Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
99 Yehova akulamulira,
mitundu ya anthu injenjemere;
Iye wakhala pa mpando wake waufumu, pakati pa akerubi,
dziko lapansi ligwedezeke.
2 Mʼziyoni wamkulu ndi Yehova;
Iye ndi wokwezeka pamwamba pa mitundu yonse ya anthu.
3 Anthu atamande dzina lanu lalikulu ndi loopsa kwambiri,
Iye ndi woyera.
4 Mfumu yamphamvu, iyo imakonda chilungamo
Inu mwakhazikitsa khalidwe losakondera;
mwachita zolungama ndi zoyenera mwa Yakobo.
5 Kwezani Yehova Mulungu wathu
ndipo mulambireni pa mapazi ake;
Iye ndi woyera.
6 Mose ndi Aaroni anali ena mwa ansembe ake,
Samueli anali pamodzi ndi iwo amene anayitana pa dzina lake;
iwo anayitana Yehova
ndipo Iyeyo anawayankha.
7 Iye anayankhula nawo kuchokera mʼchipilala cha mtambo;
iwo anasunga malamulo ake ndi zophunzitsa zomwe anawapatsa.
8 Inu Yehova Mulungu wathu,
munawayankha iwo;
Inu kwa Israeli munali Mulungu wokhululuka,
ngakhale munawalanga pa zochita zawo zoyipa.
9 Kwezani Yehova Mulungu wathu
ndipo mumulambire pa phiri lake loyera,
pakuti Yehova Mulungu wathu ndi woyera.
22 Tsono Eli anakalamba kwambiri. Iye ankamva zonse zimene ana ake aamuna ankachitira Aisraeli onse, ndiponso kuti ankagona ndi akazi pa chipata cha tenti ya msonkhano. 23 Choncho anawafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani mukuchita zinthu zotere? Ine ndikumva kuchokera kwa anthu onse za zoyipa zanuzo. 24 Ayi, ana anga si mbiri yabwino imene ndikumva anthu a Mulungu akufalitsa. 25 Ngati munthu alakwira munthu mnzake, mwina Mulungu adzamupepesera, koma ngati munthu achimwira Yehova adzamupepesera ndani?” Koma ana ake sanamvere kudzudzula kwa abambo awo, pakuti chinali cholinga cha Yehova kuti awaphe.
26 Ndipo mnyamata Samueli anapitirira kukula mu msinkhu, ndipo ankapeza kuyanja pamaso pa Yehova ndi anthu.
Uneneri Wotsutsa Banja la Eli
27 Tsiku lina munthu wa Mulungu anabwera kwa Eli ndipo anamuwuza kuti, “Yehova akuti, ‘Kodi Ine sindinadziwulule ndekha kwa banja la kholo lako pamene iwo anali akapolo a Farao ku Igupto? 28 Ndipo ndinamusankha pakati pa mafuko a Israeli kuti akhale wansembe wanga ndi kuti azipita pa guwa langa la nsembe, kufukiza Lubani ndi kuvala efodi pamaso panga. Ndinapatsa banja la abambo ako gawo la nsembe zonse zopsereza zimene Aisraeli amapereka. 29 Nʼchifukwa chiyani ukunyoza nsembe ndi zopereka zanga zimene ndinalamula? Nʼchifukwa chiyani ukupereka ulemu kwa ana ako kuposa Ine podzinenepetsa nokha ndi zopereka zabwino kwambiri za nsembe zimene Aisraeli amapereka?’ ”
30 “Paja Ine Yehova Mulungu wa Israeli ‘Ndinalonjeza kuti anthu a pa banja lako ndi a pa banja la abambo ako azidzanditumikira nthawi zonse.’ Koma tsopano ndikuti, ‘Zonsezi zithe!’ Tsopano anthu amene amandilemekeza Inenso ndidzawalemekeza koma iwo amene amandinyoza Ine ndidzawanyoza. 31 Nthawi ikubwera imene ndidzachotsa anyamata ako ndi anyamata a pa banja la abambo ako, kotero kuti sipadzakhala munthu wokalamba pa banja lako. 32 Pa mavuto ako udzayangʼana ndi maso ansanje zabwino zimene ndidzachitira Aisraeli ena. Mʼbanja lako simudzapezeka munthu wokalamba. 33 Komabe pa banja lako mmodzi yekha ndidzamuleka wosamuchotsa kuti azidzanditumikira. Iyeyu azidzakuliritsa ndi kukumvetsa chisoni. Koma ena onse pa banja lako adzafa akanali aangʼono.”
34 “ ‘Ndipo chimene chidzachitike kwa ana ako awiriwa, Hofini ndi Finehasi, chidzakhala chizindikiro kwa iwe. Onse awiri adzafa pa tsiku limodzi. 35 Pambuyo pake ndidzasankha wansembe wokhulupirika, amene adzachita zimene zili mu mtima ndi mʼmaganizo mwanga. Ndidzakhazikitsa banja lako kolimba ndipo adzatumikira pamaso pa wodzozedwa wanga nthawi zonse. 36 Ndipo aliyense wotsala wa banja lako adzabwera ndi kugwada pamaso pake kupempha ndalama kapena chakudya.’ Adzati, ‘Chonde ndiloleni kuti ndizithandizako pa ntchito iliyonse ya unsembe kuti ndipeze chakudya.’ ”
Yesu Achiritsa Munthu pa Sabata
5 Patapita nthawi Yesu anakwera kupita ku Yerusalemu ku phwando la Ayuda. 2 Ndipo ku Yerusalemuko pafupi ndi chipata cha Nkhosa kuli dziwe limene mʼChihebri limatchedwa Betisaida ndipo ndi lozunguliridwa ndi makumbi asanu. 3 Mʼmenemo munkagonamo gulu lalikulu la anthu odwala, osaona, olumala ndi ofa ziwalo. 4 Pakuti nthawi zina mngelo wa Ambuye ankatsikira mʼdziwemo nʼkuvundula madziwo. Woyamba kulowamo madzi atavundulidwa, ankachira ngakhale akhale ndi nthenda yanji. 5 Mmodzi wa amene anali pamenepo anali atadwala zaka 38. 6 Yesu atamuona ali chigonere, nadziwa kuti anakhala chotero kwa nthawi yayitali, anamufunsa iye kuti, “Kodi ukufuna kuchira?”
7 Wodwalayo anayankha kuti, “Ambuye, ndilibe wina aliyense woti angandithandize kulowa mʼdziwe pamene madzi avundulidwa. Pamene ndikuyesera kuti ndilowemo, wina amalowamo ine ndisanalowemo.”
8 Ndipo Yesu anati kwa iye, “Imirira! Nyamula mphasa yako yamba kuyenda.” 9 Nthawi yomweyo munthuyo anachiritsidwa. Iye ananyamula mphasa yake nayamba kuyenda.
Tsiku limene izi zinachitika linali la Sabata. 10 Ndipo Ayuda anati kwa munthu amene anachiritsidwayo, “Lero ndi la Sabata; lamulo silikulola iwe kunyamula mphasa yako.”
11 Koma iye anayankha kuti, “Munthu amene wandichiritsa anati kwa ine, ‘Nyamula mphasa yako yamba kuyenda.’ ”
12 Pamenepo anamufunsa iye kuti, “Kodi munthu ameneyo ndani amene wakuwuza kuti, ‘Nyamula mphasa yako ndipo yenda?’ ”
13 Munthu amene anachiritsidwayo sanadziwe kuti anali ndani, pakuti Yesu anangolowera mʼgulu la anthu ndi kupita.
14 Patapita nthawi Yesu anamupeza ku Nyumba ya Mulungu ndipo anati kwa iye, “Taona uli bwino tsopano. Usakachimwenso kuti choyipa choposa ichi chingakugwere.” 15 Munthu uja anachoka ndi kukawawuza Ayuda kuti anali Yesu amene anamuchiritsa iye.
Yesu Adziwulula kuti ndi Mwana wa Mulungu
16 Ndipo popeza Yesu amachita zinthu izi tsiku la Sabata, Ayuda anayamba kumulondalonda. 17 Yesu anawawuza kuti, “Atate anga amagwira ntchito nthawi zonse mpaka lero lino, ndipo Inenso ndili pa ntchito.” 18 Chifukwa cha ichi Ayuda anawirikiza kufuna kumupha; osati chifukwa chakuswa Sabata kokha komanso chifukwa ankanena kuti Mulungu ndi Atate ake, nadziyesa Iye wofanana ndi Mulungu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.