M’Cheyne Bible Reading Plan
Rahabe ndi Anthu Ozonda Dziko
2 Tsono Yoswa mwana wa Nuni anatuma anthu awiri okazonda dziko mwachinsinsi kuchokera ku Sitimu. Iye anawawuza kuti, “Pitani mukaone dzikolo makamaka mzinda wa Yeriko.” Kotero iwo anapita ndipo anakafika ku nyumba ya mkazi wadama dzina lake Rahabe, ndipo anagona kumeneko.
2 Mfumu ya Yeriko inawuzidwa kuti, “Aisraeli ena afika mu mzinda muno usiku uno kudzazonda dziko.” 3 Choncho Mfumu ya Yeriko inatumiza uthenga kwa Rahabe kuti, “Atulutse anthu amene abwera ku nyumba kwakowo chifukwa iwo abwera kuti adzazonde dzikoli.”
4 Koma pa nthawiyi nʼkuti mkaziyo atatenga amuna awiriwo ndi kuwabisa. Tsono anayankha kuti, “Inde, anthuwo anafikadi ku nyumba kuno. Koma sindinadziwe kumene anachokera. 5 Iwo achoka kuno ndi chisisira, chipata cha mzinda chili pafupi kutsekedwa. Ndiye sindidziwa kumene alowera. Koma mukawalondola msanga muwapeza.” 6 Koma nʼkuti atawakweza pa denga azondiwo ndi kuwabisa pansi pa mapesi a thonje amene iye anawayika pa dengapo. 7 Nthumwi za mfumu zija zitatuluka ndipo chipata chinatsekedwa. Nthumwizo zinapita kukawafunafuna azondi aja mpaka ku dooko la Yorodani.
8 Azondiwo asanagone, Rahabe anakwera pa denga 9 ndipo anawawuza kuti, “Ine ndikudziwa kuti Yehova wakupatsani dziko lino ndipo tili ndi mantha. Anthu onse a mʼdziko lino ali ndi mantha chifukwa cha inu. 10 Ife tinamva mmene Yehova anawumitsira madzi a Nyanja Yofiira inu mukufika pamene munatuluka mʼdziko la Igupto. Tamvanso zimene munachita kwa Sihoni ndi Ogi, mafumu awiri a Aamori amene ali kummawa kwa Yorodani. Inu munawawononga kotheratu. 11 Titamva zimenezi, ife tinataya mtima ndipo aliyense wa ife ali ndi mantha chifukwa cha inu. Tikudziwa kuti Yehova Mulungu wanu ndi Mulungu wa kumwamba ndi dziko lapansi. 12 Choncho mulumbire pamaso pa Yehova ndi kundipatsa chizindikiro choti mudzachitadi zimene mwalonjeza, kuti monga inu ndakuchitirani chifundo, inunso mudzachitira chifundo a pa banja la abambo anga. 13 Inu mulonjeze kuti simudzapha abambo anga ndi amayi anga, abale anga ndi alongo anga ndi mabanja awo omwe.”
14 Anthuwo anamuyankha kuti, “Ife ndife okonzeka kufa chifukwa cha inu. Ngati iwe sudzawulula zimene tachitazi, ndiye kuti ife tidzakukomera mtima ndi kusunga pangano lathu ndi iwe, Yehova akadzatipatsa dziko lino.”
15 Popeza nyumba ya Rahabe inali pa linga la mzindawo, azondi aja anatulukira pa zenera. Rahabe anawatsitsa pansi ndi chingwe. 16 Iye anawawuza kuti, “Pitani ku mapiri kuti okuthamangiraniwo asakupezeni. Mukabisale kumeneko masiku atatu mpaka iwo atabwerera, ndipo kenaka muzikapita kwanu.”
17 Anthuwo anati kwa iye, “Lonjezo limene watichititsa ifeli tidzalisungadi 18 tikadzalowa mʼdzikoli, iwe udzamangirire kansalu kofiira pa zenera limene unatitulutsira, ndi kusonkhanitsa abambo ako, amayi ako, abale ako ndi banja lako lonse mʼnyumba muno. 19 Ngati wina aliyense adzatuluka mʼnyumbamo kuti azikayendayenda mu msewu, magazi ake adzakhala pamutu pake, ife sitidzapalamula kanthu. Koma wina aliyense wokhala mʼnyumba mwakomo akadzaphedwa, mlandu udzakhala wathu. 20 Komanso iwe ukangowulula zimene ife tikuchitazi ndiye kuti ife sitidzasunga zimene talonjezazi.”
21 Rahabe anayankha kuti, “Zikhale monga mwaneneramo.” Kenaka iye anawatulutsa ndipo iwowo anapita. Pambuyo pake Rahabe anamangirira kansalu kofiira pa zenera paja.
22 Azondi aja anachoka napita ku mapiri ndipo anakhalako masiku atatu. Apa nʼkuti otumidwa ndi mfumu aja atawafunafuna ponseponse nʼkubwerera osawapeza. 23 Pambuyo pake azondi awiri aja anayamba ulendo wobwerera kwawo. Anatsika ku mapiri kuja, nawoloka mtsinje mpaka anakafika kwa Yoswa mwana wa Nuni. Ndipo anamuwuza zonse zimene zinawachitikira. 24 Iwo anati kwa Yoswa, “Ndithu, Yehova wapereka dziko lonse mʼmanja mwathu. Anthu onse kumeneko akuchita nafe mantha.”
Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.
123 Ndikweza maso anga kwa Inu,
kwa Inu amene mumakhala kumwamba.
2 Taonani, monga momwe maso a akapolo amayangʼana mʼdzanja la mbuye wawo,
monga momwenso maso a mdzakazi amayangʼana mʼdzanja la dona wake,
choncho maso athu ali kwa Yehova Mulungu wathu,
mpaka atichitire chifundo.
3 Mutichitire chifundo, Inu Yehova mutichitire chifundo,
pakuti tapirira chitonzo chachikulu.
4 Ife tapirira mnyozo wambiri kuchokera kwa anthu odzikuza,
chitonzo chachikulu kuchokera kwa anthu onyada.
Salimo la Davide. Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.
124 Akanapanda kukhala mbali yathu Yehova,
anene tsono Israeli,
2 akanapanda kukhala mbali yathu Yehova,
potiwukira anthuwo,
3 iwo atatipsera mtima,
akanatimeza amoyo;
4 chigumula chikanatimiza,
mtsinje ukanatikokolola,
5 madzi a mkokomo
akanatikokolola.
6 Atamandike Yehova,
amene sanalole kuti tikhale chakudya cha mano awo.
7 Moyo wathu wawonjoka ngati mbalame
yokodwa mu msampha wa mlenje;
msampha wathyoka,
ndipo ife tapulumuka.
8 Thandizo lathu lili mʼdzina la Yehova
wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.
Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.
125 Amene amadalira Yehova ali ngati phiri la Ziyoni,
limene silingagwedezeke koma ndi lokhala mpaka muyaya.
2 Monga mapiri azungulira Yerusalemu,
momwemonso Yehova azungulira anthu ake
kuyambira tsopano mpaka muyaya.
3 Ndodo yaufumu ya anthu oyipa sidzakhala
pa dziko limene lapatsidwa kwa anthu olungama,
kuti anthu olungamawo
angachite nawonso zoyipa.
4 Yehova chitirani zabwino amene ndi abwino,
amene ndi olungama mtima
5 Koma amene amatembenukira ku njira zokhotakhota,
Yehova adzawachotsa pamodzi ndi anthu ochita zoyipa.
Mtendere ukhale pa Israeli.
Dzina Latsopano la Ziyoni
62 Chifukwa chokonda Ziyoni sindidzakhala chete,
chifukwa chokonda Yerusalemu sindidzakhala chete,
mpaka chilungamo chake chitaoneka poyera ngati kuwala,
ndi chipulumutso chake chitaoneka ngati sakali yoyaka.
2 Mitundu ya anthu idzaona iwe utapambana pa nkhondo
ndipo mafumu onse adzaona ulemerero wako.
Adzakuyitanira dzina latsopano
limene adzakupatse ndi Yehova.
3 Udzakhala ngati chipewa chaulemerero mʼdzanja la Yehova,
ndi ngati nduwira yaufumu mʼdzanja la Mulungu wako.
4 Sadzakutchanso “Wosiyidwa,”
ndipo dziko lako silidzatchedwanso “Chipululu.”
Koma dzina lako latsopano lidzakhala “Ndakondwera naye.”
Ndipo dziko lako lidzatchedwa “Wokwatiwa.”
Chifukwa Yehova akukondwera nawe,
ndipo adzakhala ngati mwamuna wa dziko lako.
5 Monga mnyamata amakwatira namwali,
momwenso mmisiri wodzakumanga adzakukwatira;
monga mkwati amakondwera ndi mkwatibwi,
chonchonso Mulungu adzakondwera nawe.
6 Iwe Yerusalemu, pa malinga ako ndayikapo alonda;
sadzakhala chete usana kapena usiku.
Inu amene mumakumbutsa Yehova za malonjezo ake
musapumule.
7 Musamupatse mpata wopuma mpaka atakhazikitsa Yerusalemu
kukhala mzinda umene dziko lapansi lidzawutamande.
8 Yehova analumbira atakweza dzanja lake.
Anati,
“Sindidzaperekanso tirigu wako
kuti akhale chakudya cha adani ako,
ndipo alendo sadzamwanso vinyo wako watsopano
pakuti unamuvutikira.
9 Koma amene amakakolola ndiwo amene adzadye buledi
ndi kutamanda Yehova,
ndipo amene amasonkhanitsa pamodzi mphesa ndiwo amene adzamwe vinyo
mʼmabwalo a Nyumba yanga.”
10 Tulukani, dutsani pa zipata!
Konzerani anthu njira.
Lambulani, lambulani msewu waukulu!
Chotsani miyala.
Kwezani mbendera kuti mitundu ya anthu izione.
11 Yehova walengeza
ku dziko lonse lapansi kuti,
Awuzeni anthu a ku Yerusalemu kuti,
“Taonani, chipulumutso chanu chikubwera;
Yehova akubwera ndi mphotho yake
akubwera nazo zokuyenerani.”
12 Iwo adzatchedwa Anthu Opatulika,
owomboledwa a Yehova;
ndipo adzakutchani “Okondwa a Yehova”
“Mzinda umene Yehova sanawusiye.”
Yesu Atuma Ophunzira Ake
10 Yesu anayitana ophunzira ake khumi ndi awiri ndipo anawapatsa ulamuliro otulutsa mizimu yoyipa ndi kuchiritsa nthenda iliyonse ndi zofowoka zilizonse.
2 Mayina a atumwi khumi ndi awiriwo ndi awa: woyamba, Simoni (wotchedwa Petro) ndi mʼbale wake Andreya; Yakobo mwana wa Zebedayo ndi mʼbale wake Yohane, 3 Filipo ndi Bartumeyu, Tomasi ndi Mateyu wolandira msonkho, Yakobo mwana wa Alufeyo ndi Tadeyo; 4 Simoni Mzerote ndi Yudasi Isikarioti, amene anamupereka Iye.
5 Yesu anatuma khumi ndi awiriwo ndi kuwalamula kuti, “Musapite kwa anthu a mitundu ina kapena kulowa mʼmudzi uliwonse wa Asamariya. 6 Koma pitani kwa nkhosa zotayika za banja la Israeli. 7 Pamene mukupita, muzikalalikira uthenga uwu: ‘Ufumu wakumwamba wayandikira.’ 8 Chiritsani odwala, ukitsani akufa, chiritsani akhate, tulutsani ziwanda. Munalandira kwaulere, perekani kwaulere.
9 “Musatenge ndalama zagolide kapena zasiliva kapena zakopala mʼzikwama mwanu; 10 musatenge thumba la paulendo, kapena malaya awiri kapena nsapato kapena ndodo; pakuti wantchito ayenera kulandira chakudya chake. 11 Mukalowa mu mzinda ndi mʼmudzi uliwonse, funafunani munthu woyenera ndipo mukhale mʼnyumba mwake kufikira mutachoka. 12 Pamene mulowa mʼnyumba mupereke moni. 13 Mtendere wanu ukhale pa a mʼnyumbayo ngati ndi oyenera. Koma ngati siwoyenera, mtendere wanu ubwerere kwa inu. 14 Ngati wina aliyense sakakulandirani kapena sakamvera mawu anu, musase fumbi la kumapazi anu pamene mutuluka mʼnyumbayo kapena mu mzindawo. 15 Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti pa tsiku lachiweruziro, mlandu wa Sodomu ndi Gomora udzachepa kusiyana ndi wa mzindawo.
16 “Taonani ndikukutumizani inu monga nkhosa pakati pa mimbulu. Chifukwa chake khalani ochenjera ngati njoka ndi woona mtima ngati nkhunda. 17 Chenjerani ndi anthu pakuti adzakuperekani ku mabwalo amilandu nadzakukwapulani mʼmasunagoge mwawo. 18 Chifukwa cha Ine, mudzaperekedwa kwa olamulira ndi kwa mafumu kuti mukhale mboni kwa iwo ndi kwa a mitundu ina. 19 Koma pamene akumangani, inu musadandaule kuti mukanena bwanji kapena mukanena chiyani. Mudzapatsidwa pa nthawi imeneyo zoti munene, 20 pakuti sindinu mudzanena, koma Mzimu Woyera wa Atate anu, adzayankhula mwa inu.
21 “Mʼbale adzapereka mʼbale kuti aphedwe ndi abambo mwana wawo: ndipo ana adzawukira makolo awo ndi kuwapereka kuti aphedwe. 22 Anthu onse adzada inu chifukwa cha Ine, koma iye amene apirira mpaka kumapeto, adzapulumuka. 23 Pamene akuzunzani pamalo ena thawirani kwina. Pakuti ndikuwuzani zoonadi kuti simudzamaliza mizinda yonse ya Israeli Mwana wa Munthu asanabwere.
24 “Wophunzira saposa mphunzitsi wake ndipo wantchito saposa bwana wake. 25 Nʼkoyenera kuti wophunzira akhale ngati mphunzitsi wake, ndi wantchito akhale ngati bwana wake. Ngati mwini banja atchedwa Belezebabu, koposa kotani a mʼnyumba mwake!
26 “Chifukwa chake musaope iwo. Pakuti palibe chinthu chobisika chimene sichidzavundukulidwa, ndi chobisika chimene sichidzadziwika. 27 Chimene ndikuwuzani Ine mu mdima, muchiyankhule poyera; chimene akunongʼonezani mʼkhutu, muchilalikire muli pa denga. 28 Musamaope amene amapha thupi koma sangathe kuchotsa moyo. Koma muziopa Iye amene akhoza kupha mzimu ndi kuwononga thupi mu gehena. 29 Kodi suja amagulitsa mbalame ziwiri ndi ndalama imodzi? Koma palibe imodzi ya izo imene idzagwa pansi wopanda chifuniro cha Atate anu. 30 Ndipo ngakhale tsitsi la mʼmutu mwanu linawerengedwa kale. 31 Potero musaope; inu ndinu a mtengo woposa mbalame zambiri.
32 “Aliyense amene avomereza Ine pamaso pa anthu, Inenso ndidzavomereza pamaso pa Atate anga akumwamba. 33 Koma iye amene andikana Ine pamaso pa anthu, Inenso ndidzamukana pamaso pa Atate anga akumwamba.
34 “Musaganize kuti Ine ndabweretsa mtendere pa dziko lapansi. Sindinabwere kudzapereka mtendere koma lupanga. 35 Pakuti Ine ndabwera kudzalekanitsa
“ ‘Munthu ndi abambo ake,
mwana wamkazi ndi amayi ake,
mtengwa kulekanitsidwa ndi apongozi ake,
36 adani a munthu adzakhala a mʼbanja mwake momwe.’
37 “Aliyense amene akonda abambo kapena amayi ake koposa Ine sayenera kukhala wanga; aliyense amene akonda mwana wake wamwamuna kapena wamkazi koposa Ine sayenera kukhala wanga. 38 Aliyense amene satenga mtanda wake ndi kunditsata Ine sayenera kukhala wanga. 39 Aliyense amene asunga moyo wake adzawutaya koma aliyense amene ataya moyo chifukwa cha Ine adzawupeza.
40 “Iye amene alandira inu alandira Ine, ndipo amene alandira Ine alandiranso amene anandituma Ine. 41 Aliyense amene alandira mneneri chifukwa chakuti ndi mneneri alandira mphotho ya mneneri, ndipo aliyense amene alandira munthu wolungama chifukwa chakuti ndi munthu wolungama, adzalandira mphotho ya wolungama. 42 Ngati aliyense apereka madzi ozizira a mʼchikho kwa mmodzi wa angʼonoangʼono awa chifukwa cha kuti ndi ophunzira anga, ndikuwuzani zoona, ndithudi sadzataya mphotho yake.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.