Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 133

Salimo la Davide. Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

133 Onani, nʼkokoma ndi kokondweretsa ndithu
    pamene abale akhala pamodzi mwachiyanjano!
Zili ngati mafuta amtengowapatali othiridwa pa mutu,
    otsikira ku ndevu,
ku ndevu za Aaroni,
    oyenderera mpaka mʼkhosi mwa mkanjo wake.
Zili ngati mame a ku Heremoni
    otsikira pa Phiri la Ziyoni.
Pakuti pamenepo Yehova amaperekapo dalitso,
    ndiwo moyo wamuyaya.

Levitiko 19:9-18

“ ‘Pamene mukolola zinthu mʼmunda mwanu musakolole mpaka mʼmphepete mwa munda, ndipo musatole khunkha lake. 10 Musakolole mphesa zonse mʼmunda wanu wa mpesa kapena kutola mphesa zakugwa mʼmundamo. Zimenezi muzisiyire anthu osauka ndi alendo. Ine ndine Yehova Mulungu wako.

11 “ ‘Musabe.

“ ‘Musamanamizane.

“ ‘Musachitirane zinthu mwachinyengo.

12 “ ‘Musalumbire mʼdzina langa monyenga popeza kutero ndi kuyipitsa dzina la Mulungu wanu. Ine ndine Yehova.

13 “ ‘Musapsinje mnzanu kapena kumulanda zinthu zake.

“ ‘Musasunge malipiro a munthu wantchito usiku wonse mpaka mmawa.

14 “ ‘Musatemberere wosamva kapena kuyikira munthu wosaona chinthu choti apunthwe nacho patsogolo pake, koma muziopa Mulungu wanu. Ine ndine Yehova.

15 “ ‘Musamaweruze mopanda chilungamo. Musachite tsankho pakati pa osauka ndi olemera, koma muweruze mlandu wa mnzanu mwachilungamo.

16 “ ‘Musamapite uku ndi uku kunena bodza pakati pa anthu anu.

“ ‘Musachite kanthu kalikonse kamene kangadzetse imfa kwa mnzanu. Ine ndine Yehova.

17 “ ‘Musamude mʼbale wanu mu mtima mwanu. Koma mudzudzuleni mnzanu moona mtima kuti musakhale wolakwa.

18 “ ‘Musamubwezere mnzanu choyipa kapena kumusungira kanthu kunkhosi, koma konda mnansi wako monga iwe mwini. Ine ndine Yehova.

Luka 10:25-28

Fanizo la Msamariya Wachifundo

25 Nthawi ina katswiri wa malamulo anayimirira kuti ayese Yesu. Iye anati, “Aphunzitsi, ndichite chiyani kuti ndikhale ndi moyo wosatha?”

26 Yesu anayankha kuti, “Mwalembedwa chiyani mʼMalamulo, ndipo iwe umawerenga zotani?”

27 Iye anayankha kuti, “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse ndi nzeru zako zonse, ndi kukonda mnansi wako monga iwe mwini.”

28 Yesu anayankha kuti, “Iwe wayankha bwino, chita zimenezi ndipo udzakhala ndi moyo.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.