Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Salimo la Solomoni.
72 Patsani mwana wa mfumu nzeru zanu zoweruzira mwa chilungamo,
Inu Mulungu mupatseni mwana wa mfumu chilungamo chanu.
2 Iye adzaweruza anthu anu mwachilungamo,
anthu anu ozunzika mosakondera.
3 Mapiri adzabweretsa chuma kwa anthu anu,
timapiri tidzabweretsa zipatso zachilungamo.
4 Iye adzateteza ozunzika pakati pa anthu
ndi kupulumutsa ana a anthu osowa;
adzaphwanya ozunza anzawo.
5 Adzakhala ndi moyo pa mibado yonse,
nthawi zonse pamene dzuwa ndi mwezi zikuwala.
6 Iye adzakhala kugwa kwa mvula pa minda yolimidwa
ngati mivumbi yothirira dziko lapansi.
7 Mʼmasiku a munthu wolungama adzakhazikika;
chuma chidzachuluka mpaka mwezi utaleka kuwala.
8 Iye adzalamulira kuchokera ku nyanja ina mpaka ku nyanja ina
ndiponso kuchokera ku mtsinje mpaka ku malekezero a dziko lapansi.
9 Mafuko a mʼchipululu adzawerama pamaso pake
ndipo adani ake adzanyambita fumbi.
10 Mafumu a ku Tarisisi ndi a ku zilumba zakutali
adzabweretsa mitulo kwa iye,
mafumu a ku Seba ndi Seba
adzapereka mphatso kwa iyeyo.
11 Mafumu onse adzamuweramira
ndipo mitundu yonse idzamutumikira.
12 Pakuti iye adzawombola wosowa amene akulira,
wozunzika amene alibe wina womuthandiza.
13 Iye adzachitira chifundo anthu ofowoka ndi anthu osowa
ndi kupulumutsa osowa ku imfa.
14 Iye adzalanditsa iwo ku mazunzo ndi chiwawa
pakuti magazi awo ndi amtengo wapatali pamaso pake.
15 Iye akhale ndi moyo wautali;
golide ochokera ku Seba apatsidwe kwa iye.
Anthu amupempherere nthawi zonse
ndi kumudalitsa tsiku lonse.
16 Mulole kuti tirigu achuluke mʼdziko lonse;
pamwamba pa mapiri pakhale tirigu.
Zipatso zake zichuluke ngati za ku Lebanoni;
zichuluke ngati udzu wakuthengo
17 Dzina lake likhazikike kwamuyaya,
lipitirire kukhala monga momwe limakhalira dzuwa.
Mitundu yonse idzadalitsika kudzera mwa iye
ndipo iwo adzamutcha iye wodala.
18 Matamando akhale kwa Yehova Mulungu, Mulungu wa Israeli
amene Iye yekha amachita ntchito zodabwitsa.
19 Matamando akhale ku dzina lake laulemerero kwamuyaya
dziko lonse lapansi lidzaze ndi ulemerero wake.
Ameni ndi Ameni.
20 Uku ndiko kumaliza kwa mapemphero a Davide mwana wa Yese.
Mfumu Yayikazi ya ku Seba Ibwera Kudzacheza ndi Solomoni
10 Mfumu yayikazi ya ku Seba itamva za kutchuka kwa Solomoni ndi za ubale wake ndi Yehova, inabwera kudzamuyesa ndi mafunso okhwima. 2 Inafika mu Yerusalemu ndi gulu lalikulu la ngamira zonyamula zokometsera zakudya, golide wambiri ndi miyala yokongola. Inafika kwa Solomoni ndipo inayankhula naye zonse zimene zinali mu mtima mwake. 3 Solomoni anayankha mafunso ake onse ndipo panalibe kanthu kalikonse kovuta komwe sanathe kufotokozera mfumu yayikaziyo. 4 Mfumu yayikazi ya ku Seba itaona nzeru zonse za Solomoni ndiponso nyumba yaufumu imene anamanga, 5 chakudya cha pa tebulo pake, moyo wa antchito ake ndi zovala zawo, atumiki opereka zakumwa, ndiponso nsembe zopsereza zimene ankapereka ku Nyumba ya Yehova, inathedwa nzeru.
6 Iyo inati kwa mfumu, “Mbiri imene ndinamva ndili ku dziko kwathu ya zomwe munachita komanso nzeru zanu ndi yoona. 7 Koma sindinakhulupirire zinthu zimenezo mpaka nditafika ndi kuona ndi maso anga. Kunena zoona sanandiwuze ngakhale theka lomwe, pakuti nzeru ndi chuma zimene muli nazo zaposa zimene ndinamva. 8 Ngodala anthu anu! Ngodala atumiki anu amene amayimirira pamaso panu nthawi zonse ndi kumamva nzeru zanu! 9 Atamandike Yehova Mulungu wanu amene wakondwera nanu nakukhazikani pa mpando waufumu wa Israeli. Chifukwa cha chikondi chake chamuyaya pa Israeli, wayika inu kuti mukhale mfumu kuti mulamulire moyenera ndi mwachilungamo.”
10 Ndipo mfumu yayikaziyo inapatsa Solomoni golide wolemera makilogalamu 4,000, zokometsera zakudya zambirimbiri, ndiponso miyala yokongola. Sikunabwerenso zokometsera zakudya ngati zomwe mfumu yayikazi ya ku Seba inapatsa Mfumu Solomoni.
11 (Ndiponso sitima zapamadzi za Hiramu zinabweretsa golide wochokera ku Ofiri. Ndipo kuchokera kumeneko kunabweranso mitengo yambiri ya alimugi ndi miyala yokongola. 12 Mfumu inagwiritsa ntchito mitengo ya alimugi ngati yochirikizira Nyumba ya Yehova ndi nyumba yaufumu, ndipo anapangiranso azeze ndi apangwe a anthu oyimba. Mitengo yotere sinayitanitsidweponso kapena kuoneka mpaka lero lino).
13 Mfumu Solomoni inapereka kwa mfumu yayikazi ya ku Seba zonse zimene inazifuna ndi kuzipempha, osawerengera mphatso zaufumu zimene anali atamupatsa. Choncho inabwerera ku dziko la kwawo pamodzi ndi atumiki ake.
Paulo Apempherera Aefeso
14 Nʼchifukwa chake ine ndikugwada pamaso pa Atate, 15 amene banja lililonse kumwamba ndi pa dziko lapansi limatchulidwa ndi dzina lawo. 16 Ndikupemphera kuti kuchokera mʼchuma cha ulemerero wake alimbikitse moyo wanu wa mʼkati ndi mphamvu za Mzimu wake, 17 kuti Khristu akhazikike mʼmitima mwanu mwachikhulupiriro. Ndipo ndikukupemphererani kuti muzikike ndi kukhazikika mʼchikondi 18 kuti mukhale ndi mphamvu, kuti pamodzi ndi anthu oyera mtima onse muthe kuzindikira kupingasa, kutalika ndi kukwera komanso kuzama kwake kwa chikondi cha Khristu. 19 Ndikukupemphererani kuti mudziwe chikondi chija cha Khristu chopitirira nzeru za anthu, kuti mudzazidwe kwathunthu ndi moyo wa Mulungu mwini.
20 Tsopano kwa Iye amene angathe kuchita zochuluka kuposa zimene tingapemphe, kapena kuganiza molingana ndi mphamvu zake zimene zikugwira ntchito mwa ife, 21 Iyeyo akhale ndi ulemu mu mpingo ndi mwa Khristu Yesu pa mibado yonse mpaka muyaya. Ameni.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.