New Testament in a Year
Yesu Adyetsa Anthu 5,000
30 Atumwi anasonkhana mozungulira Yesu namufotokozera zonse zomwe anachita ndi kuphunzitsa. 31 Popeza kuti panali anthu ambiri amene amabwera ndi kumapita, analibe mpata wakuti adye, ndipo Iye anawawuza kuti, “Tiyeni kuno kumalo achete kuti tikapume.”
32 Ndipo anachoka okha pa bwato napita kumalo a okhaokha. 33 Koma ambiri amene anawaona akuchoka anawazindikira ndipo anathamanga wapansi kuchokera mʼmidzi yonse nakayambirira kufika. 34 Yesu atafika ku mtunda ndi kuona gulu lalikulu la anthu, anamva nawo chisoni chifukwa anali ngati nkhosa zopanda mʼbusa. Ndipo anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.
35 Pa nthawi iyi nʼkuti dzuwa litapendeka, ndipo ophunzira ake anabwera kwa Iye nati, “Kuno ndi kuthengo, ndipo ano ndi madzulo. 36 Awuzeni anthuwa azipita ku midzi ndi madera ozungulira, kuti akadzigulire kanthu kakuti adye.”
37 Koma Iye anayankha kuti, “Apatseni kanthu koti adye.”
Iwo anati kwa Iye, “Apa pafunika ndalama za miyezi isanu ndi itatu zomwe munthu amalandira! Kodi tipite kukagwiritsa ntchito ndalama zotere kugulira buledi kuti tiwapatse adye?”
38 Iye anawafunsa kuti, “Muli ndi malofu a buledi angati? Pitani mukaone.”
Ataona anati kwa Iye, “Asanu ndi nsomba ziwiri.”
39 Pamenepo Yesu anawalamulira kuti awakhazike anthu pansi mʼmagulu pa msipu obiriwira. 40 Ndipo anakhala pansi mʼmagulu a anthu 100 ndi gulu la anthu makumi asanu. 41 Atatenga malofu a buledi asanu ndi nsomba ziwiri, nayangʼana kumwamba, Iye anayamika nagawa malofu a bulediwo. Kenaka anawapatsa ophunzira ake kuti awapatse anthu. Ndipo anagawanso nsomba ziwirizo kwa onse. 42 Onse anadya ndipo anakhuta, 43 ndipo ophunzira ake anatola buledi ndi nsomba zotsalira zokwanira madengu khumi ndi awiri. 44 Chiwerengero cha amuna amene anadya chinali 5,000.
Yesu Ayenda pa Nyanja
45 Nthawi yomweyo Yesu anawuza ophunzira ake kuti alowe mʼbwato ndi kuti atsogole kupita ku Betisaida, pamene Iye ankawuza anthu kuti azipita. 46 Atawasiya, Iye anakwera ku phiri kukapemphera.
47 Pofika madzulo, bwato linali pakati pa nyanja, ndipo Iye anali yekha pa mtunda. 48 Iye anaona ophunzira ake akuvutika popalasa bwato, chifukwa mphepo imawomba mokumana nawo. Pa nthawi ya mʼbandakucha Iye anafika kwa iwo akuyenda pa nyanja. Anali pafupi kuwapitirira, 49 koma atamuona Iye akuyenda pa nyanja, anaganiza kuti anali mzukwa. Iwo anafuwula, 50 pakuti onse anamuona ndipo anachita mantha.
Nthawi yomweyo Iye anawayankhula nati, “Limbani mtima! Ndine. Musachite mantha.” 51 Ndipo Iye anakwera mʼbwato pamodzi nawo, ndipo mphepo inaleka. Iwo anadabwa kwambiri, 52 popeza sanazindikire zimene zinachitika pa malofu a buledi; pakuti mitima yawo inali yowuma.
53 Atawoloka, anafika ku Genesareti nayima pa dooko. 54 Atangotuluka mʼbwato, anthu anamuzindikira Yesu. 55 Anathamanga uku ndi uko mʼdera lonse nakanyamula odwala pa machira kupita nawo kulikonse kumene anamva kuti kuli Iye. 56 Ndipo kulikonse kumene anapita, ku midzi, mʼmizinda ndi madera a ku midzi, iwo anayika odwala mʼmalo a mʼmisika. Iwo anamupempha kuti awalole kuti akhudze ngakhale mphonje za mkanjo wake, ndipo onse amene anamukhudza anachira.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.