Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Readings for Celebrating Advent

Scripture passages that focus on the meaning of Advent and Christmas.
Duration: 35 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 100

Salimo. Nyimbo yothokoza.

100 Fuwulani kwa Yehova mwachimwemwe, inu dziko lonse lapansi.
    Mulambireni Yehova mosangalala;
    bwerani pamaso pake ndi nyimbo zachikondwerero.
Dziwani kuti Yehova ndi Mulungu.
    Iye ndiye amene anatipanga ndipo ife ndife ake;
    ndife anthu ake, nkhosa za pabusa pake.

Lowani ku zipata zake ndi chiyamiko
    ndi ku mabwalo ake ndi matamando;
    muyamikeni ndi kutamanda dzina lake.
Pakuti Yehova ndi wabwino ndipo chikondi chake ndi chamuyaya;
    kukhulupirika kwake nʼkokhazikika pa mibado ndi mibado.

Chivumbulutso 3:20-22

20 Taonani ndayima pa khomo ndikugogoda. Ngati wina amva mawu anga natsekula chitseko, Ine ndidzalowamo ndi kudya naye, Ine ndi iyeyo.

21 Amene adzapambana, ndidzamupatsa ufulu wokhala nane pamodzi pa mpando wanga waufumu monga mmene Ine ndinapambana ndi kukhala pansi ndi Atate anga pa mpando wawo waufumu. 22 Amene ali ndi makutu, amve zimene Mzimu akuwuza mipingo.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.