndi wina, achita chigololo.”
Yesu Adalitsa Ana
13 Anthu anabweretsa ana kwa Yesu kuti awadalitse, koma ophunzira anawadzudzula. 14 Pamene Yesu anaona zimenezi anayipidwa. Anati kwa iwo, “Lolani ana abwere kwa Ine, ndipo musawaletse, pakuti Ufumu wa Mulungu uli wa onga awa. 15 Ndikukuwuzani choonadi, aliyense amene sadzalandira Ufumu wa Mulungu ngati kamwana sadzalowamo.” 16 Ndipo ananyamula ana mʼmanja ake, ndi kuyika manja ake pa iwo nawadalitsa.
Munthu Wachuma ndi Ufumu wa Mulungu
17 Yesu atanyamuka, munthu wina anamuthamangira nagwa mogwada pamaso pake. Iye anafunsa kuti, “Aphunzitsi abwino, ndichite chiyani kuti ndilandire moyo wosatha?”
18 Yesu anamufunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani ukunditchula wabwino? Palibe wabwino koma Mulungu yekha. 19 Iwe umadziwa malamulo: ‘Usaphe, usachite chigololo, usabe, usapereke umboni wonama, usachite chinyengo, lemekeza abambo ndi amayi ako.’ ”
20 Iye anati, “Aphunzitsi zonsezi ndinazisunga kuyambira ndili mnyamata.”
21 Yesu anamuyangʼana ndi kumukonda nati, “Ukusowa chinthu chimodzi. Pita, kagulitse zonse zimene uli nazo ndipo kapereke kwa osauka, ndipo udzakhala ndi chuma kumwamba. Ndipo ukabwere ndi kunditsata Ine.”
22 Pa chifukwa ichi nkhope yake inagwa. Anachoka ali wachisoni, chifukwa anali ndi chuma chambiri.
23 Yesu anayangʼanayangʼana ndipo anati kwa ophunzira ake, “Nʼkovutadi kuti achuma akalowe mu ufumu wa Mulungu!”
24 Ophunzira anadabwa ndi mawu ake. Koma Yesu anatinso, “Ananu, nʼkovutadi kulowa mu ufumu wakumwamba! 25 Ndi kwapafupi kwa ngamira kuti idzere pa kabowo ka zingano kusiyana ndi munthu wachuma kuti alowe mu ufumu wa Mulungu.”
26 Ophunzira anadabwa kwambiri, ndipo anati kwa wina ndi mnzake, “Nanga ndani amene angapulumuke?”
27 Yesu anawayangʼana ndipo anati, “Kwa munthu zimenezi nʼzosatheka, koma osati ndi Mulungu; zinthu zonse zimatheka ndi Mulungu.”
28 Petro anati kwa Iye, “Ife tasiya zonse ndi kukutsatani!”
29 Yesu anayankha kuti, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti palibe aliyense amene wasiya nyumba kapena abale kapena alongo kapena amayi kapena abambo kapena ana kapena minda chifukwa cha Ine ndi Uthenga Wabwino 30 adzalephera kulandira 100 (nyumba, abale, alongo, amayi, ana ndi minda, pamodzi ndi mazunzo) mʼbado uno ndi moyo wosatha nthawi ya mʼtsogolo. 31 Koma ambiri amene ndi woyambirira adzakhala omalizira, ndipo omalizira adzakhala oyambirira.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.