Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Salimo la Davide.
143 Yehova imvani pemphero langa,
mvetserani kulira kwanga kopempha chifundo;
mwa kukhulupirika kwanu ndi chilungamo chanu
bwerani kudzandithandiza.
2 Musazenge mlandu mtumiki wanu,
pakuti palibe munthu wamoyo amene ndi wolungama pamaso panu.
3 Mdani akundithamangitsa,
iye wandipondereza pansi;
wachititsa kuti ndikhale mu mdima
ngati munthu amene anafa kale.
4 Choncho mzimu wanga ukufowoka mʼkati mwanga;
mʼkati mwanga, mtima wanga uli ndi nkhawa.
5 Ndimakumbukira masiku amakedzana;
ndimalingalira za ntchito yanu yonse,
ndimaganizira zimene manja anu anachita.
6 Ndatambalitsa manja anga kwa Inu;
moyo wanga uli ndi ludzu lofuna Inu monga nthaka yowuma.
Sela
7 Yehova ndiyankheni msanga;
mzimu wanga ukufowoka.
Musandibisire nkhope yanu,
mwina ndidzakhala ngati iwo amene atsikira ku dzenje.
8 Lolani kuti mmawa ubweretse mawu achikondi chanu chosasinthika,
pakuti ine ndimadalira Inu.
Mundisonyeze njira yoti ndiyendemo,
pakuti kwa Inu nditukulira moyo wanga.
9 Pulumutseni kwa adani anga, Inu Yehova,
pakuti ndimabisala mwa Inu.
10 Phunzitseni kuchita chifuniro chanu,
popeza ndinu Mulungu wanga;
Mzimu wanu wabwino unditsogolere
pa njira yanu yosalala.
11 Sungani moyo wanga Inu Yehova chifukwa cha dzina lanu;
mwa chilungamo chanu tulutseni mʼmasautso anga.
12 Mwa chikondi chanu chosasinthika khalitsani chete adani anga;
wonongani adani anga,
pakuti ndine mtumiki wanu.
17 Tsiku lina mwana wake wa mkazi wamasiye uja, mwini nyumbayo, anadwala. Matenda ananka nakulirakulirabe, ndipo kenaka analeka kupuma. 18 Mayiyo anati kwa Eliya, “Kodi ndakulakwirani chiyani, inu munthu wa Mulungu? Kodi munabwera kuno kudzandikumbutsa tchimo langa ndi kudzandiphera mwana wanga?”
19 Eliya anayankha kuti, “Patseni mwana wanuyo.” Iye anatenga mwanayo mʼmanja mwa mayiyo napita naye mʼchipinda chapamwamba, kumene Eliyayo amagona, namugoneka pa bedi lake. 20 Kenaka Eliya anafuwula kwa Yehova nati, “Inu Yehova Mulungu wanga, kodi mwabweretsanso choyipa chotere pa mkazi wamasiye amene ine ndikukhala naye, pakuchititsa kuti mwana wake afe?” 21 Pamenepo Eliya anakumbatira mwanayo katatu ndi kufuwula kwa Yehova kuti, “Inu Yehova Mulungu wanga, mubwezereni mwanayu moyo wake!”
22 Yehova anamva kufuwula kwa Eliya, ndipo moyo wa mwanayo unabwerera mwa iye ndipo anatsitsimuka. 23 Eliya ananyamula mwanayo natsika naye kuchoka mʼchipinda chapamwamba chija nalowa naye mʼnyumba. Anamupereka kwa amayi ake ndipo anati, “Taonani, mwana wanu ali ndi moyo!”
24 Pamenepo mayiyo anati kwa Eliya, “Tsopano ndadziwa kuti ndinu munthu wa Mulungu ndipo mawu a Yehova amene mumayankhula ndi owona.”
Paulo Aukitsa Utiko ku Trowa
7 Pa tsiku loyamba la Sabata, tinasonkhana kuti tidye mgonero. Paulo analalikira kwa anthu chifukwa anaganiza zoti achoke tsiku linalo, ndipo analalika mpaka pakati pa usiku. 8 Munali nyale zambiri mʼchipinda chammwamba mʼmene tinasonkhanamo. 9 Pa chipinda chachitatu chammwamba cha nyumbayo, pa zenera, panakhala mnyamata wina dzina lake Utiko, amene ankasinza pomwe Paulo amayankhulabe. Atagona tulo, iye anagwa pansi kuchokera pa chipinda chammwamba ndipo anamutola atafa. 10 Paulo anatsika, nadziponya pa mnyamatayo, namukumbatira. Paulo anati, “Musadandaule, ali moyo!” 11 Kenaka Paulo anakweranso, mʼchipinda muja nanyema buledi nadya. Atayankhula mpaka kucha, anachoka. 12 Anthu anatenga mnyamatayo kupita kwawo ali moyo ndipo anatonthozedwa mtima kwambiri.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.