Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Genesis 32:22-31

Yakobo Alimbana ndi Mulungu

22 Usiku umenewo Yakobo anauka natenga akazi ake awiri, antchito ake awiri ndi ana ake aamuna khumi ndi mmodzi nawoloka pa dooko la mtsinje wa Yaboki. 23 Atatha kuwawolotsa pa mtsinjewo anawolotsanso katundu wake yense. 24 Tsono Yakobo anatsala yekha. Tsono munthu wina anadzalimbana naye mpaka mʼmbandakucha. 25 Pamene munthuyo anaona kuti sangathe kumugonjetsa, anakhudza nyungʼunyu ya pa ntchafu ya Yakobo ndipo inaguluka polimbanapo. 26 Kenaka munthuyo anati, “Ndisiye ndizipita, popeza kunja kukucha.”

Koma Yakobo anayankha, “Sindikulolani kupita pokhapokha mutandidalitsa.”

27 Munthu uja anamufunsa Yakobo kuti, “Kodi dzina lako ndiwe yani?”

Iye anayankha, “Ndine Yakobo.”

28 Pamenepo munthuyo anati, “Dzina lako silidzakhalanso Yakobo koma Israeli, chifukwa walimbana ndi Mulungu ndi anthu ndipo wapambana.”

29 Yakobo anati, “Chonde, uzeni dzina lanu.”

Koma munthuyo anati, “Chifukwa chiyani ukundifunsa dzina?” Kenaka anamudalitsa pomwepo.

30 Choncho Yakobo anawatcha malowo Penueli, popeza anati, “Ndinaonana ndi Mulungu maso ndi maso koma sindinafe.”

31 Dzuwa linamutulukira Yakobo pamene amachoka pa Penueli. Tsono ankayenda chotsimphina chifukwa cha nyungʼunyu yake ija.

Masalimo 17:1-7

Pemphero la Davide.

17 Imvani Inu Yehova pempho langa lachilungamo;
    mverani kulira kwanga.
Tcherani khutu kuti mumve pemphero langa
    popeza silikuchokera pakamwa pachinyengo.
Kusalakwa kwanga kuchokera kwa inu;
    maso anu aone chimene ndi cholungama.

Ngakhale Inu mutafufuza mtima wanga ndi kundisanthula usiku,
    ngakhale mutandiyesa, simudzapeza kanthu;
    Ine ndatsimikiza kuti pakamwa panga sipadzachimwa.
Kunena za ntchito za anthu,
    monga mwa mawu a pakamwa panu,
Ine ndadzisunga ndekha
    posatsata njira zachiwawa.
Mayendedwe anga akhazikika pa njira zanu;
    mapazi anga sanaterereke.

Ine ndikuyitana Inu, Mulungu wanga, pakuti mudzandiyankha;
    tcherani khutu lanu kwa ine ndipo mumve pemphero langa.
Onetsani kudabwitsa kwa chikondi chanu chachikulu,
    Inu amene mumapulumutsa ndi dzanja lanu lamanja
    iwo amene amathawira kwa inu kuchoka kwa adani awo.

Masalimo 17:15

15 Ndipo ine mʼchilungamo ndidzaona nkhope yanu;
    pamene ndidzadzuka, ndidzakondwera kwambiri poonana nanu.

Aroma 9:1-5

Chisankho Chopambana cha Mulungu

Ine ndikunena zoona mwa Khristu. Sindikunama ndipo chikumbumtima changa kudzera mwa Mzimu Woyera chikundichitira umboni. Ndili ndi chisoni chachikulu ndipo ndikumva kupwetekeka kosalekeza mu mtima mwanga. Pakuti ndikanafuna ine mwini nditatembereredwa ndi kuchotsedwa mwa Khristu chifukwa cha abale anga, amene ndi a mtundu wanga, anthu Aisraeli. Iwo anasankhidwa kukhala ana. Mulungu anawapatsa ulemerero, anachita nawo mapangano, kuwapatsa Malamulo, Nyumba yopembedzeramo ndi malonjezano ake. Awo ndi makolo athu. Kuchokera kwa iwo mʼthupi ndi kumene kunachokera makolo a Khristu Yesu amene ndi Mulungu wolamulira zinthu zonse, alemekezeke mpaka muyaya! Ameni.

Mateyu 14:13-21

Yesu Adyetsa Anthu 5,000

13 Yesu atamva zimene zinachitika, anachoka pa bwato mwachinsinsi kupita kumalo a yekha. Magulu a anthu atamva izi anamutsatira Iye poyenda pansi kuchokera ku mizinda. 14 Yesu atafika ku mtunda, ndi kuona gulu lalikulu la anthu, Iye anamva nawo chifundo ndipo anachiritsa odwala awo.

15 Kutayamba mdima, ophunzira anabwera kwa Iye nati, “Kuno ndi kutchire ndipo kwayamba kale kuda. Awuzeni anthu azipita kuti afike ku midzi ndi kukadzigulira zakudya.”

16 Yesu anawayankha kuti, “Sikofunika kuti azipita. Inuyo muwapatse kanthu kuti adye.”

17 Iwo anayankha kuti, “Tili ndi malofu asanu okha a buledi ndi nsomba ziwiri.”

18 Koma Iye anati, “Bweretsani kwa Ine.” 19 Analamula anthu kuti akhale pansi pa udzu ndipo anatenga buledi musanu ndi nsomba ziwiri nayangʼana kumwamba, nayamika nagawa bulediyo. Kenaka anapereka bulediyo kwa ophunzira ake ndipo ophunzirawo anagawira anthu. 20 Onse anadya nakhuta ndipo ophunzira anatola zotsalira ndi kudzaza madengu khumi ndi awiri. 21 Chiwerengero cha amene anadya kupatulako amayi ndi ana chinali pafupifupi amuna 5,000.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.