Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

New Testament in a Year

Read the New Testament from start to finish, from Matthew to Revelation.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Marko 3:1-19

Yesu Achiritsa Wolumala Dzanja

Nthawi inanso analowa mʼsunagoge, ndipo munthu wa dzanja lolumala anali momwemo. Ena a iwo anafunafuna chifukwa chakuti akamuneneze Yesu, potero anamuyangʼanitsitsa kuti aone ngati angamuchiritse tsiku la Sabata. Yesu anati kwa munthu wolumala dzanjayo, “Imirira, bwera kuno kutsogolo.”

Ndipo Yesu anawafunsa kuti, “Kodi chololedwa ndi chiyani pa tsiku la Sabata: kuchita chabwino kapena kuchita choyipa, kupulumutsa moyo kapena kupha?” Koma iwo anakhala chete.

Yesu anawayangʼana ndi mkwiyo ndipo powawidwa mtima chifukwa cha mitima yawo yowuma anati kwa munthuyo, “Wongola dzanja lako.” Iye analiwongola, ndipo dzanja lake linachira. Kenaka Afarisi anatuluka nayamba kukonza chiwembu ndi Aherode mmene angamuphere Yesu.

Magulu a Anthu Amutsata Yesu

Yesu anachoka pamodzi ndi ophunzira ake napita ku nyanja, ndipo gulu lalikulu la anthu lochokera ku Galileya linamutsata. Atamva zonse zimene amachita, anthu ambiri anabwera kwa Iye kuchokera ku Yudeya, Yerusalemu, Idumeya ndi madera a ku tsidya kwa mtsinje wa Yorodani ndi ozungulira Turo ndi Sidoni. Chifukwa cha gulu la anthu, anawuza ophunzira ake kuti apezeretu bwato likhale, kuti anthu angamupanikize. 10 Pakuti anachiritsa ambiri, kotero kuti iwo amene anali ndi matenda amakankhana kutsogolo kuti amukhudze. 11 Nthawi iliyonse mizimu yoyipa ikamuona, imagwa pansi pamaso pake ndi kufuwula kuti, “Inu ndinu Mwana wa Mulungu!” 12 Koma anayichenjeza mwamphamvu kuti isanene kuti Iye anali ndani.

Yesu Asankha Ophunzira Khumi ndi Awiri

13 Yesu anakwera ku phiri ndipo anayitana amene anawafuna, ndipo anabwera kwa Iye. 14 Iye anasankha khumi ndi awiri, nawayika akhale atumwi; pokhala ndi Iye aziwatuma kukalalikira 15 ndi kuti akhale ndi ulamuliro wotulutsa ziwanda. 16 Awa ndi khumi ndi awiri amene anawasankha: Simoni (amene anapatsidwa dzina lakuti Petro); 17 Yakobo mwana wa Zebedayo, ndi mʼbale wake Yohane (iwowa anawapatsa dzina lakuti Bowanege, ndiye kuti ana a bingu); 18 Andreya, Filipo, Bartumeyu, Mateyu, Tomasi, Yakobo mwana wa Alufeyo, Tadeyo, Simoni Zelote, 19 ndi Yudasi Isikarioti, amene anamupereka Iye.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.