Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 119:49-56

Zayini

49 Kumbukirani mawu anu kwa mtumiki wanu,
    popeza mwandipatsa chiyembekezo.
50 Chitonthozo changa pa masautso anga ndi ichi:
    lonjezo lanu limasunga moyo wanga.
51 Odzikuza amandinyoza popanda chowaletsa,
    koma sindichoka pa malamulo anu.
52 Ndimakumbukira malamulo anu Yehova akalekale,
    ndipo mwa iwo ndimapeza chitonthozo.
53 Ndayipidwa kwambiri chifukwa cha oyipa
    amene ataya malamulo anu.
54 Zophunzitsa zanu ndi mitu ya nyimbo yanga
    kulikonse kumene ndigonako.
55 Usiku ndimakumbukira dzina lanu Yehova,
    ndipo ndidzasunga malamulo anu.
56 Ichi ndicho ndakhala ndikuchita:
    ndimasunga malangizo anu.

Deuteronomo 5:22-6:3

22 Awa ndi malamulo amene Yehova anayankhula ndi mawu okweza kwa gulu lanu lonse pa phiri paja mʼmoto, mtambo ndi mdima woopsa, sanawonjezerepo kanthu. Ndipo anawalemba pa mapale awiri amiyala ndi kundipatsa.

23 Mutamva mawu kuchokera mu mdimawo, phiri lili moto lawilawi, atsogoleri onse a mafuko anu ndi akuluakulu anu anabwera kwa ine. 24 Ndipo munati, “Yehova Mulungu wathu wationetsa ulemerero ndi ukulu wake, ndipo tamva mawu ake kuchokera mʼmoto. Lero taona kuti munthu akhoza kukhala ndi moyo ngakhale Mulungu atayankhula naye. 25 Koma tsopano tife chifukwa chiyani? Moto waukuluwu utinyeketsa, ndipo tifa tikapitirirabe kumva mawu a Yehova Mulungu wathu. 26 Pakuti ndi munthu uti wolengedwa amene anamvapo mawu a Mulungu wamoyo akuyankhula kuchokera mʼmoto, monga tachitiramu, nakhala ndi moyo? 27 Pita pafupi kuti ukamvetsere zonse zimene Yehova Mulungu wathu akunena. Kenaka udzatiwuze chilichonse chimene Yehova Mulungu wathu akunena ndipo tidzamvera ndi kuchita.”

28 Yehova anakumvani pamene munkayankhula kwa ine ndipo Yehova anati kwa ine, “Ndamva zimene anthuwa anena kwa iwe. Chilichonse chimene anena ndi chabwino. 29 Zikanakhala bwino akanakhala ndi mtima wondiopa ndi kusunga malamulo anga nthawi zonse kuti zinthu ziziwayendera bwino, iwowo pamodzi ndi ana awo kwamuyaya.

30 “Pita uwawuze kuti abwerere ku matenti awo. 31 Koma iwe ukhale kuno ndi ine kuti ndikupatse malamulo, malangizo ndi ziphunzitso zimene azitsatira mʼdziko limene ndiwapatse kuti alitenge.”

32 Choncho samalirani kuchita zimene Yehova Mulungu wanu akukulamulirani inu, musapatukire kudzanja lamanja kapena lamanzere. 33 Muyende mʼnjira yonse imene Yehova Mulungu wanu wakulamulirani kuti mukhale ndi moyo ndi kupambana, ndi kuti masiku anu achuluke mʼdziko limene mudzatengelo.

Konda Yehova Mulungu Wako

Awa ndi malamulo, malangizo ndi ziphunzitso zimene Yehova Mulungu wanu anandilamula kuti ndikuphunzitseni kuti mukawatsatire mʼdziko limene mukuwolokera Yorodani kuti mukalitenge, kuti inuyo, ana anu, ndi zidzukulu zanu mʼtsogolomo mudzaope Yehova Mulungu wanu moyo wanu wonse posunga malangizo ndi malamulo ake onse amene ndinakupatsani inu kuti musangalale ndi moyo wautali. Mvera Israeli ndipo usamalitse kuchita malamulowa kuti zinthu zikuyendere bwino mʼdziko ndi kuti muchuluke kwambiri mʼdziko loyenda mkaka ndi uchi monga momwe Yehova Mulungu wa makolo anu anakulonjezerani.

2 Akorinto 5:17-21

17 Nʼchifukwa chake, ngati munthu aliyense ali mwa Khristu, ndi wolengedwa kwatsopano; zinthu zakale zapita taonani, zakhala zatsopano. 18 Zonsezi zichokera kwa Mulungu amene anatiyanjanitsa ndi Iye mwini kudzera mwa Khristu ndipo anatipatsa ife utumiki wa chiyanjanitso. 19 Mulungu ankayanjanitsa dziko lapansi kwa Iye mwini kudzera mwa Khristu, osawerengera anthu monga mwa zochimwa zawo. Ndipo watisungitsa ife uthenga uwu wa chiyanjanitso. 20 Choncho ife ndi akazembe a Khristu, monga ngati Mulungu akudandaulira anthu kudzera mwa ife. Ife tikukupemphani inu mʼmalo mwa Khristu kuti, yanjanitsidwani ndi Mulungu. 21 Chifukwa cha ife, Mulungu anasandutsa wopanda tchimoyo kukhala tchimo, kuti mwa Iye ife tikakhale chilungamo cha Mulungu.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.