Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

New Testament in a Year

Read the New Testament from start to finish, from Matthew to Revelation.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Marko 4:1-20

Fanizo la Wofesa Mbewu

Nthawi inanso Yesu atakhala mʼmbali mwa nyanja, anayamba kuphunzitsa. Gulu lalikulu la anthu linasonkhana momuzungulira kotero kuti Iye analowa mʼbwato lomwe linali pa nyanja nakhalamo, anthu onse ali pa mtunda mʼmbali mwa madzi. Anawaphunzitsa zinthu zambiri mʼmafanizo, ndipo mʼchiphunzitso chake anati: “Tamverani! Mlimi anapita kukafesa mbewu zake. Akufesa, mbewu zina zinagwera mʼmbali mwa njira, ndipo mbalame zinabwera ndi kuzidya. Zina zinagwa pa malo a miyala pamene panalibe dothi lambiri. Zinamera mofulumira chifukwa panalibe dothi lambiri. Koma dzuwa litakwera, mbewuzo zinapserera, ndipo zinawuma chifukwa zinalibe mizu. Mbewu zina zinagwa pa minga, ndipo mingayo inayanga ndi kuzirepheretsa kukula. Mbewu zinanso zinagwa pa nthaka yabwino ndipo zinamera, zinakula ndi kubereka zipatso, zina zochuluka makumi atatu, zina makumi asanu ndi limodzi ndi zina 100.”

Pamenepo Yesu anati, “Amene ali ndi makutu akumva, amve.”

10 Ali yekha, ophunzira ndi ena omuzungulira, anamufunsa za mafanizo. 11 Iye anawawuza kuti, “Chinsinsi cha ufumu wa Mulungu chapatsidwa kwa inu. Koma kwa amene ali kunja zinthu zonse zinenedwa mʼmafanizo: 12 kotero kuti,

“ ‘Kupenya mudzapenya koma osaona kanthu,
    kumva mudzamva koma osamvetsetsa,
kuti mwina angatembenuke ndi kukhululukidwa!’ ”

13 Pamenepo Yesu anawawuza kuti, “Kodi simukulimvetsa fanizoli? Kodi nanga mudzazindikira bwanji fanizo lina lililonse? 14 Wofesa amafesa mawu. 15 Anthu ena ali ngati mbewu za mʼmbali mwa njira, mʼmene mawu amafesedwamo. Akangowamva, Satana amabwera ndi kuchotsa mawu amene anafesedwa mwa iwo. 16 Ena, monga mbewu zofesedwa pa miyala, amamva mawu ndipo nthawi yomweyo amawalandira ndi chimwemwe. 17 Koma popeza alibe mizu, amakhala kwa kanthawi kochepa. Mavuto kapena masautso akafika chifukwa cha mawu, amagwa mofulumira. 18 Komabe ena, monga mbewu zofesedwa pakati pa minga, amamva mawu; 19 koma nkhawa zamoyo uno, chinyengo cha chuma ndi zokhumba za zinthu zina zimabwera ndi kutchinga mawu, ndipo amawachititsa kukhala osabala chipatso. 20 Ena, ngati mbewu zofesedwa pa nthaka yabwino, amamva mawu, nawalandira, ndi kubereka zipatso zokwanira makumi atatu, makumi asanu ndi limodzi, kapena ngakhale 100 kuwonjezera pa zomwe zinafesedwa.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.