New Testament in a Year
Yesu Adzozedwa ku Betaniya
14 Tsopano panali patatsala masiku awiri okha kuti tsiku la Paska ndi Phwando la Buledi wopanda yisiti lifike, ndipo akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo ankafunafuna mpata woti amugwire Yesu ndi kumupha. 2 Iwo anati, “Koma osati nthawi yaphwando, chifukwa anthu angachite chiwawa.”
3 Pamene Iye anali mʼBetaniya, atakhala pa tebulo akudya mʼnyumba ya munthu wodziwika kuti Simoni wakhate, anabwera mayi ndi botolo la mafuta onunkhira amtengo wapamwamba opangidwa ndi nadi. Anaphwanya botololo nakhuthula mafutawo pa mutu wa Yesu.
4 Ena mwa iwo amene analipo, anakwiya nati kwa wina ndi mnzake, “Chifukwa chiyani akuwononga mafuta onunkhirawa? 5 Akanatheka kugulitsidwa ndi ndalama zambiri zoposa malipiro a pa chaka ndipo ndalamazo ndi kupatsa osauka.” Ndipo anamudzudzula iye mwaukali.
6 Yesu anati, “Musiyeni, chifukwa chiyani mukumuvutitsa? Wandichitira Ine chinthu chabwino. 7 Anthu osauka mudzakhala nawo nthawi zonse, ndipo mukhoza kuwathandiza nthawi iliyonse mungafune. Koma simudzakhala ndi Ine nthawi zonse. 8 Wachita zimene akanatha. Wathira mafuta onunkhira pa thupi langa nthawi isanakwane kukonzekera kuyikidwa kwanga mʼmanda. 9 Zoonadi, ndikuwuzani kuti kulikonse kumene Uthenga Wabwino udzalalikidwa pa dziko lonse, zimene wachitazi zidzanenedwa pomukumbukira iye.”
10 Kenaka Yudasi Isikarioti, mmodzi mwa khumi ndi awiriwo, anapita kwa akulu a ansembe kuti akamupereke Yesu. 11 Iwo anakondwa pakumva zimenezi ndipo analonjeza kumupatsa iye ndalama. Ndipo ankadikira mpata wabwino woti amupereke.
Mgonero wa Ambuye
12 Pa tsiku loyamba la Phwando la Buledi wopanda yisiti, nthawi imene mwa mwambo inali ya kupha mwana wankhosa wa Paska, ophunzira a Yesu anafunsa Iye kuti, “Mufuna tipite kuti kumene tikakonzekere kuti mukadyere Paska?”
13 Pamenepo anatumiza awiri mwa ophunzira ake, nawawuza kuti, “Pitani mu mzinda, ndipo mukakumana ndi mwamuna wonyamula mtsuko wa madzi. Kamutsatireni iye. 14 Kawuzeni mwini nyumba imene iye akalowemo kuti, ‘Aphunzitsi akufunsa: kodi chili kuti chipinda changa cha alendo, kumene ndidyere Paska ndi ophunzira anga?’ 15 Iye adzakuonetsani chipinda chachikulu chapamwamba, chokhala kale ndi zonse ndi chokonzedwa kale. Katikonzereni ife Paska kumeneko.”
16 Ophunzirawo anachoka, napita mu mzindawo ndipo anakapeza zinthu monga mmene Yesu anawawuzira. Choncho anakakonza Paska.
17 Ndipo kutada Yesu anafika ndi khumi ndi awiriwo. 18 Pamene ankadya pa tebulo Iye anati, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti mmodzi wa inu adzandipereka, mmodzi amene akudya ndi Ine.”
19 Iwo anamva chisoni, ndipo mmodzi ndi mmodzi anati kwa Iye, “Kodi ndine?”
20 Iye anayankha kuti, “Ndi mmodzi mwa khumi ndi awirinu, amene akusunsa buledi mʼmbale pamodzi ndi Ine. 21 Mwana wa Munthu adzapita monga momwe zinalembedwera za Iye. Koma tsoka kwa munthu amene adzapereka Mwana wa Munthu! Kukanakhala bwino kwa iye akanapanda kubadwa.”
22 Pamene ankadya, Yesu anatenga buledi, nayamika ndipo anamunyema nagawira ophunzira ake nanena kuti, “Tengani, ili ndi thupi langa.”
23 Kenaka anatenga chikho, nayamika nachipereka kwa iwo ndipo onse anamweramo.
24 Iye anawawuza kuti, “Awa ndi magazi anga a pangano amene akhetsedwa chifukwa cha ambiri. 25 Zoonadi, ndikuwuzani kuti sindidzamwanso kuchokera ku chipatso cha mphesa mpaka tsikulo pamene ndidzamwa chatsopano mu ufumu wa Mulungu.”
26 Atayimba nyimbo, anapita ku phiri la Olivi.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.